민수기 7 – KLB & CCL

Korean Living Bible

민수기 7:1-89

지도자들이 바친 예물

1모세는 성막을 다 세우고 나서 성막과 그 모든 기구와 단과 그 모든 기구에 기 름을 발라 거룩하게 하였다.

2그리고 인구 조사를 맡았던 각 지파의 지도자들이 그 날 여호와께 예물을 드렸다.

3그들은 지도자 두 명에 덮개 있는 수레 한 대씩, 지도자 한 명에 소 한 마리씩 모두 수레 여섯 대와 소 열두 마리를 가져와 성막 앞에서 여호와께 드렸다.

4그때 여호와께서 모세에게

5“너는 그 예물을 받아 레위인에게 주어 그들이 성막 일을 할 때 각자 필요한 대로 사용하게 하라” 하고 말씀하셨다.

6그래서 모세는 그 수레와 소를 받아 레위인에게 주었는데

7게르손 자손에게 수레 두 대와 소 네 마리를 주었고,

8므라리 자손에게 수레 네 대와 소 여덟 마리를 주었다. 그리고 그들은 모두 아론의 아들인 제사장 이다말의 지시를 받게 하였다.

9그러나 고핫 자손들은 거룩한 물건을 어깨로 메어 운반하는 일을 맡았기 때문에 모세는 그들에게 수레나 소를 주지 않았다.

10그리고 제단에 기름을 바르던 날에 지도자들은 제단 봉헌 예물을 가져왔다.

11그때 여호와께서 모세에게 “너는 그 지도자들에게 매일 한 사람씩 자기가 가져온 제단 봉헌 예물을 바치게 하라” 하고 말씀하셨다.

12-83그래서 이스라엘의 그 열두 지도자들 은 각자 지정된 날에 모두 똑같은 예물을 드렸는데 그들이 드린 예물은 7:12-83 히 ‘130세겔’1.5킬로그램의 은쟁반 하나, 7:12-83 히 ‘70세겔’798그램의 은대접 하나 (이 두 그릇에는 고운 밀가루에 기름 섞은 소제물을 가득 담았음); 향을 가득 담은 7:12-83 히 ‘10세겔’114그램의 금접시 하나; 번제물로 수송아지 한 마리, 숫양 한 마리, 일 년 된 어린 숫양 한 마리; 속죄제물로 숫염소 한 마리; 화목제물로 소 두 마리, 숫양 다섯 마리, 숫염소 다섯 마리, 일 년 된 어린 숫양 다섯 마리였다. 그리고 각 지파의 이 지도자들이 예물을 드린 날은 다음과 같다:

1일에는 유다 지파에서암미나답의 아들 나손이 드렸으며,2일에는 잇사갈 지파에서수알의 아들 느다넬이,3일에는 스불론 지파에서헬론의 아들 엘리압이,4일에는 르우벤 지파에서스데울의 아들 엘리술이,5일에는 시므온 지파에서수리삿대의 아들 슬루미엘이,6일에는 갓 지파에서드우엘의 아들 엘리아삽이,7일에는 에브라임 지파에서암미훗의 아들 엘리사마가,8일에는 므낫세 지파에서브다술의 아들 가말리엘이,9일에는 베냐민 지파에서기드오니의 아들 아비단이,10일에는 단 지파에서암미삿대의 아들 아히에셀이,11일에는 아셀 지파에서오그란의 아들 바기엘이,12일에는 납달리 지파에서에난의 아들 아히라가 드렸다.

84-88이와 같이 이스라엘 지도자들이 제단 봉헌 때 드린 전체 예물은 1.5킬로그램의 은쟁반 12개, 798그램의 은대접 12개 (이 두 은그릇의 전체 중량은 7:84-88 히 ‘2,400세겔’약 27.4킬로그램); 향을 가득 담은 114그램의 금접시 12개 (전체 중량 7:84-88 히 ‘120세겔’약 1.4킬로그램); 번제물로 수송아지 12마리, 숫양 12마리, 일 년 된 어린 숫양 12마리, 이것들과 함께 드린 소제물; 속죄제물로 숫염소 12마리; 화목제물로 수소 24마리, 숫양 60마리, 숫염소 60마리, 일 년 된 어린 숫양 60마리였다.

89모세가 여호와와 말하려고 성막에 들어갔을 때 그는 여호와께서 법궤 뚜껑인 속죄소 위의 두 그룹 천사 사이에서 자기에게 말씀하시는 소리를 들었다.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 7:1-89

Zopereka Popatula Chihema

1Mose atamaliza kuyimika chihema chija, anachidzoza mafuta ndi kuchipatula pamodzi ndi ziwiya zake zonse. Anadzozanso guwa lansembe ndi kulipatula pamodzi ndi ziwiya zake zonse. 2Kenaka atsogoleri a Aisraeli, akuluakulu a mabanja omwe ankayangʼanira mafuko a anthu omwe anawawerenga aja, anachita chopereka. 3Anabweretsa zopereka zawo pamaso pa Yehova: ngolo zophimbidwa zisanu ndi imodzi ndiponso ngʼombe zothena khumi ndi ziwiri. Mtsogoleri mmodzi ngʼombe yothena imodzi ndipo atsogoleri awiri ngolo imodzi. Izi anazipereka ku chihema.

4Yehova anawuza Mose kuti, 5“Ulandire zimenezi kwa iwo kuti zigwire ntchito ku tenti ya msonkhano. Uzipereke kwa Alevi, aliyense monga mwa ntchito yake.”

6Choncho Mose anatenga ngolo ndi ngʼombe zothenazo nazipereka kwa Alevi. 7Anapereka ngolo ziwiri ndi ngʼombe zothena zinayi kwa Ageresoni monga mwantchito yawo 8ndiponso anapereka ngolo zinayi ndi ngʼombe zothena zisanu ndi zitatu kwa Amerari molingananso ndi ntchito yawo. Onsewa ankawayangʼanira anali Itamara mwana wa Aaroni wansembe. 9Koma Mose sanapereke zimenezi kwa Akohati chifukwa zinthu zawo zopatulika zomwe ankayangʼanira zinali zoti azinyamula pa mapewa awo.

10Guwa la nsembe litadzozedwa, atsogoleri anabweretsa zopereka zawo zopatulira guwa nazipereka paguwapo. 11Pakuti Yehova anawuza Mose kuti, “Tsiku lililonse mtsogoleri mmodzi azibweretsa chopereka chake chopatulira guwa lansembe.”

12Amene anabweretsa chopereka chake tsiku loyamba anali Naasoni mwana wa Aminadabu wa fuko la Yuda.

13Chopereka chake chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi, ndi beseni lasiliva limodzi lowazira, lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo wopatulika ndipo zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta ngati chopereka chachakudya; 14mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; 15mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa wamwamuna mmodzi wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza; 16mbuzi yayimuna imodzi, nsembe ya machimo; 17ndi ngʼombe zothena ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa asanu a chaka chimodzi kuti zikhale za nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Naasoni mwana wa Aminadabu.

18Pa tsiku lachiwiri, Natanieli mwana wa Zuwara, mtsogoleri wa Isakara, anabweretsa chopereka chake.

19Chopereka chomwe anabwera nacho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, molingana ndi muyeso wa ku malo opatulika. Mbale zonse zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka cha chakudya. 20Mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110 yodzaza ndi lubani; 21mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza: 22mbuzi yayimuna imodzi ya nsembe yotetezera machimo; 23ndi ngʼombe ziwiri, nkhosa zazimuna ziwiri, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa asanu a chaka chimodzi, nsembe ya chiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Netanieli mwana wa Zuwara.

24Pa tsiku lachitatu, Eliabu mwana wa Heloni, mtsogoleri wa Azebuloni, anabweretsa chopereka chake.

25Chopereka chake chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, ndi beseni limodzi lasiliva lowazira lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika, mbale zonse zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, chopereka cha chakudya; 26mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; 27mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa wamwamuna mmodzi wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza; 28mbuzi imodzi ya nsembe yopepesera machimo; 29ndi ngʼombe ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Eliabu mwana wa Heloni.

30Tsiku lachinayi linali la Elizuri mwana wa Sedeuri, mtsogoleri wa fuko la Rubeni, anabweretsa chopereka chake.

31Chopereka chake chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika; zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, chopereka chachakudya. 32Mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; 33mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza; 34mbuzi imodzi ya nsembe yopepesera machimo; 35ndi ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna ziwiri, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Elizuri mwana wa Sedeuri.

36Pa tsiku lachisanu Selumieli mwana wa Zurisadai, mtsogoleri wa fuko la Simeoni, anabweretsa chopereka chake.

37Chopereka chake chinali mbale yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka ndi beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika. Zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya; 38mbale yagolide imodzi yolemera 110, yodzaza ndi lubani; 39mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi ndi mwana wankhosa mmodzi wamwamuna wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza; 40mbuzi imodzi ya nsembe yopepesera machimo; 41ngʼombe ziwiri, nkhosa zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Selumieli mwana wa Zurisadai.

42Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi, Eliyasafu mwana wa Deuweli, mtsogoleri wa fuko la Gadi, anabweretsa chopereka chake.

43Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika; zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya; 44mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; 45mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa wamwamuna mmodzi wa chaka chimodzi, chopereka cha nsembe yopsereza: 46mbuzi yayimuna imodzi ya nsembe yopepesera machimo; 47ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Eliyasafu mwana wa Deuweli.

48Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri Elisama mwana wa Amihudi, mtsogoleri wa fuko la Efereimu, anabweretsa chopereka chake.

49Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, ndi beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonsezi monga mwa muyeso wa ku malo opatulika, zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya; 50mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; 51mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi yayimuna ndi mwana wankhosa wamwamuna mmodzi wa chaka chimodzi, nsembe yopsereza; 52mbuzi imodzi ya nsembe yopepesera machimo; 53ngʼombe ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Elisama mwana wa Amihudi.

54Pa tsiku lachisanu ndi chitatu Gamalieli mwana wa Pedazuri, mtsogoleri wa fuko Manase, anabweretsa chopereka chake.

55Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, ndi beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika; zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya; 56mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani, 57mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, nsembe yopsereza; 58mbuzi imodzi ya nsembe yopepesera machimo; 59ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu ndi ana ankhosa a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Gamalieli mwana wa Pedazuri.

60Pa tsiku lachisanu ndi chinayi Abidani mwana wa Gideoni mtsogoleri wa fuko la Benjamini, anabweretsa chopereka chake.

61Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka ndi beseni limodzi lowazira lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika; zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka cha zakudya; 62mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; 63mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi yayimuna ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, nsembe yopsereza; 64mbuzi yayimuna imodzi ya nsembe yopepesera machimo; 65ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu, ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Abidani mwana wa Gideoni.

66Pa tsiku lakhumi Ahiyezeri mwana wa Amisadai, mtsogoleri wa fuko la Dani anabweretsa chopereka chake.

67Chopereka chake chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika, zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya; 68mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; 69mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi yayimuna ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, nsembe yopsereza; 70mbuzi yayimuna imodzi ya nsembe yopepesera machimo; 71ndi ngʼombe ziwiri zazimuna, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu, ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Ahiyezeri mwana wa Amisadai.

72Pa tsiku la khumi ndi chimodzi, Pagieli mwana wa Okirani, mtsogoleri wa fuko la Aseri, anabweretsa chopereka chake.

73Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika; zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya; 74mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; 75mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi yayimuna ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza; 76mbuzi imodzi yayimuna ya nsembe yopepesera machimo; 77ngʼombe ziwiri zazimuna, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu, ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Pagieli mwana wa Okirani.

78Pa tsiku la khumi ndi chimodzi Ahira mwana wa Enani, mtsogoleri wa fuko la Nafutali, anabweretsa chopereka chake.

79Chopereka chakecho chinali mbale imodzi yasiliva yolemera kilogalamu imodzi ndi theka, beseni limodzi lowazira lasiliva lowazira lolemera magalamu 800, zonse monga mwa muyeso wa ku malo opatulika, zonse ziwiri zinali zodzaza ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta monga chopereka chachakudya; 80mbale imodzi yagolide yolemera magalamu 110, yodzaza ndi lubani; 81mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi yayimuna ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, nsembe yopsereza; 82mbuzi yayimuna imodzi ya nsembe yopepesera machimo; 83ngʼombe zazimuna ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu, mbuzi zazimuna zisanu, ndi ana ankhosa aamuna asanu a chaka chimodzi, nsembe yachiyanjano. Ichi chinali chopereka cha Ahira mwana wa Enani.

84Zopereka za atsogoleri a Israeli zopatulira guwa lansembe pamene linadzozedwa zinali izi: mbale khumi ndi ziwiri zasiliva, mabeseni owazira asiliva khumi ndi awiri ndi mbale zagolide khumi ndi ziwiri. 85Mbale iliyonse yasiliva inkalemera kilogalamu imodzi ndi theka, ndipo beseni lililonse lowazira linkalemera magalamu 800. Pamodzi, mbale zonse zasiliva zinkalemera makilogalamu 27 monga mwa muyeso wa ku malo opatulika. 86Mbale khumi ndi ziwiri zagolide zodzaza ndi lubanizo zinkalemera magalamu 110 iliyonse, monga mwa muyeso wa ku malo opatulika. Pamodzi, mbale zagolide zinkalemera kilogalamu imodzi ndi theka. 87Chiwerengero cha nyama zonse za nsembe yopsereza chinali motere: ngʼombe zazimuna khumi ndi ziwiri, nkhosa zazimuna khumi ndi ziwiri ndi ana ankhosa aamuna khumi ndi awiri a chaka chimodzi pamodzi ndi chopereka chachakudya. Mbuzi zazimuna khumi ndi ziwiri zinali za nsembe yopepesera machimo. 88Chiwerengero cha nyama zonse za nsembe yachiyanjano chinali motere: ngʼombe zothena 24, nkhosa zazimuna 60, mbuzi zazimuna 60 ndi ana ankhosa aamuna a chaka chimodzi 60. Zimenezi ndi zimene zinali zopereka zopatulira guwa lansembe litadzozedwa.

89Mose atalowa mu tenti ya msonkhano kukayankhula ndi Yehova, anamva mawu kuchokera pakati pa Akerubi awiri amene anali pamwamba pa chivundikiro cha bokosi la umboni. Ndipo anayankhula naye.