Jeremiah 38 – KJV & CCL

King James Version

Jeremiah 38:1-28

1Then Shephatiah the son of Mattan, and Gedaliah the son of Pashur, and Jucal the son of Shelemiah, and Pashur the son of Malchiah, heard the words that Jeremiah had spoken unto all the people, saying, 2Thus saith the LORD, He that remaineth in this city shall die by the sword, by the famine, and by the pestilence: but he that goeth forth to the Chaldeans shall live; for he shall have his life for a prey, and shall live. 3Thus saith the LORD, This city shall surely be given into the hand of the king of Babylon’s army, which shall take it. 4Therefore the princes said unto the king, We beseech thee, let this man be put to death: for thus he weakeneth the hands of the men of war that remain in this city, and the hands of all the people, in speaking such words unto them: for this man seeketh not the welfare of this people, but the hurt.38.4 welfare: Heb. peace 5Then Zedekiah the king said, Behold, he is in your hand: for the king is not he that can do any thing against you. 6Then took they Jeremiah, and cast him into the dungeon of Malchiah the son of Hammelech, that was in the court of the prison: and they let down Jeremiah with cords. And in the dungeon there was no water, but mire: so Jeremiah sunk in the mire.38.6 of Hammelech: or, of the king

7¶ Now when Ebed-melech the Ethiopian, one of the eunuchs which was in the king’s house, heard that they had put Jeremiah in the dungeon; the king then sitting in the gate of Benjamin; 8Ebed-melech went forth out of the king’s house, and spake to the king, saying, 9My lord the king, these men have done evil in all that they have done to Jeremiah the prophet, whom they have cast into the dungeon; and he is like to die for hunger in the place where he is: for there is no more bread in the city.38.9 he is like…: Heb. he will die 10Then the king commanded Ebed-melech the Ethiopian, saying, Take from hence thirty men with thee, and take up Jeremiah the prophet out of the dungeon, before he die.38.10 with thee: Heb. in thine hand 11So Ebed-melech took the men with him, and went into the house of the king under the treasury, and took thence old cast clouts and old rotten rags, and let them down by cords into the dungeon to Jeremiah. 12And Ebed-melech the Ethiopian said unto Jeremiah, Put now these old cast clouts and rotten rags under thine armholes under the cords. And Jeremiah did so. 13So they drew up Jeremiah with cords, and took him up out of the dungeon: and Jeremiah remained in the court of the prison.

14¶ Then Zedekiah the king sent, and took Jeremiah the prophet unto him into the third entry that is in the house of the LORD: and the king said unto Jeremiah, I will ask thee a thing; hide nothing from me.38.14 third: or, principal 15Then Jeremiah said unto Zedekiah, If I declare it unto thee, wilt thou not surely put me to death? and if I give thee counsel, wilt thou not hearken unto me? 16So Zedekiah the king sware secretly unto Jeremiah, saying, As the LORD liveth, that made us this soul, I will not put thee to death, neither will I give thee into the hand of these men that seek thy life. 17Then said Jeremiah unto Zedekiah, Thus saith the LORD, the God of hosts, the God of Israel; If thou wilt assuredly go forth unto the king of Babylon’s princes, then thy soul shall live, and this city shall not be burned with fire; and thou shalt live, and thine house: 18But if thou wilt not go forth to the king of Babylon’s princes, then shall this city be given into the hand of the Chaldeans, and they shall burn it with fire, and thou shalt not escape out of their hand. 19And Zedekiah the king said unto Jeremiah, I am afraid of the Jews that are fallen to the Chaldeans, lest they deliver me into their hand, and they mock me. 20But Jeremiah said, They shall not deliver thee. Obey, I beseech thee, the voice of the LORD, which I speak unto thee: so it shall be well unto thee, and thy soul shall live. 21But if thou refuse to go forth, this is the word that the LORD hath shewed me: 22And, behold, all the women that are left in the king of Judah’s house shall be brought forth to the king of Babylon’s princes, and those women shall say, Thy friends have set thee on, and have prevailed against thee: thy feet are sunk in the mire, and they are turned away back.38.22 Thy friends: Heb. Men of thy peace 23So they shall bring out all thy wives and thy children to the Chaldeans: and thou shalt not escape out of their hand, but shalt be taken by the hand of the king of Babylon: and thou shalt cause this city to be burned with fire.38.23 thou shalt cause…: Heb. thou shalt burn, etc

24¶ Then said Zedekiah unto Jeremiah, Let no man know of these words, and thou shalt not die. 25But if the princes hear that I have talked with thee, and they come unto thee, and say unto thee, Declare unto us now what thou hast said unto the king, hide it not from us, and we will not put thee to death; also what the king said unto thee: 26Then thou shalt say unto them, I presented my supplication before the king, that he would not cause me to return to Jonathan’s house, to die there. 27Then came all the princes unto Jeremiah, and asked him: and he told them according to all these words that the king had commanded. So they left off speaking with him; for the matter was not perceived.38.27 they…: Heb. they were silent from him 28So Jeremiah abode in the court of the prison until the day that Jerusalem was taken: and he was there when Jerusalem was taken.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yeremiya 38:1-28

Yeremiya Aponyedwa Mʼchitsime cha Matope

1Sefatiya mwana wa Matani, Gedaliya mwana wa Pasi-Huri, Yukali mwana wa Selemiya, ndi Pasi-Huri mwana wa Malikiya anamva zimene Yeremiya ankawuza anthu onse kuti, 2“Yehova akuti, ‘Aliyense amene akhale mu mzinda muno adzafa ndi nkhondo njala kapena mliri. Koma aliyense amene atatuluke kukadzipereka kwa Ababuloni adzapulumutsa moyo wake; iyeyo adzakhala ndi moyo. 3Mzinda uno udzaperekedwa ndithu kwa gulu lankhondo la mfumu ya ku Babuloni, amene adzawulande.’ ”

4Tsono akuluakuluwo anawuza mfumu kuti, “Munthu uyu ayenera kuphedwa. Iye akutayitsa mtima asilikali pamodzi ndi anthu onse amene atsala mu mzinda muno, chifukwa cha zimene akuwawuza. Munthu ameneyu sakufunira zabwino anthuwa koma chiwonongeko chawo.”

5Mfumu Zedekiya anayankha kuti, “Munthuyu ali mʼmanja mwanu. Ine sindingakuletseni chimene mukufuna kumuchitira.”

6Choncho iwo anatenga Yeremiya nakamuponya mʼchitsime cha Malikiya, mwana wa mfumu, chimene chinali mʼbwalo la alonda. Iwo anamutsitsira mʼdzenjemo ndi chingwe. Munalibe madzi koma matope okhaokha, ndipo Yeremiya anamira mʼmatopewo.

7Koma Ebedi-Meleki, Mkusi, mmodzi mwa anthu ofulidwa ogwira ntchito mʼnyumba ya mfumu, anamva kuti Yeremiya anamuponya mʼchitsime. Nthawi imeneyo nʼkuti mfumu ili ku chipata cha Benjamini. 8Ebedi-Meleki anatuluka ku nyumba ya mfumu kukayiwuza kuti, 9“Mbuye wanga mfumu, zimene anthu awa amuchitira mneneri Yeremiya ndi zoyipa kwambiri. Iwo amuponya mʼchitsime, ndipo adzafa ndi njala chifukwa buledi watha mu mzinda muno.”

10Tsono mfumu inalamula Ebedi-Meleki, Mkusi, kuti, “Tenga anthu makumi atatu, ndipo mukamutulutse mʼchitsimemo mneneri Yeremiya asanafe.”

11Pamenepo Ebedi-Meleki anatenga anthuwo, napita nawo ku nyumba ya mfumu ya pansi pa chipinda chosungiramo chuma. Kumeneko anakatengako sanza ndipo anatsitsira sanzazo ndi chingwe mʼchitsime mʼmene munali Yeremiya. 12Ebedi-Meleki, Mkusi, anawuza Yeremiya kuti, “Ika sanzazo mkwapa mwako kuti zingwe zingakupweteke.” Yeremiya anachitadi zimenezi, 13ndipo anamukoka ndi zingwe ndi kumutulutsa mʼchitsimecho. Ndipo Yeremiya anakhalabe ku bwalo la alonda.

Zedekiya Afunsanso Yeremiya

14Tsiku lina Mfumu Zedekiya anayitana mneneri Yeremiya ndipo anabwera naye ku chipata chachitatu cha Nyumba ya Yehova. Mfumu inawuza Yeremiya kuti, “Ndikufuna kukufunsa kanthu kena, ndipo usandibisire chilichonse.”

15Yeremiya anati kwa Zedekiya, “Ndikakuyankhani, kodi simundipha? Ngakhaletu ine nditakulangizani, inu simudzandimvera.”

16Koma Mfumu Zedekiya mwachinsinsi inalumbira kwa Yeremiya kuti, “Pali Yehova wamoyo, amene amatipatsa moyo, sindidzakupha ngakhalenso kukupereka kwa amene akufuna kukuphawa.”

17Pamenepo Yeremiya anati kwa Zedekiya, “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ngati mutuluka kukadzipereka kwa ankhondo a mfumu ya ku Babuloni, mudzakhala ndi moyo ndipo mzinda uno sadzawutentha, inu pamodzi ndi banja lanu mudzakhala ndi moyo. 18Koma ngati simutuluka kukadzipereka kwa ankhondo a mfumu ya ku Babuloni, mzinda uno udzaperekedwa kwa Ababuloni ndipo adzawutentha; inuyo simudzapulumuka mʼdzanja mwawo.’ ”

19Mfumu Zedekiya inati kwa Yeremiya, “Ine ndikuopa Ayuda amene anathawira kale kwa Ababuloni, pakuti mwina Ababuloniwo adzandipereka kwa Ayudawo ndipo iwowo adzandizunza.”

20Yeremiya anayankha kuti, “Ngati mumvera Yehova ndi kuchita zimene ndakuwuzani, ndiye kuti zinthu zidzakuyenderani bwino. Inu simudzaphedwa. 21Koma mukakana kudzipereka, chimene Yehova wandiwululira ndi ichi: 22Akazi onse amene atsala mʼnyumba ya mfumu ya Yuda adzaperekedwa kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babuloni. Akazi amenewo adzakuwuzani kuti,

“ ‘Abwenzi ako okhulupirika aja anakusokeretsa,

ndipo anakugonjetsa.

Poti tsopano miyendo yako yazama mʼmatope;

abwenzi ako aja akusiya.’

23“Akazi pamodzi ndi ana anu adzaperekedwa kwa Ababuloni. Inuyo simudzapulumuka mʼmanja mwawo koma mfumu ya ku Babuloni idzakugwirani; mzinda uno adzawutentha.”

24Pamenepo Zedekiya anati kwa Yeremiya, “Usawuze munthu wina aliyense zimene takambiranazi, ukatero udzaphedwa. 25Akuluakulu akamva kuti ndinayankhula nawe ndipo akabwera kwa iwe nʼkudzakufunsa kuti, ‘Tiwuze zimene unanena kwa mfumu ndi zimene mfumu inanena kwa iwe; usatibisire, ukatero tidzakupha,’ 26udzawawuze kuti, ‘Ine ndimapempha mfumu kuti isandibwezerenso ku nyumba ya Yonatani kuti ndikafere kumeneko.’ ”

27Akuluakulu onse anabweradi kwa Yeremiya kudzamufunsa. Iye anawayankha monga momwe mfumu inamulamula. Choncho palibe amene ananenanso kanthu, pakuti palibe amene anamva zomwe anakambirana ndi mfumu.

28Ndipo Yeremiya anakhalabe mʼbwalo la alonda mpaka tsiku limene mzinda wa Yerusalemu unalandidwa.