2 Kronieken 4 – HTB & CCL

Het Boek

2 Kronieken 4:1-22

Churam, een vakman voor God

1Verder maakte hij een koperen altaar van negen meter in het vierkant en een hoogte van 4,5 meter. 2Daarna goot hij een koperen bassin met een doorsnede van 4,5 meter. De rand van dit bassin was ruim 2,25 meter hoog en had een lengte van 13,5 meter. 3Twee rijen koperen runderen ondersteunden dit bassin en ze vormden samen één gegoten geheel. 4Deze runderen, twaalf in getal, stonden met de staarten naar elkaar toe. Drie keken naar het noorden, drie naar het westen, drie naar het zuiden en drie naar het oosten. 5De wanden van het bassin waren acht centimeter dik en bogen naar buiten als de rand van een beker of als bij een lelie. De inhoud bedroeg vierenveertigduizend liter water.

6Hij maakte ook tien vaten voor het water waarmee alles voor de offerdienst moest worden gewassen. Vijf stonden aan de linkerkant van het vertrek en vijf aan de rechterkant. De priesters gebruikten het grote bassin om zichzelf in te wassen. 7Verder maakte hij tien gouden kandelaars en gaf ze een plaats in de tempel, vijf aan elke kant. 8Tevens maakte hij tien tafels en zette er vijf tegen de muur aan de linkerkant en vijf tegen die aan de rechterkant. Ook maakte hij honderd massief gouden offerschalen. 9Daarna bouwde hij een voorhof voor de priesters en een voorhof voor het publiek. De toegangsdeuren en scharnieren van beide hoven overtrok hij met koper. 10Het grote bassin stond in de zuidoostelijke hoek van het buitenvertrek van de tempel.

11Churam maakte tevens de potten, scheppen en offerschalen die bij het offeren werden gebruikt. Zo voltooide hij de taak die koning Salomo hem had opgedragen: 12-16het maken van de twee pilaren, de twee bolvormige kapitelen bovenop de pilaren, de twee gevlochten slingers op de kapitelen, de rijen granaatappels die aan de slingers op de kapitelen hingen, de voetstukken voor de vaten en de vaten zelf, het grote bassin en de runderen die deze ondersteunden, de potten, scheppen en vleeshaken. Deze ervaren vakman, Churam, maakte alle bovengenoemde voorwerpen voor koning Salomo. Als materiaal gebruikte hij gepolijst koper. 17-18 De koning liet het gietwerk maken op de kleibanken in het Jordaandal tussen Sukkot en Zeredatha. Er werden grote hoeveelheden koper gebruikt, te veel om te kunnen wegen.

19Ook liet Salomo alle voorwerpen maken die in de tempel thuishoren: het gouden altaar en de tafel voor de toonbroden. 20Hetzelfde gold voor de gouden kandelaars en de lampen, die volgens de regels vóór de achterzaal werden aangestoken, 21de bloemdecoraties 22de snuiters, lepels, offerschalen, schotels en vuurpannen, alles werd van puur goud gemaakt. Zelfs de deuren van de tempel waren van goud, zowel de deuren van de ingang van het Heilige der Heiligen als van de ingang van de grote zaal.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 4:1-22

Zipangizo za mʼNyumba ya Mulungu

1Solomoni anapanga guwa lamkuwa limene mulitali mwake linali mamita asanu ndi anayi, mulifupi mwakenso mamita asanu ndi anayi ndipo msinkhu wake unali mamita anayi ndi theka. 2Kenaka iye anapanga mbiya yayikulu yachitsulo. Inali yozungulira ndipo pakamwa pake panali pa mamita anayi ndi theka, poyeza modutsa pakati pake. Msinkhu wake unali wopitirirapo mamita awiri. Thunthu lake linali mamita 13. 3Mʼmunsi mwa mkombero wa mbiyayo anajambulamo zithunzi zangʼombe zazimuna mozungulira, zithunzi khumi pa theka la mita. Ngʼombezo zimajambulidwa mʼmizere iwiri ndipo anazipangira kumodzi ndi mbiyayo.

4Mbiyayo anayisanjika pa ngʼombe zamkuwa khumi ndi ziwiri, zitatu zoyangʼana kumpoto, zitatu zoyangʼana kumadzulo, zitatu zoyangʼana kummwera ndipo zitatu zoyangʼana kummawa. Mbiyayo inakhazikika pamwamba pa ngʼombezo, ndipo miyendo yake yonse yakumbuyo ya ngʼombezo inkaloza mʼkati. 5Mbiyayo inali yochindikala ngati chikhatho ndipo mkombero wake unali ngati mkombero wa chikho, ngati duwa lokongola kwambiri. Mʼmbiyamo munkalowa madzi okwana malita 60,000.

6Kenaka anapanga mabeseni khumi otsukira zinthu ndipo asanu amawayika mbali ya kummwera, asanu mbali ya kumpoto. Mʼmenemo amatsukiramo zinthu zimene zimagwiritsidwa ntchito pa nsembe zopsereza koma mbiyamo ndi mʼmene ankasambiramo ansembe.

7Solomoni anapanga zoyikapo nyale khumi zagolide monga momwe kunalembedwera ndipo anaziyika mʼNyumba ya Mulungu, zisanu mbali ya kummwera, ndi zisanu mbali ya kumpoto.

8Iye anapanga matebulo khumi ndipo anawayika mʼNyumba ya Mulungu, asanu mbali ya kummwera ndi asanu mbali ya kumpoto. Iye anapanganso mabeseni agolide okwanira 100.

9Iye anapanga bwalo la ansembe, bwalo lalikulu ndi zitseko za bwalolo ndipo anakuta zitsekozo ndi mkuwa. 10Anayika mbiya ija mbali yakummwera pamene mbali ya kummawa ndi kummwera zimakumana.

11Iye anapanganso miphika ndi mafosholo ndi mabeseni owazira magazi.

Kotero Hiramu anatsiriza ntchito yonse ya ku Nyumba ya Mulungu imene ankagwirira Mfumu Solomoni:

12Nsanamira ziwiri;

mbale ziwiri za mitu yapamwamba pa nsanamirazo;

maukonde awiri okongoletsera mbale ziwiri za mitu yapamwamba pa nsanamirazo;

13makangadza 400 a maukonde awiri okongoletserawo (mizere iwiri ya makangadza pa ukonde uliwonse, kukongoletsa mbale za mitu yapamwamba pa nsanamira);

14miyendo pamodzi ndi mabeseni ake;

15mbiya pamodzi ndi ngʼombe khumi ndi ziwiri zazimuna zosanjikapo mbiyayo.

16Miphika, mafosholo, mafoloko otengera nyama ndi ziwiya zina zonse.

Zipangizo zonse zimene Hiramu Abi anapangira Mfumu Solomoni za mʼNyumba ya Yehova zinali zamkuwa wonyezimira. 17Mfumu inapangitsa zimenezi mʼchigwa cha Yorodani, ku malo amtapo amene anali pakati pa Sukoti ndi Zaretani. 18Zinthu zonse zimene Solomoni anapanga zinali zochuluka kwambiri kotero kuti kulemera kwa mkuwa sikunadziwike.

19Solomoni anapanganso ziwiya zonse zimene zinali mʼNyumba ya Mulungu:

guwa lansembe lagolide;

matebulo pamene ankayikapo buledi woperekedwa kwa Mulungu;

20zoyikapo nyale zagolide ndi nyale zake zagolide weniweni, kuti ziziyaka mʼkati mwenimweni mwa malo opatulika monga analembera,

21maluwa agolide, nyale ndi mbaniro. (Zinali zagolide mmodzi);

22zozimitsira nyale zagolide weniweni, mbale zowazira magazi, mbale ndi zofukizira; ndiponso zitseko zagolide za Nyumba ya Mulungu, chitseko cha ku Malo Opatulika Kwambiri ndi zitseko za ku chipinda chachikulu.