Luka 19 – CRO & CCL

Knijga O Kristu

Luka 19:1-48

Isus i Zakej

1Isus uđe u Jerihon. Dok je prolazio gradom, 2dođe čovjek imenom Zakej, utjecajan Židov koji je radio za rimsku poreznu upravu i vrlo se obogatio. 3Želio je vidjeti Isusa, ali je bio prenizak rastom da bi ga mogao vidjeti preko mnoštva. 4On zato potrči naprijed te se popne na smokvu pokraj koje je Isus trebao proći da s nje promatra.

5Kad je Isus stigao do njega, pogleda gore i reče mu: “Zakeju, brzo siđi! Danas moram k tebi u goste.”

6Zakej žurno siđe s drveta i primi ga u goste sav radostan. 7Ali mnoštvo koje je to promatralo počne prigovarati: “Otišao je takvom grešniku u goste!”

8A Zakej ustane i reče Gospodinu: “Gospodine, polovicu svojega imanja dat ću siromasima, a svakome koga sam prevario četverostruko ću vratiti.”

9“Danas je u ovu kuću došlo spasenje jer je i ovaj čovjek Abrahamov sin! 10Ja, Sin Čovječji, došao sam tražiti i spasiti izgubljene.”

Prispodoba o desetorici slugu

(Mt 25:14-30)

11Mnoštvo je sve to slušalo. Kako je već bio nadomak Jeruzalemu, mislili su da će se kraljevstvo Božje odmah pojaviti. Isus im zato ispriča prispodobu: 12“Neki je ugledan čovjek trebao otputovati u daleku zemlju da ga ondje okrune za kralja, a zatim se vratiti. 13Pozove zato desetoricu svojih slugu, dade svakomu pola kilograma srebra19:13 U grčkome: 10 mina (svakome jednu minu, što je u to doba iznosilo otprilike tri mjesečne plaće). te im reče: ‘Trgujte s njime dok ne dođem.’ 14Ali njegovi su ga građani mrzili i poslali su za njim poslanike s porukom: ‘Ne želimo da on kraljuje nad nama.’

15Kad se vratio kao kralj, zapovjedi da mu pozovu sluge kojima je dao novac. Htio je znati koliko je koji zaradio. 16Prvi sluga dođe i reče: ‘Gospodaru, udeseterostručio sam iznos koji si mi dao.’ 17‘Odlično! Dobar si sluga’, reče mu on. ‘Zato što si bio vjeran u najmanjemu, dajem ti da vladaš nad deset gradova.’

18Drugi sluga dođe i reče: ‘Upeterostručio sam iznos, gospodaru.’ 19‘Dobro! Vladaj nad pet gradova’, reče i njemu.

20Ali treći sluga dođe bez zarade i reče: ‘Gospodaru, evo ti srebra. Držao sam ga skrivenoga u rupcu. 21Bojao sam te se zato što si strog čovjek. Uzimaš što nije tvoje i žanješ što nisi posijao.’

22‘Zli slugo!’ odgovori mu on. ‘Sudit ću ti prema tvojim vlastitim riječima. Znao si da sam strog, da uzimam što nije moje i da žanjem što nisam posijao? 23Zašto onda nisi moj novac uložio u banku?19:23 U grčkome: kod novčara. Tako bih barem dobio kamate.’ 24Zatim kralj reče: ‘Oduzmite mu to srebro i dajte ga onome koji ima deset!’

25‘Ali, gospodaru, pa on već ima pet kilograma srebra!19:25 U grčkome: deset mina.’ kazali su.

26‘Velim vam,’ odgovori im kralj, ‘onome tko ima dat će se još, a onome tko nema oduzet će se i ono što ima. 27A moje neprijatelje, koji me nisu htjeli za kralja, dovedite ovamo i smaknite ih preda mnom.’”

Mesijanski ulazak u Jeruzalem

(Mt 21:1-11; Mk 11:1-11; Iv 12:12-19)

28Pošto im je to ispričao, Isus krene dalje prema Jeruzalemu. 29Kad se približio mjestima Betfagi i Betaniji na Maslinskoj gori, pošalje naprijed dvojicu učenika. 30“Idite u ono selo pred vama”, reče im, “i čim uđete, vidjet ćete privezano magare koje još nitko nije jahao. Odvežite ga i dovedite ovamo. 31Upita li vas tko: ‘Što to radite?’ recite samo: ‘Treba Gospodinu.’”

32Oni odu i nađu magare kako im je rekao. 33Dok su ga odvezivali, neki ih ljudi upitaju: “Zašto odvezujete magare?”

34“Gospodinu treba”, odgovore oni. 35Dovedu magare Isusu i prebace preko njega svoje ogrtače te posjednu Isusa na njega.

36Mnoštvo je pred Isusom prostiralo svoje ogrtače po putu. 37Kad se već približio obronku Maslinske gore, mnoštvo njegovih sljedbenika počne na sav glas zahvaljivati Bogu za sva slavna djela što su ih vidjeli:

38“Blagoslovljen kralj

koji dolazi u ime Gospodnje!

Na nebu mir!

Slava Bogu na nebu!”19:38 Psalam 118:25-26 i Psalam 148:1.

39Ali neki farizeji među njime kazaše: “Učitelju, opomeni svoje učenike da to ne govore!”

40“Kažem vam,” reče im Isus, “ako oni ušute, klicat će kamenje na cesti!”

Isus tuži nad Jeruzalemom

41Kad se približio Jeruzalemu i ugledao grad, Isus zaplače nad njim: 42“Kako bih volio da si danas pronašao put mira! Ali sada je prekasno i mir je skriven od tebe. 43Doći će dani kada će neprijatelj zauzeti tvoje zidine, opkoliti te i pritisnuti sa svih strana. 44Sravnit će sa zemljom i tebe i tvoju djecu u tebi. Neće od tebe ostati ni kamena na kamenu jer nisi prepoznao da te je Bog pohodio.”

Isus izgoni trgovce iz Hrama

(Mt 21:12-17; Mk 11:15-19; Iv 2:13-22)

45Kad je ušao u Hram, Isus počne iz njega izgoniti trgovce. 46“U Svetome pismu piše: ‘Moj Hram treba biti molitveni dom’, a vi ste ga pretvorili u razbojničku špilju!”,19:46 Izaija 56:7; Jeremija 7:11. reče im.

47Nakon toga Isus je danomice poučavao u Hramu, a svećenički poglavari i pismoznanci smišljali su skupa s narodnim starješinama kako da ga ubiju, 48ali im to nije polazilo za rukom jer je narod upijao svaku njegovu riječ.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Luka 19:1-48

Zakeyu Apulumutsidwa

1Yesu analowa mu Yeriko napitirira. 2Kunali munthu kumeneko dzina lake Zakeyu; iye anali mkulu wa wolandira msonkho ndipo anali wolemera. 3Iye ankafuna kuona Yesu kuti ndani, koma pokhala wamfupi sanathe chifukwa cha gulu la anthu. 4Choncho iye anathamangira patsogolo ndipo anakwera mu mtengo wamkuyu kuti amuone Iye, pakuti Yesu ankadutsa njira imeneyo.

5Yesu atafika pa malopo, anayangʼana mmwamba ndipo anati kwa iye, “Zakeyu, tsika msangamsanga. Ine ndiyenera kukhala mʼnyumba mwako lero.” 6Ndipo nthawi yomweyo anatsika ndipo anamulandira mosangalala.

7Anthu onse ataona zimenezi anayamba kungʼungʼudza, nati, “Iye akupita kuti akakhale mlendo wa wochimwa.”

8Koma Zakeyu anayimirira ndipo anati kwa Ambuye, “Taonani Ambuye! Theka la chuma changa ndipereka kwa osauka ndipo ngati ndinamubera wina aliyense pa chilichonse, ndidzamubwezera mochulukitsa kanayi.”

9Yesu anati kwa iye, “Lero chipulumutso chafika mʼnyumba ino, chifukwa munthu uyu nayenso ndi mwana wa Abrahamu. 10Pajatu Mwana wa Munthu anabwera kudzafunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.”

Antchito Opindula Mosiyana

11Pamene iwo ankamvera izi, Iye anapitiriza kuwawuza fanizo, chifukwa Iye anali kufupi ndi Yerusalemu ndipo anthu ankaganiza kuti ufumu wa Mulungu ukanaoneka nthawi yomweyo. 12Iye anati, “Munthu wa banja laufumu anapita ku dziko lakutali kukadzozedwa ufumu ndipo kenaka abwerenso kwawo. 13Tsono iye anayitana antchito ake khumi ndi kuwapatsa ndalama khumi. Iye anati, ‘Gwiritsani ntchito ndalama izi mpaka nditabwerera.’

14“Koma anthu ake anamuda ndipo anatuma nthumwi pambuyo pake kukanena kuti, ‘Sitikufuna munthuyu kuti akhale mfumu yathu.’

15“Iye analandira ufumuwo ngakhale zinali zotero, ndipo anabwerera kwawo. Kenaka iye anatumiza uthenga kwa antchito ake amene anawapatsa ndalama aja, ndi cholinga chakuti adziwe chimene anapindula nazo.

16“Woyamba anabwera ndipo anati, ‘Bwana ndalama zanu zapindula khumi zina.’

17“Bwana wakeyo anayankha kuti, Wachita bwino wantchito wabwino. ‘Chifukwa wakhulupirika pa zinthu zazingʼono, lamulira mizinda khumi.’

18“Wachiwiri anabwera ndipo anati, ‘Bwana, ndalama zanu zapindula zisanu zina.’

19“Bwana anayankha kuti, ‘Iwe lamulira mizinda isanu.’

20“Kenaka wantchito wina anabwera ndipo anati, ‘Bwana, ndalama yanu nayi; ine ndinayibisa ndi kuyisunga mʼkansalu. 21Ine ndimakuopani, chifukwa ndinu munthu wowuma mtima. Inu mumatenga chimene simunachiyike ndi kukolola chimene simunadzale.’

22“Bwana wake anayankha kuti, ‘Ine ndikukuweruza iwe ndi mawu ako omwewo. Ndiwe wantchito woyipa. Kani umadziwa kuti ndine munthu wowuma mtima ndi wotenga chimene sindinasungitse, ndi kukolola chimene sindinadzale? 23Nanga nʼchifukwa chiyani sunasungitse ndalama yanga, kuti ine pobwera, ndidzayitenge ndi chiwongoladzanja?’

24“Ndipo iye anawuza amene anayimirira pafupi kuti, ‘Tengani ndalama yake ndi kumupatsa amene ali ndi ndalama khumiyo!’ ”

25Iwo anati, “Bwana iyeyu ali nazo kale khumi!”

26Iye anayankha kuti, “Ndikukuwuzani kuti, aliyense amene ali nazo, adzapatsidwa zambiri, koma amene alibe, adzalandidwa ngakhale chimene ali nacho. 27Tsono adani anga aja amene sankafuna kuti ndikhale mfumu yawo, abweretseni pano ndi kuwapha ine ndikuona.”

Yesu Alowa mu Yerusalemu Mwaulemerero

28Yesu atatha kunena izi, anayendabe kupita ku Yerusalemu. 29Iye atayandikira ku Betifage ndi Betaniya pa phiri lotchedwa Olivi, Iye anatuma awiri a ophunzira nati kwa iwo, 30“Pitani mʼmudzi uli patsogolo panu, mukakalowa mʼmudzimo, mukapeza mwana wabulu womangiriridwa amene wina aliyense sanakwerepo. Mukamumasule ndi kubwera naye kuno. 31Ngati wina aliyense akakufunsani kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mukumumasula mwana buluyo?’ Mukamuwuze kuti, ‘Ambuye akumufuna.’ ”

32Otumidwawo anapita nakamupeza mwana wabulu monga momwe Yesu anawawuzira. 33Pamene ankamasula mwana wabuluyo, eni ake anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukumasula mwana wabuluyo?”

34Iwo anayankha kuti, “Ambuye akumufuna.”

35Iwo anabweretsa buluyo kwa Yesu, naponya zovala zawo pa bulupo ndi kumukwezapo Yesu. 36Pamene ankapita, anthu anayala zovala zawo mu msewu.

37Iye atafika pafupi ndi pamene msewu umatsikira ku phiri la Olivi, gulu lonse la ophunzira linayamba kuyamika Mulungu mwachimwemwe ndi mawu ofuwula chifukwa cha zodabwitsa zonse anaziona.

38“Yodala mfumu imene ikubwera mʼdzina la Ambuye!”

“Mtendere kumwamba ndi ulemerero mmwambamwamba!”

39Ena mwa Afarisi mʼgulumo anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, adzudzuleni ophunzira anu!”

40Iye anayankha kuti, “Ine ndikukuwuzani kuti, ngati atakhala chete, miyala idzafuwula.”

41Iye atayandikira ku Yerusalemu ndi kuona mzindawo, anawulirira 42nati, “Iwe ukanadziwa lero lino zinthu zokubweretsera mtendere, koma tsopano zabisikira maso ako. 43Pakuti masiku adzabwera pamene adani ako adzamanga mitumbira yankhondo nakuzungulira, nadzakutsekereza mbali zonse. 44Iwo adzakugwetsera pansi, iwe, ana ako onse a mʼkati mwako. Iwo sadzasiya mwa iwe mwala wina pa unzake, chifukwa sunazindikire nthawi ya kubwera kwa Mulungu.”

Yesu mʼNyumba ya Mulungu

45Kenaka Iye analowa mʼdera la Nyumba ya Mulungu ndi kuyamba kutulutsa kunja amene amachita malonda. 46Iye anawawuza kuti, “Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzakhala nyumba ya mapemphero, koma inu mwayisadutsa phanga la achifwamba.”

47Tsiku lililonse amaphunzitsa mʼNyumba ya Mulungu. Koma akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo ndi atsogoleri pakati pa anthu amayesetsa kuti amuphe. 48Komabe iwo sanathe kupeza njira ina iliyonse kuti achite izi, chifukwa anthu onse anakhulupirira mawu ake.