詩篇 5 – JCB & CCL

Japanese Contemporary Bible

詩篇 5:1-12

5

1-2ああ主よ、この祈りを聞いてください。

王なる神よ、私の嘆きに耳を傾けてください。

私はあなた以外のだれにも、決して祈ったりしません。

3朝ごとに、天におられるあなたを見上げ、

御前に願い事を申し上げ、ひたすら祈ります。

4あなたは、どんな小さな悪も喜んだりなさらず、

ささいな罪でも大目に見たりはなさいません。

5ですから、おごり高ぶる罪人たちは、

あなたの鋭い視線を逃れて

罪を知られないままでいることはできません。

あなたは悪事を徹底的に憎まれるからです。

6うそはあばかれ、彼らは滅ぼされます。

主は、殺人と欺きを

どんなにお嫌いになることでしょう。

7しかしこの私は、

あわれみと愛に守られて、神殿へまいります。

心の底から恐れかしこんで神を礼拝します。

8主よ、お約束のとおり、私を導いてください。

そうでなければ、敵に踏みにじられてしまいます。

何をすればよいのか、どちらへ進むべきか、

はっきりとお教えください。

9彼らはうそばかりつき、心は悪い思いで満ちています。

彼らの誘いには罪と死の悪臭がただよいます。

彼らは甘いことばで人々を欺き、

邪悪な目的をはたそうとしています。

10ああ神よ、彼らに責任をとらせてください。

自分でしかけた罠にかからせてください。

自らの罪の重みに耐えかねて、

その下敷きになりますように。

彼らは神に背いたのですから。

11しかし、すべて神を信頼する者には、

喜びを与えてください。

神がかばってくださることを知って、

彼らがいつまでも喜びの声を上げますように。

神を愛する人たちを、幸福にひたらせてください。

12神は心から信じる者を祝福されます。

主よ、あなたは愛の盾で彼らを囲まれます。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 5:1-12

Salimo 5

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe zoyimbira za zitoliro. Salimo la Davide.

1Tcherani khutu ku mawu anga, Inu Yehova,

ganizirani za kusisima kwanga

2Mverani kulira kwanga kofuna thandizo,

Mfumu yanga ndi Mulungu wanga,

pakuti kwa Inu, ine ndikupemphera.

3Mmawa, Yehova mumamva mawu anga;

Mmawa ndimayala zopempha zanga pamaso panu

ndi kudikira mwachiyembekezo.

4Inu si Mulungu amene mumasangalala ndi zoyipa;

choyipa sichikhala pamaso panu.

5Onyada sangathe kuyima pamaso panu;

Inu mumadana ndi onse ochita zoyipa.

6Mumawononga iwo amene amanena mabodza;

anthu akupha ndi achinyengo,

Yehova amanyansidwa nawo.

7Koma Ine, mwa chifundo chanu chachikulu,

ndidzalowa mʼNyumba yanu;

mwa ulemu ndidzaweramira pansi

kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera.

8Tsogolereni Inu Yehova, mwa chilungamo chanu

chifukwa cha adani anga ndipo

wongolani njira yanu pamaso panga.

9Palibe mawu ochokera mʼkamwa mwawo amene angadalirike;

mtima wawo wadzaza ndi chiwonongeko.

Kummero kwawo kuli ngati manda apululu;

ndi lilime lawo amayankhula zachinyengo.

10Lengezani kuti ndi olakwa, Inu Mulungu!

Zochita zawo zoyipa zikhale kugwa kwawo.

Achotseni pamaso panu chifukwa cha machimo awo ambiri,

pakuti awukira Inu.

11Koma lolani kuti onse amene apeza chitetezo mwa Inu akondwere;

lolani kuti aziyimba nthawi zonse chifukwa cha chimwemwe.

Aphimbeni ndi chitetezo chanu,

iwo amene amakonda dzina lanu akondwere mwa Inu.

12Ndithu, Inu Yehova, mumadalitsa olungama;

mumawazungulira ndi kukoma mtima kwanu ngati chishango.