Revelation 13 – KJV & CCL

King James Version

Revelation 13:1-18

1And I stood upon the sand of the sea, and saw a beast rise up out of the sea, having seven heads and ten horns, and upon his horns ten crowns, and upon his heads the name of blasphemy. 2And the beast which I saw was like unto a leopard, and his feet were as the feet of a bear, and his mouth as the mouth of a lion: and the dragon gave him his power, and his seat, and great authority. 3And I saw one of his heads as it were wounded to death; and his deadly wound was healed: and all the world wondered after the beast. 4And they worshipped the dragon which gave power unto the beast: and they worshipped the beast, saying, Who is like unto the beast? who is able to make war with him? 5And there was given unto him a mouth speaking great things and blasphemies; and power was given unto him to continue forty and two months. 6And he opened his mouth in blasphemy against God, to blaspheme his name, and his tabernacle, and them that dwell in heaven. 7And it was given unto him to make war with the saints, and to overcome them: and power was given him over all kindreds, and tongues, and nations. 8And all that dwell upon the earth shall worship him, whose names are not written in the book of life of the Lamb slain from the foundation of the world. 9If any man have an ear, let him hear. 10He that leadeth into captivity shall go into captivity: he that killeth with the sword must be killed with the sword. Here is the patience and the faith of the saints. 11And I beheld another beast coming up out of the earth; and he had two horns like a lamb, and he spake as a dragon. 12And he exerciseth all the power of the first beast before him, and causeth the earth and them which dwell therein to worship the first beast, whose deadly wound was healed. 13And he doeth great wonders, so that he maketh fire come down from heaven on the earth in the sight of men, 14And deceiveth them that dwell on the earth by the means of those miracles which he had power to do in the sight of the beast; saying to them that dwell on the earth, that they should make an image to the beast, which had the wound by a sword, and did live. 15And he had power to give life unto the image of the beast, that the image of the beast should both speak, and cause that as many as would not worship the image of the beast should be killed. 16And he causeth all, both small and great, rich and poor, free and bond, to receive a mark in their right hand, or in their foreheads: 17And that no man might buy or sell, save he that had the mark, or the name of the beast, or the number of his name. 18Here is wisdom. Let him that hath understanding count the number of the beast: for it is the number of a man; and his number is Six hundred threescore and six.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chivumbulutso 13:1-18

Chirombo Chotuluka Mʼnyanja

1Ndipo ndinaona chirombo chikutuluka mʼnyanja. Chinali ndi nyanga khumi ndi mitu isanu ndi iwiri. Pa nyanga iliyonse chinavala chipewa chaufumu, ndipo pa mutu uliwonse panali dzina lonyoza Mulungu. 2Chirombo chimene ndinachionacho chinali ngati kambuku, mapazi ake ngati chimbalangondo, kukamwa kwake ngati kwa mkango. Chinjoka chija chinapatsa chirombocho mphamvu zake, mpando wake waufumu ndiponso ulamuliro waukulu. 3Umodzi wa mitu wa chirombocho unkaoneka ngati uli ndi bala losati nʼkupola, koma nʼkuti balalo litapola. Dziko lonse linadabwa ndipo linatsatira chirombocho. 4Anthu anapembedza chinjoka chija chifukwa chinapereka ulamuliro wake kwa chirombocho. Nachonso chirombo chija anachipembedza nʼkumafunsa kuti, “Ndani angafanane ndi chirombochi? Ndani angachite nacho nkhondo?”

5Chirombo chija chinaloledwa kuyankhula mawu onyada ndi achipongwe kwa Mulungu. Chinapatsidwa mphamvu zolamulira pa miyezi 42. 6Ndipo chinayamba kuyankhula mawu achipongwe onyoza Mulungu, dzina lake, malo okhalamo ndi onse amene amakhala kumwamba. 7Chinaloledwa kuchita nkhondo ndi oyera mtima ndi kuwagonjetsa. Ndipo chinapatsidwanso mphamvu zolamulira anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse ndi chiyankhulo chilichonse. 8Anthu onse okhala pa dziko lapansi adzapembedza chirombocho, aliyense amene chilengedwere cha dziko lapansi dzina lake silinalembedwe mʼbuku la amoyo la Mwana Wankhosa anaphedwa uja.

9Iye amene ali ndi makutu, amve.

10“Woyenera kupita ku ukapolo,

adzapita ku ukapolo.

Woyenera kufa ndi lupanga,

adzafa ndi lupanga.”

Pamenepa kwa anthu a Mulungu pakufunika kupirira ndi kukhulupirika.

Chirombo Chotuluka Mʼnthaka

11Kenaka ndinaona chirombo china chikutuluka mʼnthaka. Chinali ndi nyanga ziwiri ngati mwana wankhosa koma kuyankhula kwake ngati chinjoka. 12Chinalamulira ndi mphamvu zonse za chirombo choyamba chija, ndipo chinachititsa kuti dziko lapansi ndi anthu okhalamo alambire chirombo choyamba chija, chimene bala lake losati nʼkupola linali litapola. 13Ndipo chinachita zizindikiro zazikulu zodabwitsa, mpaka kumagwetsa moto pa dziko lapansi kuchokera kumwamba anthu akuona. 14Chifukwa cha zizindikiro zimene chinaloledwa kuchita mʼmalo mwa chirombo choyamba chija, chimene bala lake linapola, chinanyenga anthu okhala pa dziko lapansi. Chinalamula anthu kuti apange fano mopereka ulemu kwa chirombo chimene chinavulazidwa ndi lupanga, koma nʼkukhalabe ndi moyo. 15Chirombo cha chiwirichi chinapatsidwa mphamvu zakupereka mpweya kwa fano la chirombo choyamba chija kuti liyankhule ndi kuphetsa aliyense wokana kupembedza fanolo. 16Chinakakamiza aliyense, wamngʼono, wamkulu, wolemera, wosauka, mfulu ndi kapolo kuti alembedwe chizindikiro pa dzanja lamanja kapena pa mphumi. 17Chinkachita zimenezi kuti wina aliyense asaloledwe kugula kapena kugulitsa kanthu ngati alibe chizindikiro chimenechi, chimene ndi dzina la chirombocho kapena nambala yotanthauza dzina lake.

18Pano pafunika nzeru. Munthu amene ali ndi nzeru atanthauze nambala ya chirombocho, pakuti nambalayo ikutanthauza munthu. Nambala yake ndi 666.