1 Chronicles 6 – KJV & CCL

King James Version

1 Chronicles 6:1-81

1The sons of Levi; Gershon, Kohath, and Merari.6.1 Gershon: or, Gershom 2And the sons of Kohath; Amram, Izhar, and Hebron, and Uzziel. 3And the children of Amram; Aaron, and Moses, and Miriam. The sons also of Aaron; Nadab, and Abihu, Eleazar, and Ithamar.

4¶ Eleazar begat Phinehas, Phinehas begat Abishua, 5And Abishua begat Bukki, and Bukki begat Uzzi, 6And Uzzi begat Zerahiah, and Zerahiah begat Meraioth, 7Meraioth begat Amariah, and Amariah begat Ahitub, 8And Ahitub begat Zadok, and Zadok begat Ahimaaz, 9And Ahimaaz begat Azariah, and Azariah begat Johanan, 10And Johanan begat Azariah, (he it is that executed the priest’s office in the temple that Solomon built in Jerusalem:)6.10 in the temple: Heb. in the house 11And Azariah begat Amariah, and Amariah begat Ahitub, 12And Ahitub begat Zadok, and Zadok begat Shallum,6.12 Shallum: or, Meshullam 13And Shallum begat Hilkiah, and Hilkiah begat Azariah, 14And Azariah begat Seraiah, and Seraiah begat Jehozadak, 15And Jehozadak went into captivity, when the LORD carried away Judah and Jerusalem by the hand of Nebuchadnezzar.

16¶ The sons of Levi; Gershom, Kohath, and Merari.6.16 Gershom: or, Gershon 17And these be the names of the sons of Gershom; Libni, and Shimei. 18And the sons of Kohath were, Amram, and Izhar, and Hebron, and Uzziel. 19The sons of Merari; Mahli, and Mushi. And these are the families of the Levites according to their fathers. 20Of Gershom; Libni his son, Jahath his son, Zimmah his son, 21Joah his son, Iddo his son, Zerah his son, Jeaterai his son.6.21 Joah: or, Ethan6.21 Iddo: or, Adaiah6.21 Jeaterai: also called, Ethni 22The sons of Kohath; Amminadab his son, Korah his son, Assir his son,6.22 Amminadab: or, Izhar 23Elkanah his son, and Ebiasaph his son, and Assir his son, 24Tahath his son, Uriel his son, Uzziah his son, and Shaul his son. 25And the sons of Elkanah; Amasai, and Ahimoth. 26As for Elkanah: the sons of Elkanah; Zophai his son, and Nahath his son,6.26 Zophai: or, Zuph 27Eliab his son, Jeroham his son, Elkanah his son. 28And the sons of Samuel; the firstborn Vashni, and Abiah.6.28 Vashni: called also Joel 29The sons of Merari; Mahli, Libni his son, Shimei his son, Uzza his son, 30Shimea his son, Haggiah his son, Asaiah his son.

31And these are they whom David set over the service of song in the house of the LORD, after that the ark had rest. 32And they ministered before the dwelling place of the tabernacle of the congregation with singing, until Solomon had built the house of the LORD in Jerusalem: and then they waited on their office according to their order. 33And these are they that waited with their children. Of the sons of the Kohathites: Heman a singer, the son of Joel, the son of Shemuel,6.33 waited: Heb. stood 34The son of Elkanah, the son of Jeroham, the son of Eliel, the son of Toah, 35The son of Zuph, the son of Elkanah, the son of Mahath, the son of Amasai, 36The son of Elkanah, the son of Joel, the son of Azariah, the son of Zephaniah, 37The son of Tahath, the son of Assir, the son of Ebiasaph, the son of Korah, 38The son of Izhar, the son of Kohath, the son of Levi, the son of Israel. 39And his brother Asaph, who stood on his right hand, even Asaph the son of Berachiah, the son of Shimea, 40The son of Michael, the son of Baaseiah, the son of Malchiah, 41The son of Ethni, the son of Zerah, the son of Adaiah, 42The son of Ethan, the son of Zimmah, the son of Shimei, 43The son of Jahath, the son of Gershom, the son of Levi. 44And their brethren the sons of Merari stood on the left hand: Ethan the son of Kishi, the son of Abdi, the son of Malluch,6.44 Kishi: or, Kushaiah 45The son of Hashabiah, the son of Amaziah, the son of Hilkiah, 46The son of Amzi, the son of Bani, the son of Shamer, 47The son of Mahli, the son of Mushi, the son of Merari, the son of Levi. 48Their brethren also the Levites were appointed unto all manner of service of the tabernacle of the house of God.

49¶ But Aaron and his sons offered upon the altar of the burnt offering, and on the altar of incense, and were appointed for all the work of the place most holy, and to make an atonement for Israel, according to all that Moses the servant of God had commanded. 50And these are the sons of Aaron; Eleazar his son, Phinehas his son, Abishua his son, 51Bukki his son, Uzzi his son, Zerahiah his son, 52Meraioth his son, Amariah his son, Ahitub his son, 53Zadok his son, Ahimaaz his son.

54¶ Now these are their dwelling places throughout their castles in their coasts, of the sons of Aaron, of the families of the Kohathites: for theirs was the lot. 55And they gave them Hebron in the land of Judah, and the suburbs thereof round about it. 56But the fields of the city, and the villages thereof, they gave to Caleb the son of Jephunneh. 57And to the sons of Aaron they gave the cities of Judah, namely, Hebron, the city of refuge, and Libnah with her suburbs, and Jattir, and Eshtemoa, with their suburbs, 58And Hilen with her suburbs, Debir with her suburbs,6.58 Hilen: or, Holon 59And Ashan with her suburbs, and Beth-shemesh with her suburbs:6.59 Ashan: or, Ain 60And out of the tribe of Benjamin; Geba with her suburbs, and Alemeth with her suburbs, and Anathoth with her suburbs. All their cities throughout their families were thirteen cities.6.60 Alemeth: or, Almon 61And unto the sons of Kohath, which were left of the family of that tribe, were cities given out of the half tribe, namely, out of the half tribe of Manasseh, by lot, ten cities. 62And to the sons of Gershom throughout their families out of the tribe of Issachar, and out of the tribe of Asher, and out of the tribe of Naphtali, and out of the tribe of Manasseh in Bashan, thirteen cities. 63Unto the sons of Merari were given by lot, throughout their families, out of the tribe of Reuben, and out of the tribe of Gad, and out of the tribe of Zebulun, twelve cities. 64And the children of Israel gave to the Levites these cities with their suburbs. 65And they gave by lot out of the tribe of the children of Judah, and out of the tribe of the children of Simeon, and out of the tribe of the children of Benjamin, these cities, which are called by their names. 66And the residue of the families of the sons of Kohath had cities of their coasts out of the tribe of Ephraim. 67And they gave unto them, of the cities of refuge, Shechem in mount Ephraim with her suburbs; they gave also Gezer with her suburbs, 68And Jokmeam with her suburbs, and Beth-horon with her suburbs, 69And Aijalon with her suburbs, and Gath-rimmon with her suburbs: 70And out of the half tribe of Manasseh; Aner with her suburbs, and Bileam with her suburbs, for the family of the remnant of the sons of Kohath. 71Unto the sons of Gershom were given out of the family of the half tribe of Manasseh, Golan in Bashan with her suburbs, and Ashtaroth with her suburbs: 72And out of the tribe of Issachar; Kedesh with her suburbs, Daberath with her suburbs, 73And Ramoth with her suburbs, and Anem with her suburbs: 74And out of the tribe of Asher; Mashal with her suburbs, and Abdon with her suburbs, 75And Hukok with her suburbs, and Rehob with her suburbs: 76And out of the tribe of Naphtali; Kedesh in Galilee with her suburbs, and Hammon with her suburbs, and Kirjathaim with her suburbs. 77Unto the rest of the children of Merari were given out of the tribe of Zebulun, Rimmon with her suburbs, Tabor with her suburbs: 78And on the other side Jordan by Jericho, on the east side of Jordan, were given them out of the tribe of Reuben, Bezer in the wilderness with her suburbs, and Jahzah with her suburbs, 79Kedemoth also with her suburbs, and Mephaath with her suburbs: 80And out of the tribe of Gad; Ramoth in Gilead with her suburbs, and Mahanaim with her suburbs, 81And Heshbon with her suburbs, and Jazer with her suburbs.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 6:1-81

Fuko la Levi

1Ana a Levi anali awa:

Geresoni, Kohati ndi Merari.

2Ana a Kohati anali awa:

Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli.

3Ana a Amramu anali awa:

Aaroni, Mose ndi Miriamu.

Ana a Aaroni anali awa:

Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara

4Eliezara anabereka Finehasi,

Finehasi anabereka Abisuwa,

5Abisuwa anabereka Buki,

Buki anabereka Uzi.

6Uzi anabereka Zerahiya,

Zerahiya anabereka Merayoti,

7Merayoti anabereka Amariya,

Amariya anabereka Ahitubi.

8Ahitubi anabereka Zadoki,

Zadoki anabereka Ahimaazi.

9Ahimaazi anabereka Azariya,

Azariya anabereka Yohanani,

10Yohanani anabereka Azariya (uyu ndi amene anatumikira monga wansembe mʼNyumba ya Mulungu imene Solomoni anamanga mu Yerusalemu),

11Azariya anabereka Amariya,

Amariya anabereka Ahitubi,

12Ahitubi anabereka Zadoki,

Zadoki anabereka Salumu,

13Salumu anabereka Hilikiya,

Hilikiya anabereka Azariya,

14Azariya anabereka Seraya,

ndipo Seraya anabereka Yehozadaki.

15Yehozadaki anagwidwa ukapolo pamene Yehova analola Nebukadinezara kuti agwire ukapolo Yuda ndi Yerusalemu.

16Ana a Levi anali awa:

Geresomu, Kohati ndi Merari.

17Mayina a ana a Geresomu ndi awa:

Libini ndi Simei.

18Ana a Kohati anali awa:

Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli.

19Ana a Merari anali awa:

Mahili ndi Musi.

Mayina a mabanja a fuko la Levi olembedwa potsata makolo awo ndi awa:

20Ana a Geresomu ndi awa:

Libini, Yehati,

Zima, 21Yowa,

Ido, Zera

ndi Yeaterai.

22Zidzukulu za Kohati ndi izi:

Aminadabu, Kora,

Asiri, 23Elikana,

Ebiyasafu, Asiri,

24Tahati, Urieli,

Uziya ndi Sauli.

25Zidzukulu za Elikana ndi izi:

Amasai, Ahimoti,

26Elikana, Zofai,

Nahati, 27Eliabu,

Yerohamu, Elikana

ndi Samueli.

28Ana a Samueli ndi awa:

Mwana wake woyamba anali Yoweli,

wachiwiri anali Abiya.

29Zidzukulu za Merari ndi izi:

Mahili, Libini,

Simei, Uza,

30Simea, Hagiya

ndi Asaya.

Oyimba mʼNyumba ya Mulungu

31Awa ndi anthu amene Davide anawayika kuti aziyangʼanira mayimbidwe mʼNyumba ya Yehova, Bokosi la Chipangano litabwera kudzakhala mʼmenemo. 32Iwo ankatumikira akuyimba nyimbo pa khomo la malo opatulika, tenti ya msonkhano, mpaka Solomoni atamanga Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu. Iwo ankagwira ntchito zawo potsata malamulo amene anawapatsa.

33Mayina a anthuwo, pamodzi ndi ana awo, anali awa:

Ochokera ku banja la Kohati:

Hemani, katswiri woyimba,

anali mwana wa Yoweli, mwana wa Samueli,

34mwana wa Elikana, mwana wa Yerohamu,

mwana wa Elieli, mwana wa Towa,

35mwana wa Zufi, mwana wa Elikana,

mwana wa Mahati, mwana wa Amasai,

36mwana wa Elikana, mwana wa Yoweli,

mwana wa Azariya, mwana wa Zefaniya,

37mwana wa Tahati, mwana wa Asiri,

mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora,

38mwana wa Izihari, mwana wa Kohati,

mwana wa Levi, mwana wa Israeli;

39ndi Asafu mʼbale wake, amene ankatumikira ku dzanja lake lamanja:

Asafu anali mwana wa Berekiya, mwana wa Simea,

40mwana wa Mikayeli, mwana wa Baaseya,

mwana wa Malikiya, 41mwana wa Etini,

mwana wa Zera, mwana wa Adaya,

42mwana wa Etani, mwana wa Zima,

mwana Simei, 43mwana wa Yahati,

mwana wa Geresomu, mwana wa Levi;

44ndipo abale awo ena anali a banja la Merari amene amatumikira ku dzanja lake lamanzere:

Etani anali mwana wa Kisi, mwana wa Abidi,

mwana wa Maluki, 45mwana wa Hasabiya,

mwana wa Amaziya, mwana wa Hilikiya,

46mwana wa Amizi, mwana wa Bani,

mwana wa Semeri, 47mwana wa Mahili,

mwana wa Musi, mwana wa Merari,

mwana wa Levi.

48Abale awo Alevi anapatsidwa ntchito zina zonse ku malo opatulika ku nyumba ya Mulungu. 49Koma Aaroni ndi zidzukulu zake anali amene amapereka nsembe pa guwa lansembe zopsereza ndi pa guwa lansembe zofukiza pamodzi ndi zonse zimene zimachitika ku malo opatulika kwambiri, kuchita mwambo wopepesera Israeli, potsata zonse zimene Mose mtumiki wa Mulungu anawalamulira.

50Ana a Aaroni ndi zidzukulu zake anali awa:

Eliezara, Finehasi,

Abisuwa, 51Buki,

Uzi, Zerahiya,

52Merayoti, Amariya,

Ahitubi, 53Zadoki

ndi Ahimaazi.

54Malo amene iwo anapatsidwa kuti likhale dziko lawo ndi awa: (Malowa anapatsidwa kwa zidzukulu za Aaroni zimene zinali za banja la Kohati, chifukwa malo oyamba kugawidwa anali awo).

55Iwo anapatsidwa Hebroni mʼdziko la Yuda ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa. 56Koma minda ndi midzi yozungulira mzindawo zinapatsidwa kwa Kalebe mwana wa Yefune.

57Kotero zidzukulu za Aaroni zinapatsidwa Hebroni (mzinda wopulumukirako), ndi Libina, Yatiri, Esitemowa, 58Hileni, Debri, 59Asani, Yuta ndi Beti-Semesi pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa. 60Ndipo ku fuko la Benjamini anapatsidwa Gibiyoni, Geba, Alemeti ndi Anatoti, pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa.

Mizinda imene anapatsidwa ku banja la Kohati onse pamodzi inalipo 13.

61Zidzukulu zotsala za Kohati anazigawira midzi khumi kuchokera ku mabanja a fuko la theka la Manase.

62Zidzukulu za Geresomu banja ndi banja zinapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mafuko a Isakara, Aseri ndi Nafutali, ndi gawo lina la fuko la Manase limene lili ku Basani.

63Zidzukulu za Merari banja ndi banja zinapatsidwa mizinda khumi ndi iwiri kuchokera ku mafuko a Rubeni, Gadi ndi Zebuloni.

64Kotero Aisraeli anapatsa Alevi mizindayi ndi madera a msipu ozungulira malowa. 65Kuchokera ku mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini anawapatsa mizinda imene inawatchula kale mayina.

66Mabanja ena a Kohati anapatsidwanso malo kuchokera ku fuko la Efereimu.

67Kuchokera ku dziko lamapiri la Efereimu anapatsidwa Sekemu (mzinda wopulumukirako) ndi Gezeri, 68Yokineamu, Beti-Horoni, 69Ayaloni ndi Gati-Rimoni, pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira.

70Ndipo kuchokera ku theka la fuko la Manase, Aisraeli anapereka Aneri ndi Bileamu pamodzi ndi madera odyetsera ziweto kwa mabanja ena onse a Kohati.

71Ageresomu analandira malo awa:

Kuchokera ku theka la fuko la Manase,

analandira Golani ku Basani ndiponso Asiteroti, ndi malo awo odyetsera ziweto;

72Kuchokera ku fuko la Isakara

analandira Kedesi, Daberati, 73Ramoti ndi Anemu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;

74kuchokera ku fuko la Aseri

analandira Masala, Abidoni, 75Hukoki ndi Rehobu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;

76ndipo kuchokera ku fuko la Nafutali

analandira Kedesi ku Galileya, Hamoni ndi Kiriyataimu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto.

77Amerari (Alevi ena onse) analandira madera awa:

kuchokera ku fuko la Zebuloni,

iwo analandira Yokineamu, Karita, Rimono ndi Tabori, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;

78Kuchokera ku fuko la Rubeni kutsidya kwa Yorodani, kummawa kwa Yeriko,

analandira Bezeri ku chipululu, Yaza, 79Kedemoti ndi Mefaati, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto;

80ndipo kuchokera ku fuko la Gadi

analandira Ramoti ku Giliyadi, Mahanaimu, 81Hesiboni ndi Yazeri, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto.