Ezechiël 8 – HTB & CCL

Het Boek

Ezechiël 8:1-18

De zonden van de Israëlieten

1Op de vijfde dag van de zesde maand in het zesde jaar van koning Jojakins gevangenschap, kwam de kracht van de Oppermachtige Here over mij, terwijl ik in mijn huis met de leiders van Juda zat te praten. 2En ik zag een gedaante als van vuur, vanaf zijn middel naar beneden leek hij te bestaan uit vuur en zijn bovenlichaam glansde en schitterde als wit goud. 3De gedaante stak iets uit dat op een hand leek en pakte mij bij mijn haren. En de Geest tilde mij op in de lucht en bracht mij in dit visioen naar Jeruzalem, naar de ingang van de noordelijke poort waar het grote afgodsbeeld stond dat zoveel ergernis opwekt.

4Plotseling verscheen de heerlijkheid van de God van Israël, net zoals ik eerder had gezien in het dal. 5Hij zei tegen mij: ‘Mensenzoon, kijk naar het noorden.’ Ik zag ten noorden van de poort bij het altaar het afgodsbeeld staan. 6Hij zei: ‘Mensenzoon, ziet u wat zij doen? Ziet u welke grote zonden de Israëlieten hier begaan, zodat Ik uit mijn tempel word verdreven? Maar kom, Ik zal u nog grotere zonden laten zien!’ 7Hij bracht mij naar de toegangsdeur van de tempelhof, waar ik een gat in de muur ontdekte. 8‘Breek door deze muur heen,’ zei Hij. Toen ik dat deed, kwam een deur naar een verborgen kamer tevoorschijn. 9‘Ga naar binnen,’ zei Hij, ‘en kijk welke goddeloosheid daar wordt bedreven.’

10Ik ging naar binnen. De muren waren versierd met afbeeldingen van allerlei slangen, hagedissen en andere weerzinwekkende dieren. Ook waren er afbeeldingen van alle afgoden die de Israëlieten vereerden. 11En zeventig leiders van Israël stonden daar in het gezelschap van Safans zoon Jaäzanja en aanbaden de afbeeldingen. Ieder van hen had een wierookvat in de hand en de rook vulde de hele kamer. 12Toen zei de Here tegen mij: ‘Mensenzoon, hebt u gezien wat de leiders van Israël in het geheim doen, ieder bij zijn afgodsbeeld? Zij zeggen: “De Here ziet ons toch niet, want Hij heeft het land verlaten”.’ 13Hij vervolgde: ‘Kom, dan zal Ik u zonden laten zien die nog gruwelijker zijn dan deze!’

14Hij bracht mij naar de noordelijke tempelpoort en daar zaten vrouwen te huilen om hun god Tammuz. 15‘Hebt u dit gezien?’ vroeg Hij. ‘Maar Ik zal u nog grotere gruwelen laten zien.’

16Toen bracht Hij mij in de binnenste tempelhof en daar bij de deur, tussen de voorhal en het koperen altaar, stonden ongeveer vijfentwintig mannen met hun rug naar de tempel van de Here en met hun gezicht naar het oosten gekeerd de zon te aanbidden! 17‘Hebt u het gezien?’ vroeg Hij. ‘Doet het de inwoners van Juda dan helemaal niets dat zij deze gruwelijke zonden bedrijven en het hele land vullen met onrecht? Zij steken hun tong tegen Mij uit en wakkeren zo mijn toorn aan. 18Daarom zal Ik hun in mijn toorn meedogenloos straffen zonder iemand te sparen. En ook al schreeuwen zij om genade, Ik zal niet luisteren.’

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 8:1-18

Kupembedza Mafano Mʼnyumba ya Mulungu

1Tsiku lachisanu la mwezi wachisanu ndi chimodzi, mʼchaka chachisanu ndi chimodzi, ndinakhala mʼnyumba mwanga pamodzi ndi akuluakulu a ku Yuda. Tsono mphamvu za Ambuye Yehova zinandifikira. 2Nditayangʼana ndinangoona chinthu chooneka ngati munthu. Kuchokera pamene pamaoneka ngati chiwuno chake kumatsika mʼmunsi anali ngati moto, ndipo kuchokera mʼchiwuno kukwera mmwamba amaoneka mowala ngati mkuwa wonyezimira. 3Iye anatambasula chinthu chooneka ngati dzanja ndipo anagwira tsitsi la pamutu panga. Nthawi yomweyo Mzimu unandikweza mlengalenga. Tsono ndikumachita ngati ndikuona Mulungu kutulo, Mzimu uja unapita nane ku Yerusalemu nundiyika pa khomo la chipata chamʼkati choyangʼana kumpoto. Kumeneko kunali fano limene limaputa mkwiyo wa Mulungu. 4Kumeneko ndinaona ulemerero wa Mulungu wa Israeli ngati momwe ndinaonera mʼmasomphenya mʼchigwa muja.

5Tsono Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tayangʼana kumpoto.” Choncho ndinayangʼana kumpoto ndipo ndinaona pa khomo la chipata pafupi ndi guwa lansembe ndinaona fano loputa mkwiyo wa Mulungu lija.

6Ndipo Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuona zimene akuchitazi, zonyansa zazikulu zimene Aisraeli akuchita kuno, zinthu zondichotsa Ine kumalo anga opatulika? Koma iwe udzaona zinthu zimene zili zonyansa kwambiri.”

7Kenaka Iye anandipititsa ku khomo lolowera ku bwalo la Nyumba ya Mulungu. Nditayangʼanitsitsa ndinangoona dzenje pa khomapo. 8Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tsopano bowola pa khomapo.” Ndinabowoladi pa khomapo ndipo ndinapezapo khomo.

9Ndipo Yehova anandiwuza kuti, “Lowa, ndipo ona zinthu zonyansa zimene akuchita pamenepa.” 10Motero Ine ndinalowa ndi kuyangʼana, ndipo ndinaona pa makoma onse zithunzi za zinthu zosiyanasiyana zokwawa pansi, za nyama zonyansa ndiponso za mafano onse amene Aisraeli ankapembedza. 11Patsogolo pa zimenezi panayima akuluakulu makumi asanu ndi awiri a Aisraeli, ndipo Yaazaniya mwana wa Safani anali atayima pakati pawo. Aliyense wa iwo anali ndi chofukizira lubani mʼdzanja lake ndipo utsi wa fungo lokoma la lubani unkafuka.

12Tsono Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimene akuluakulu a Aisraeli akuchita mu mdima, aliyense akupembedza fano lakelake mʼnyumbamo? Iwo akuti, ‘Yehova sakutiona; Yehova walisiya dziko!’ 13Iye anandiwuzanso kuti, ‘Iwe udzawaonanso akuchita zinthu zonyansa kwambiri.’ ”

14Kenaka anapita nane pa khomo la ku khomo la chipata cha Nyumba ya Mulungu choyangʼana kumpoto, ndipo kumeneko ndinaona akazi ena atakhala pansi, akulira mulungu wawo wotchedwa Tamuzi. 15Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziona zimenezi? Iwe udzaona zinthu zimene zili zonyansa kwambiri kuposa izi.”

16Kenaka Iye anapita nane mʼkati mwa bwalo la Nyumba ya Yehova. Kumeneko ku khomo lolowera ku Nyumba ya Yehova pakati pa khonde ndi guwa lansembe, panali amuna 25. Anafulatira Nyumba ya Mulungu wa Yehova ndipo nkhope zawo zinaloza kummawa, ndipo ankapembedza dzuwa choyangʼana kummawa.

17Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi waziona zimenezi? Kodi nʼchinthu chopepuka kuti anthu a ku Yuda azichita zonyansa zimene akuchitazi pano? Kodi afike mpaka pomafalitsa za ndewu mʼdziko lonse? Iwotu akuwutsa ukali wanga. Akundipsetsa mtima ndi zochita zawo! 18Choncho Ine ndidzawalanga ndili wokwiya. Sindidzawamvera chisoni kapena kuwaleka. Ngakhale atandifuwulira mʼmakutu mwanga sindidzawamvera.”