King James Version

Revelation 5

1And I saw in the right hand of him that sat on the throne a book written within and on the backside, sealed with seven seals.

And I saw a strong angel proclaiming with a loud voice, Who is worthy to open the book, and to loose the seals thereof?

And no man in heaven, nor in earth, neither under the earth, was able to open the book, neither to look thereon.

And I wept much, because no man was found worthy to open and to read the book, neither to look thereon.

And one of the elders saith unto me, Weep not: behold, the Lion of the tribe of Judah, the Root of David, hath prevailed to open the book, and to loose the seven seals thereof.

And I beheld, and, lo, in the midst of the throne and of the four beasts, and in the midst of the elders, stood a Lamb as it had been slain, having seven horns and seven eyes, which are the seven Spirits of God sent forth into all the earth.

And he came and took the book out of the right hand of him that sat upon the throne.

And when he had taken the book, the four beasts and four and twenty elders fell down before the Lamb, having every one of them harps, and golden vials full of odours, which are the prayers of saints.

And they sung a new song, saying, Thou art worthy to take the book, and to open the seals thereof: for thou wast slain, and hast redeemed us to God by thy blood out of every kindred, and tongue, and people, and nation;

10 And hast made us unto our God kings and priests: and we shall reign on the earth.

11 And I beheld, and I heard the voice of many angels round about the throne and the beasts and the elders: and the number of them was ten thousand times ten thousand, and thousands of thousands;

12 Saying with a loud voice, Worthy is the Lamb that was slain to receive power, and riches, and wisdom, and strength, and honour, and glory, and blessing.

13 And every creature which is in heaven, and on the earth, and under the earth, and such as are in the sea, and all that are in them, heard I saying, Blessing, and honour, and glory, and power, be unto him that sitteth upon the throne, and unto the Lamb for ever and ever.

14 And the four beasts said, Amen. And the four and twenty elders fell down and worshipped him that liveth for ever and ever.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chivumbulutso 5

Buku la Mwana Wankhosa

1Kenaka ndinaona buku mʼdzanja la wokhala pa mpando waufumu uja. Bukulo linali lolembedwa mbali zonse ndipo linali lomatidwa ndi zomatira zisanu ndi ziwiri. Ndipo ndinaona mngelo wamphamvu akulengeza ndi mawu okweza kuti, “Ndani ali woyenera kumatula zomatira ndi kufutukula bukuli?” Koma panalibe ndi mmodzi yemwe kumwamba kapena pa dziko lapansi kapena kunsi kwa dziko lapansi woti afutukule bukulo kapena kuona zamʼkati mwake. Ndinalira kwambiri chifukwa panalibe amene anapezeka woyenera kufutukula bukuli kapena kuona zamʼkati mwake. Tsono mmodzi mwa akuluakulu aja anati kwa ine, “Usalire! Taona, Mkango wa fuko la Yuda, Muzu wa Davide, wapambana. Iye angathe kufutukula bukuli ndi kumatula zomatira zisanu ndi ziwirizo.”

Kenaka ndinaona Mwana Wankhosa akuoneka ngati wophedwa atayimirira pakatikati pa mpando waufumu uja ndi zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu aja. Mwana Wankhosayo anali ndi nyanga zisanu ndi ziwiri ndi maso asanu ndi awiri omwe ndi Mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu yomwe anayitumiza ku dziko lonse lapansi. Iye anabwera natenga buku lija limene linali mʼdzanja lamanja la wokhala pa mpando waufumuyo. Ndipo atalitenga, zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu 24 aja anadzigwetsa pansi pamaso pa Mwana Wankhosa. Aliyense wa akuluakuluwo anali ndi zeze ndiponso mbale zagolide zodzaza ndi lubani. Lubaniyo ndi mapemphero a oyera mtima. Ndipo ankayimba nyimbo yatsopano yakuti,

“Inu ndinu woyenera kulandira bukuli
    ndi kumatula zomatira zake,
chifukwa munaphedwa,
    ndipo magazi anu munagulira Mulungu
    anthu a fuko lililonse, a chiyankhulo chilichonse, ndi mtundu uliwonse.
10 Inu munawasandutsa kukhala mtundu waufumu ndi ansembe otumikira Mulungu,
    ndipo adzalamulira dziko lapansi.”

11 Kenaka nditayangʼananso ndinamva mawu a angelo ambiri, miyandamiyanda kuchulukitsa ndi miyandamiyanda. Anazungulira mpando waufumu pamodzi ndi zamoyo zija ndi akuluakulu aja. 12 Ndipo angelowo anayimba ndi mawu ofuwula akuti,

“Mwana Wankhosa amene anaphedwayu
    ndi woyenera kulandira ulamuliro, chuma, nzeru, mphamvu, ulemu,
    ulemerero ndi mayamiko.”

13 Kenaka ndinamva mawu a cholengedwa chilichonse kumwamba, pa dziko lapansi, kunsi kwa dziko lapansi, pa nyanja ndi zonse zili mʼmenemo zikuyimba kuti,

“Kwa wokhala pa mpando waufumu ndi kwa Mwana Wankhosa,
    kukhale mayamiko, ulemu, ulemerero ndi mphamvu
mpaka muyaya!”

14 Zamoyo zinayi zija zinati: “Ameni,” ndipo akuluakulu aja anadzigwetsa pansi napembedza.