2 Timothy 1 – KJV & CCL

King James Version

2 Timothy 1:1-18

1Paul, an apostle of Jesus Christ by the will of God, according to the promise of life which is in Christ Jesus, 2To Timothy, my dearly beloved son: Grace, mercy, and peace, from God the Father and Christ Jesus our Lord. 3I thank God, whom I serve from my forefathers with pure conscience, that without ceasing I have remembrance of thee in my prayers night and day; 4Greatly desiring to see thee, being mindful of thy tears, that I may be filled with joy; 5When I call to remembrance the unfeigned faith that is in thee, which dwelt first in thy grandmother Lois, and thy mother Eunice; and I am persuaded that in thee also. 6Wherefore I put thee in remembrance that thou stir up the gift of God, which is in thee by the putting on of my hands. 7For God hath not given us the spirit of fear; but of power, and of love, and of a sound mind. 8Be not thou therefore ashamed of the testimony of our Lord, nor of me his prisoner: but be thou partaker of the afflictions of the gospel according to the power of God; 9Who hath saved us, and called us with an holy calling, not according to our works, but according to his own purpose and grace, which was given us in Christ Jesus before the world began, 10But is now made manifest by the appearing of our Saviour Jesus Christ, who hath abolished death, and hath brought life and immortality to light through the gospel: 11Whereunto I am appointed a preacher, and an apostle, and a teacher of the Gentiles. 12For the which cause I also suffer these things: nevertheless I am not ashamed: for I know whom I have believed, and am persuaded that he is able to keep that which I have committed unto him against that day. 13Hold fast the form of sound words, which thou hast heard of me, in faith and love which is in Christ Jesus. 14That good thing which was committed unto thee keep by the Holy Ghost which dwelleth in us. 15This thou knowest, that all they which are in Asia be turned away from me; of whom are Phygellus and Hermogenes. 16The Lord give mercy unto the house of Onesiphorus; for he oft refreshed me, and was not ashamed of my chain: 17But, when he was in Rome, he sought me out very diligently, and found me. 18The Lord grant unto him that he may find mercy of the Lord in that day: and in how many things he ministered unto me at Ephesus, thou knowest very well.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Timoteyo 1:1-18

1Paulo mtumwi wa Khristu Yesu mwa chifuniro cha Mulungu. Anandituma kuti ndilalike za lonjezo la moyo umene uli mwa Khristu Yesu.

2Kwa Timoteyo, mwana wanga wokondedwa:

Chisomo, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye athu Yesu Khristu.

Chilimbikitso Pokhala Wokhulupirika

3Ndikuyamika Mulungu amene ndimamutumikira ndi chikumbumtima chosatsutsika, monga momwe ankachitira makolo anga. Usiku ndi usana ndimakukumbukira mosalekeza mʼmapemphero anga. 4Ndikamakumbukira misozi yako, ndimalakalaka nditakuona kuti ndidzazidwe ndi chimwemwe. 5Ndakumbukira za chikhulupiriro chako choona chimene chinayamba mwa agogo ako a Loisi ndi mwa amayi ako Yunike ndipo ndikutsimikiza mtima kuti chilinso mwa iwe.

Kumvera Paulo ndi Uthenga Wabwino

6Nʼchifukwa chake ndikukukumbutsa kuti upemerere monga amachitira moto, mphatso imene Mulungu anakupatsa nditakusanjika manja. 7Pakuti Mzimu amene Mulungu anatipatsa, si Mzimu wotipatsa manyazi, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzisunga.

8Choncho usachite manyazi kuchitira umboni Ambuye athu, kapena kuchita manyazi chifukwa cha ine wamʼndende. Koma umve nane zowawa chifukwa cha Uthenga Wabwino, mothandizidwa ndi mphamvu za Mulungu. 9Iye anatipulumutsa ndipo anatiyitanira ku moyo oyera mtima, osati chifukwa cha chilichonse chimene tinachita, koma chifukwa cha chikonzero ndi chisomo chake. Chisomo chimenechi anatipatsa ife mwa Khristu Yesu nthawi isanayambe. 10Koma tsopano Mulungu watiwululira kudzera mʼkuoneka kwa Mpulumutsi wathu, Khristu Yesu, amene anathetsa mphamvu za imfa ndipo mwa Uthenga Wabwino anaonetsa poyera moyo umene sungafe. 11Ine ndinasankhidwa kukhala wamthenga, ndi mtumwi ndi mphunzitsi wa Uthenga Wabwinowu. 12Nʼchifukwa chake ndikuvutika monga ndililimu. Komabe zimenezi sizikundichititsa manyazi, popeza ndikumudziwa amene ndamukhulupirira ndipo ndikutsimikiza mtima kuti akhoza kusamalira chimene ndinamusungitsa mpaka tsiku lijalo.

13Zimene unamva kwa ine, uzisunge kuti zikhale chitsanzo cha chiphunzitso choona, mwa chikhulupiriro ndi chikondi mwa Khristu Yesu. 14Samalira bwino zokoma zimene anakusungitsa. Uzisamalire mothandizidwa ndi Mzimu Woyera amene amakhala mwa ife.

Zitsanzo za Kusakhulupirika ndi Kukhulupirika

15Iwe udziwa kuti onse a mʼchigawo cha Asiya anandithawa, kuphatikizapo Fugelo ndi Herimogene omwe.

16Mulungu achitire chifundo banja lonse la Onesiforo chifukwa ankandisangalatsa kawirikawiri ndipo sankachita nane manyazi ngakhale ndinali womangidwa ndi maunyolo. 17Mʼmalo mwake, atangofika ku Roma, anandifunafuna ndipo anandipeza. 18Ambuye amulole kuti adzalandire chifundo kwa Ambuye pa tsiku lijalo! Ukudziwa bwino momwe iye anandithandizira mʼnjira zosiyanasiyana ku Efeso.