John 10 – KJV & CCL

King James Version

John 10:1-42

1Verily, verily, I say unto you, He that entereth not by the door into the sheepfold, but climbeth up some other way, the same is a thief and a robber. 2But he that entereth in by the door is the shepherd of the sheep. 3To him the porter openeth; and the sheep hear his voice: and he calleth his own sheep by name, and leadeth them out. 4And when he putteth forth his own sheep, he goeth before them, and the sheep follow him: for they know his voice. 5And a stranger will they not follow, but will flee from him: for they know not the voice of strangers. 6This parable spake Jesus unto them: but they understood not what things they were which he spake unto them. 7Then said Jesus unto them again, Verily, verily, I say unto you, I am the door of the sheep. 8All that ever came before me are thieves and robbers: but the sheep did not hear them. 9I am the door: by me if any man enter in, he shall be saved, and shall go in and out, and find pasture. 10The thief cometh not, but for to steal, and to kill, and to destroy: I am come that they might have life, and that they might have it more abundantly. 11I am the good shepherd: the good shepherd giveth his life for the sheep. 12But he that is an hireling, and not the shepherd, whose own the sheep are not, seeth the wolf coming, and leaveth the sheep, and fleeth: and the wolf catcheth them, and scattereth the sheep. 13The hireling fleeth, because he is an hireling, and careth not for the sheep. 14I am the good shepherd, and know my sheep, and am known of mine. 15As the Father knoweth me, even so know I the Father: and I lay down my life for the sheep. 16And other sheep I have, which are not of this fold: them also I must bring, and they shall hear my voice; and there shall be one fold, and one shepherd. 17Therefore doth my Father love me, because I lay down my life, that I might take it again. 18No man taketh it from me, but I lay it down of myself. I have power to lay it down, and I have power to take it again. This commandment have I received of my Father.

19¶ There was a division therefore again among the Jews for these sayings. 20And many of them said, He hath a devil, and is mad; why hear ye him? 21Others said, These are not the words of him that hath a devil. Can a devil open the eyes of the blind?

22¶ And it was at Jerusalem the feast of the dedication, and it was winter. 23And Jesus walked in the temple in Solomon’s porch. 24Then came the Jews round about him, and said unto him, How long dost thou make us to doubt? If thou be the Christ, tell us plainly. 25Jesus answered them, I told you, and ye believed not: the works that I do in my Father’s name, they bear witness of me. 26But ye believe not, because ye are not of my sheep, as I said unto you. 27My sheep hear my voice, and I know them, and they follow me: 28And I give unto them eternal life; and they shall never perish, neither shall any man pluck them out of my hand. 29My Father, which gave them me, is greater than all; and no man is able to pluck them out of my Father’s hand. 30I and my Father are one. 31Then the Jews took up stones again to stone him. 32Jesus answered them, Many good works have I shewed you from my Father; for which of those works do ye stone me? 33The Jews answered him, saying, For a good work we stone thee not; but for blasphemy; and because that thou, being a man, makest thyself God. 34Jesus answered them, Is it not written in your law, I said, Ye are gods? 35If he called them gods, unto whom the word of God came, and the scripture cannot be broken; 36Say ye of him, whom the Father hath sanctified, and sent into the world, Thou blasphemest; because I said, I am the Son of God? 37If I do not the works of my Father, believe me not. 38But if I do, though ye believe not me, believe the works: that ye may know, and believe, that the Father is in me, and I in him. 39Therefore they sought again to take him: but he escaped out of their hand, 40And went away again beyond Jordan into the place where John at first baptized; and there he abode. 41And many resorted unto him, and said, John did no miracle: but all things that John spake of this man were true. 42And many believed on him there.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yohane 10:1-42

Mʼbusa Wabwino ndi Nkhosa Zake

1“Zoonadi, Ine ndikukuwuzani inu Afarisi, kuti munthu amene salowera pa khomo mʼkhola la nkhosa, koma amalowera pena pake ndi wakuba ndi wachifwamba. 2Munthu amene amalowera pa khomo ndi mʼbusa wankhosazo. 3Mlonda amamutsekulira khomo, ndipo nkhosa zimamvera mawu ake. Iye amaziyitana mayina nkhosa zakezo, nazitulutsa. 4Akazitulutsa nkhosa zake zonse, iye amazitsogolera, ndipo nkhosa zakezo zimamutsata chifukwa zimadziwa mawu ake. 5Koma nkhosazo sizidzatsatira mlendo. Izo zidzamuthawa chifukwa sizizindikira mawu a mlendo.” 6Yesu ananena mawu ophiphiritsawa, koma Afarisi sanazindikire zimene ankawawuza.

7Choncho Yesu anatinso, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Ine ndine khomo la nkhosa. 8Onse amene anadza ndisanabwere Ine ndi akuba ndi achifwamba, ndipo nkhosa sizinawamvere. 9Ine ndine khomo, aliyense amene alowa kudzera mwa Ine adzapulumuka. Iye adzalowa ndi kutuluka ndi kupeza msipu. 10Mbala sibwera chabe koma kuti idzabe, kupha ndi kuwononga. Ine ndabwera kuti iwo akhale ndi moyo, ndi kukhala nawo wochuluka.

11“Ine ndine Mʼbusa wabwino. Mʼbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake. 12Wantchito ndi mʼbusa amene nkhosazo si zake. Choncho, pamene aona mmbulu ukubwera, iye amazisiya nkhosazo ndi kuthawa. Ndipo mmbulu umagwira nkhosazo ndikuzibalalitsa. 13Munthuyo amathawa chifukwa ndi wantchito ndipo sasamalira chilichonse cha nkhosazo.

14“Ine ndine mʼbusa wabwino. Ine ndimazidziwa nkhosa zanga ndipo nkhosa zangazo zimandidziwa, 15monga momwe Atate amandidziwa Ine, ndiponso Ine kudziwira Atatewo. Ndimapereka moyo wanga chifukwa cha nkhosa. 16Ine ndili ndi nkhosa zina zimene sizili za gulu ili. Ine ndiyenera kuzibweretsanso. Izonso zidzamvera mawu anga, ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi mʼbusa mmodzi. 17Nʼchifukwa chake Atate anga amandikonda, popeza Ine ndikupereka moyo wanga kuti ndiwutengenso. 18Palibe amene angawuchotse mwa Ine, koma ndikuwupereka mwakufuna kwanga. Ine ndili ndi ulamuliro wa kuwupereka ndi ulamuliro wakuwutenganso. Lamulo ili ndinalandira kwa Atate anga.”

19Pa mawu awa Ayuda anagawikananso. 20Ambiri a iwo anati, “Iye ndi wogwidwa ndi ziwanda ndi wamisala. Chifukwa chiyani mukumvera Iye?”

21Koma ena anati, “Awa si mawu a munthu wogwidwa ndi ziwanda. Kodi ziwanda zingathe bwanji kutsekula maso a wosaona?”

Kusakhulupirira kwa Ayuda

22Ku Yerusalemu kunali chikondwerero chokumbukira kupatulidwa kwa Nyumba ya Mulungu. Inali nthawi yozizira, 23ndipo Yesu ankayenda mʼbwalo la Nyumbayo ku malo a Solomoni. 24Ayuda anamuzungulira Iye akunena kuti, “Kodi iwe udzazunguza malingaliro athu mpaka liti? Ngati iwe ndi Khristu, tiwuze momveka.”

25Yesu anayankha kuti, “Ine ndimakuwuzani, koma inu simukhulupirira. Ntchito zimene ndikuchita mʼdzina la Atate anga zikundichitira umboni, 26koma inu simukhulupirira chifukwa simuli a gulu lankhosa zanga. 27Nkhosa zanga zimamva mawu anga, Ine ndimazidziwa, ndipo zimanditsata Ine. 28Ine ndimazipatsa moyo wosatha ndipo sizidzawonongeka. Palibe amene adzazikwatula mʼdzanja langa. 29Atate anga, amene anandipatsa Ine, ndi akulu kuposa onse. Palibe amene angazikwatule mʼdzanja la Atate anga. 30Ine ndi Atate ndife amodzi.”

31Ayuda anatolanso miyala kuti amugende Iye, 32koma Yesu anawawuza kuti, “Ine ndakuonetsani zinthu zambiri zabwino zodabwitsa kuchokera kwa Atate. Nʼchifukwa chiti mwa izi chimene mukundigendera?”

33Ayuda anayankha kuti, “Ife sitikukugenda chifukwa cha izi, koma popeza ukunyoza Mulungu, chifukwa iwe, munthu wamba, ukuti ndiwe Mulungu.”

34Yesu anawayankha kuti, “Kodi sizinalembedwa mʼmalamulo anu kuti, ‘Ine ndanena kuti ndinu milungu?’ 35Ngati anawatcha milungu anthu amene analandira mawu a Mulungu, pajatu Malemba sangasweke, 36nanga bwanji uyu amene Atate anamuyika padera monga wake weniweni ndi kumutuma ku dziko lapansi? Nanga ndi chifukwa chiyani mukundinena Ine kuti ndikuchita chipongwe? Kodi nʼchifukwa choti ndanena kuti, ‘Ine ndine Mwana wa Mulungu?’ 37Musandikhulupirire Ine ngati sindichita ntchito za Atate anga. 38Koma ngati Ine ndikuchita zimenezi, ngakhale kuti simundikhulupirira, khulupirirani ntchito zodabwitsazo, ndipo mudziwe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa Ine, ndiponso Ine ndili mwa Atate.” 39Iwo anafuna kumugwiranso koma anawapulumuka mʼmanja mwawo.

40Kenaka Yesu anabwereranso kutsidya la mtsinje wa Yorodani kumalo kumene Yohane ankabatiza mʼmasiku akale. Iye anakhala kumeneko 41ndipo anthu ambiri anabwera kwa Iye. Iwo anati, “Ngakhale kuti Yohane sanachite chizindikiro chodabwitsa, zonse zimene Yohane ananena za munthu uyu zinali zoona.” 42Ndipo pamalo amenewo ambiri anakhulupirira Yesu.