1 Peter 1 – KJV & CCL

King James Version

1 Peter 1:1-25

1Peter, an apostle of Jesus Christ, to the strangers scattered throughout Pontus, Galatia, Cappadocia, Asia, and Bithynia, 2Elect according to the foreknowledge of God the Father, through sanctification of the Spirit, unto obedience and sprinkling of the blood of Jesus Christ: Grace unto you, and peace, be multiplied.

3Blessed be the God and Father of our Lord Jesus Christ, which according to his abundant mercy hath begotten us again unto a lively hope by the resurrection of Jesus Christ from the dead, 4To an inheritance incorruptible, and undefiled, and that fadeth not away, reserved in heaven for you, 5Who are kept by the power of God through faith unto salvation ready to be revealed in the last time. 6Wherein ye greatly rejoice, though now for a season, if need be, ye are in heaviness through manifold temptations: 7That the trial of your faith, being much more precious than of gold that perisheth, though it be tried with fire, might be found unto praise and honour and glory at the appearing of Jesus Christ: 8Whom having not seen, ye love; in whom, though now ye see him not, yet believing, ye rejoice with joy unspeakable and full of glory: 9Receiving the end of your faith, even the salvation of your souls. 10Of which salvation the prophets have enquired and searched diligently, who prophesied of the grace that should come unto you: 11Searching what, or what manner of time the Spirit of Christ which was in them did signify, when it testified beforehand the sufferings of Christ, and the glory that should follow. 12Unto whom it was revealed, that not unto themselves, but unto us they did minister the things, which are now reported unto you by them that have preached the gospel unto you with the Holy Ghost sent down from heaven; which things the angels desire to look into. 13Wherefore gird up the loins of your mind, be sober, and hope to the end for the grace that is to be brought unto you at the revelation of Jesus Christ; 14As obedient children, not fashioning yourselves according to the former lusts in your ignorance: 15But as he which hath called you is holy, so be ye holy in all manner of conversation; 16Because it is written, Be ye holy; for I am holy. 17And if ye call on the Father, who without respect of persons judgeth according to every man’s work, pass the time of your sojourning here in fear: 18Forasmuch as ye know that ye were not redeemed with corruptible things, as silver and gold, from your vain conversation received by tradition from your fathers; 19But with the precious blood of Christ, as of a lamb without blemish and without spot: 20Who verily was foreordained before the foundation of the world, but was manifest in these last times for you, 21Who by him do believe in God, that raised him up from the dead, and gave him glory; that your faith and hope might be in God. 22Seeing ye have purified your souls in obeying the truth through the Spirit unto unfeigned love of the brethren, see that ye love one another with a pure heart fervently: 23Being born again, not of corruptible seed, but of incorruptible, by the word of God, which liveth and abideth for ever. 24For all flesh is as grass, and all the glory of man as the flower of grass. The grass withereth, and the flower thereof falleth away: 25But the word of the Lord endureth for ever. And this is the word which by the gospel is preached unto you.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Petro 1:1-25

1Ndine Petro, mtumwi wa Yesu Khristu.

Ndikulemba kalatayi kwa onse osankhidwa ndi Mulungu, alendo mʼdziko lapansi, obalalikira ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya ndi Bituniya. 2Mulungu Atate anakusankhani, atakudziwani kuyambira pachiyambi, ndipo Mzimu Woyera wakuyeretsani kuti mumvere Yesu Khristu ndikutsukidwa ndi magazi ake.

Chisomo ndi mtendere zikhale ndi inu mochuluka.

Kuyamika Mulungu Chifukwa cha Chiyembekezo Chamoyo

3Alemekezedwe Mulungu, Atate wa Ambuye athu Yesu Khristu. Mwachifundo chake chachikulu anatibadwitsa kwatsopano, mʼchiyembekezo chamoyo pomuukitsa Yesu Khristu kwa akufa, 4kuti tidzalandire chuma chomwe sichingawonongeke, kuyipitsidwa kapena kufota. Chuma chimenechi akukusungirani kumwamba. 5Mwachikhulupiriro, mukusungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mpaka chipulumutso chitafika chimene chinakonzedwa kuti adzachionetse nthawi yotsiriza. 6Zimenezi zikukondweretseni kwambiri, ngakhale tsopano, kwa kanthawi kochepa, mukumva zowawa mʼmayesero osiyanasiyana. 7Mayeserowa abwera nʼcholinga chakuti chikhulupiriro chanu, chimene ndi chamtengo woposa wa golide, amene amawonongeka ngakhale amayengedwa ndi moto, chitsimikizike kuti ndi chenicheni. Pamenepo ndiye mudzalandire mayamiko, ulemerero ndi ulemu pamene Yesu Khristu adzaoneka. 8Ngakhale kuti simunamuone, mumamukonda; ndipo ngakhale kuti simukumuona tsopano, mumamukhulupirira ndipo mumakondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka. 9Motero mukulandira mphotho ya chikhulupiriro chanu, ndiyo chipulumutso cha moyo wanu.

10Kunena za chipulumutso chimenechi, aneneri amene ananeneratu za chisomo chimene chimabwera kwa inu, anafunafuna mofufuzafufuza za chipulumutsochi, 11kufuna kudziwa nthawi ndi momwe zidzachitikire zinthu zimene Mzimu wa Khristu amene ali mwa iwo ankanenera za kuvutika kwa Khristu, ndi ulemerero umene adzakhale nawo pambuyo pake. 12Mulungu anawawululira kuti ntchito yawoyo sankayigwira chifukwa cha iwo eni, koma chifukwa inu, pamene iwo ankayankhula zinthu zimene mwamva tsopano kuchokera kwa amene amalalikira Uthenga Wabwino mwamphamvu ya Mzimu Woyera wotumidwa kuchokera kumwamba. Ngakhale angelo amalakalaka kuona nawo zinthuzi.

Khalani Oyera Mtima

13Choncho konzani mtima wanu, khalani odziretsa; khazikitsani chiyembekezo chanu kotheratu pa chisomo chimene mudzapatsidwe pamene Yesu Khristu adzaonekera. 14Monga ana omvera, musatsatenso zilakolako zoyipa zomwe munali nazo pamene munali osadziwa. 15Koma monga amene anakuyitanani ndi woyera, inunso khalani oyera mtima mʼmakhalidwe anu wonse. 16Pakuti, kwalembedwa kuti, “Khalani oyera mtima, chifukwa Ine ndine Woyera.”

17Popeza mumapemphera kwa Atate amene amaweruza munthu aliyense mopanda tsankho molingana ndi zochita zake, pa nthawi imene muli alendo pa dziko lapansi khalani moopa Mulungu. 18Pakuti mukudziwa kuti simunawomboledwe ndi zinthu zimene zimawonongeka monga siliva kapena golide, kuchoka ku khalidwe lanu lachabe limene munalandira kwa makolo anu. 19Koma munawomboledwa ndi magazi a mtengowapatali a Khristu, Mwana Wankhosa wopanda banga kapena chilema. 20Iye anasankhidwa lisanalengedwe dziko lapansi, koma waonetsedwa chifukwa cha inu pa nthawi ino yotsiriza. 21Kudzera mwa Iye mumakhulupirira Mulungu, amene anamuukitsa kwa akufa namupatsa ulemerero. Nʼchifukwa chake chikhulupiriro ndi chiyembekezo chanu chili mwa Mulungu.

22Tsopano mwayeretsa mitima yanu pomvera choonadi, kuti muzikondana ndi abale anu, kukondana kwenikweni kochokera pansi pa mtima. 23Popeza mwabadwanso, osati ndi mbewu imene imawonongeka, koma imene siwonongeka, ndiye kuti ndi Mawu a Mulungu amoyo ndi okhalitsa. 24Pakuti,

“Anthu onse ali ngati udzu,

ndipo ulemerero wawo uli ngati duwa la kuthengo.

Udzu umafota ndipo duwa limathothoka,

25koma mawu a Ambuye adzakhala mpaka muyaya.”

Ndipo awa ndi mawu amene tinalalikira kwa inu.