Isaiah 51 – KJV & CCL

King James Version

Isaiah 51:1-23

1Hearken to me, ye that follow after righteousness, ye that seek the LORD: look unto the rock whence ye are hewn, and to the hole of the pit whence ye are digged. 2Look unto Abraham your father, and unto Sarah that bare you: for I called him alone, and blessed him, and increased him. 3For the LORD shall comfort Zion: he will comfort all her waste places; and he will make her wilderness like Eden, and her desert like the garden of the LORD; joy and gladness shall be found therein, thanksgiving, and the voice of melody.

4¶ Hearken unto me, my people; and give ear unto me, O my nation: for a law shall proceed from me, and I will make my judgment to rest for a light of the people. 5My righteousness is near; my salvation is gone forth, and mine arms shall judge the people; the isles shall wait upon me, and on mine arm shall they trust. 6Lift up your eyes to the heavens, and look upon the earth beneath: for the heavens shall vanish away like smoke, and the earth shall wax old like a garment, and they that dwell therein shall die in like manner: but my salvation shall be for ever, and my righteousness shall not be abolished.

7¶ Hearken unto me, ye that know righteousness, the people in whose heart is my law; fear ye not the reproach of men, neither be ye afraid of their revilings. 8For the moth shall eat them up like a garment, and the worm shall eat them like wool: but my righteousness shall be for ever, and my salvation from generation to generation.

9¶ Awake, awake, put on strength, O arm of the LORD; awake, as in the ancient days, in the generations of old. Art thou not it that hath cut Rahab, and wounded the dragon? 10Art thou not it which hath dried the sea, the waters of the great deep; that hath made the depths of the sea a way for the ransomed to pass over? 11Therefore the redeemed of the LORD shall return, and come with singing unto Zion; and everlasting joy shall be upon their head: they shall obtain gladness and joy; and sorrow and mourning shall flee away. 12I, even I, am he that comforteth you: who art thou, that thou shouldest be afraid of a man that shall die, and of the son of man which shall be made as grass; 13And forgettest the LORD thy maker, that hath stretched forth the heavens, and laid the foundations of the earth; and hast feared continually every day because of the fury of the oppressor, as if he were ready to destroy? and where is the fury of the oppressor?51.13 were…: or, made himself ready 14The captive exile hasteneth that he may be loosed, and that he should not die in the pit, nor that his bread should fail. 15But I am the LORD thy God, that divided the sea, whose waves roared: The LORD of hosts is his name. 16And I have put my words in thy mouth, and I have covered thee in the shadow of mine hand, that I may plant the heavens, and lay the foundations of the earth, and say unto Zion, Thou art my people.

17¶ Awake, awake, stand up, O Jerusalem, which hast drunk at the hand of the LORD the cup of his fury; thou hast drunken the dregs of the cup of trembling, and wrung them out. 18There is none to guide her among all the sons whom she hath brought forth; neither is there any that taketh her by the hand of all the sons that she hath brought up. 19These two things are come unto thee; who shall be sorry for thee? desolation, and destruction, and the famine, and the sword: by whom shall I comfort thee?51.19 are…: Heb. happened51.19 destruction: Heb. breaking 20Thy sons have fainted, they lie at the head of all the streets, as a wild bull in a net: they are full of the fury of the LORD, the rebuke of thy God.

21¶ Therefore hear now this, thou afflicted, and drunken, but not with wine: 22Thus saith thy Lord the LORD, and thy God that pleadeth the cause of his people, Behold, I have taken out of thine hand the cup of trembling, even the dregs of the cup of my fury; thou shalt no more drink it again: 23But I will put it into the hand of them that afflict thee; which have said to thy soul, Bow down, that we may go over: and thou hast laid thy body as the ground, and as the street, to them that went over.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yesaya 51:1-23

Chipulumutso Chamuyaya cha Ziyoni

1“Mverani Ine, inu amene mukufuna chipulumutso

ndiponso amene mumafunafuna Yehova:

Taganizani za thanthwe kumene munasemedwa

ndipo ku ngwenya kumene anakukumbani;

2taganizani za Abrahamu, kholo lanu,

ndi Sara, amene anakubalani.

Pamene ndinkamuyitana nʼkuti alibe mwana,

koma ndinamudalitsa ndi kumupatsa ana ambiri.

3Yehova adzatonthozadi Ziyoni,

ndipo adzachitira chifundo mabwinja ake onse;

Dziko lake la chipululu adzalisandutsa ngati Edeni,

malo ake owuma ngati munda wa Yehova.

Anthu adzayimba nyimbo zonditamanda

ndi kundiyamika.

4“Mverani Ine, anthu anga:

tcherani khutu, inu mtundu wanga:

malangizo adzachokera kwa Ine;

cholungama changa chidzawunikira anthu a mitundu yonse.

5Ndili pafupi kubwera kudzawombola anthu anga.

Ndidzabwera mofulumira ngati kuwunika kudzapulumutsa anthu anga;

ndipo ndidzalamulira anthu a mitundu yonse.

Mayiko akutali akundiyembekezera.

Iwo akudikira kuti ndidzawapulumutse.

6Kwezani maso anu mlengalenga,

yangʼanani pansi pa dziko;

mlengalenga udzazimirira ngati utsi,

dziko lapansi lidzatha ngati chovala

ndipo anthu ake adzafa ngati nsabwe.

Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka muyaya,

chilungamo changa chidzakhala cha nthawi zonse.

7“Mverani Ine, inu amene mukudziwa choonadi,

anthu inu amene mukusunga malangizo anga mʼmitima yanu;

musaope kudzudzulidwa ndi anthu

kapena kuopsezedwa akamakulalatirani.

8Pakuti njenjete idzawadya ngati chovala;

mbozi idzawadya ngati thonje.

Koma chilungamo changa chidzakhala mpaka muyaya,

chipulumutso changa chidzakhala mpaka mibadomibado.”

9Dzambatukani, dzambatukani! Valani zilimbe,

Inu Yehova;

dzambatukani, monga munkachitira masiku amakedzana,

monga nthawi ya mibado yakale.

Si ndinu kodi amene munaduladula Rahabe,

amene munabaya chinjoka cha mʼnyanja chija?

10Kodi sindinu amene munawumitsa nyanja yayikulu,

madzi ozama kwambiri aja?

Kodi sindinu amene munapanga njira pa madzi ozama,

kuti anthu amene munawapulumutsa awoloke powuma?

11Anthu amene Yehova anawawombola adzabwerera

nakafika ku Ziyoni nyimbo ili pakamwa;

chimwemwe chamuyaya chizidzaonekera pa nkhope zawo.

Adzakhala ndi chikondwerero ndi chimwemwe,

chisoni ndi kubuwula zidzathawa.

12Yehova akuti, “Ndinetu amene ndimakutonthozani mtima.

Chifukwa chiyani mukuopa munthu woti adzafa?

Mukuopa munthu woti monga udzu sadzakhalitsa.

13Koma inu mumayiwala Yehova Mlengi wanu,

amene anayala za mlengalenga

ndi kuyika maziko a dziko lapansi.

Inu nthawi zonse mumaopsezedwa

chifukwa cha ukali wa anthu okuponderezani

amene angofuna kukuwonongani.

Kodi uli kuti tsopano ukali wa anthu okuponderezaniwo?

14Amʼndende adzamasulidwa posachedwa;

sadzalowa mʼmanda awo,

kapena kusowa chakudya.

15Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu,

amene ndimavundula nyanja kotero mafunde ake amakokoma.

Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.

16Ndayika mawu anga mʼkamwa mwanu

ndipo ndakuphimbani ndi mthunzi wa dzanja langa.

Ine ndimayika pa malo pake zinthu za mlengalenga,

ndipo ndinayika maziko a dziko lapansi,

ndimawuza anthu a ku Ziyoni kuti, ‘Ndinu anthu anga.’ ”

Kutha kwa Mavuto A Yerusalemu

17Dzambatuka, dzambatuka!

Imirira iwe Yerusalemu.

Iwe amene wamwa chikho cha mkwiyo

chimene Yehova anakupatsa.

Iwe amene unagugudiza

chikho chochititsa chizwezwe.

18Mwa ana onse amene anabereka,

panalibe ndi mmodzi yemwe anamutsogolera;

mwa ana onse amene analera,

panalibe ndi mmodzi yemwe anamugwira dzanja.

19Mavuto awiriwa akugwera iwe.

Dziko lako lasakazika ndi kuwonongeka. Anthu afa ndi njala ndi lupanga.

Ndani angakumvere chisoni?

Ndani angakutonthoze?

20Ana ako akomoka;

ali lambalamba pa msewu,

ngati mphoyo yogwidwa mu ukonde.

Ukali wa Yehova

ndi chidzudzulo chake zidzawagwera.

21Nʼchifukwa chake imva izi iwe amene ukuvutika,

iwe amene waledzera, koma osati ndi vinyo.

22Ambuye Yehova wanu,

Mulungu amene amateteza anthu ake akuti,

“Taona, ndachotsa mʼdzanja lako

chikho chimene chimakuchititsa kudzandira;

sudzamwanso chikho

cha ukali wanga.

23Ndidzapereka chikhocho kwa anthu amene amakuzunza,

amene ankakuwuza kuti,

‘gona pansi tikuyende pa msana.’

Ndipo msana wako anawuyesa pansi popondapo,

ngati msewu woti ayendepo.”