Djela Apostolska 24 – CRO & CCL

Knijga O Kristu

Djela Apostolska 24:1-27

Pavao pred Feliksom

1Nakon pet dana dođe židovski veliki svećenik Ananija sa starješinama i odvjetnikom Tertulom. Iznesu upravitelju tužbu protiv Pavla. 2Pošto su pozvali Pavla da dođe, Tertulijan ga počne optuživati pred upraviteljem:

“Preuzvišeni Felikse, mi Židovi uživamo velik mir i boljitak korisnih promjena u narodu zahvaljujući tvojoj providnosti. 3Na svemu tome smo duboko zahvalni. 4Da ti dugo ne dodijavam, molim te da nas blagonaklono poslušaš samo nakratko. 5Utvrdili smo da je taj čovjek prava kuga, da neprekidno podjaruje Židove po cijelomu svijetu i da je kolovođa nazaretske sljedbe. 6Čak je i Hram pokušao oskvrnuti pa smo ga uhitili. 8Ispitaš li ga sam, utvrdit ćeš da su naše optužbe opravdane.” 9Potvrde to i drugi Židovi podupirući ga.

10Upravitelj glavom dade Pavlu znak da govori te on reče: “Znam da već mnogo godina sudiš ovomu narodu i zato se mirne duše branim. 11Sam se možeš osvjedočiti da nije prošlo više od dvanaest dana otkako sam se otišao pokloniti Bogu u jeruzalemski Hram. 12Nisam ni s kim raspravljao niti dizao bunu ni ondje, ni u sinagogama, ni po gradu. 13Ovi ljudi ne mogu dokazati to za što me optužuju.

14Ali priznajem da sam sljedbenik Puta, koji oni nazivaju sljedbom, te služim Bogu svojih predaka vjerujući u sve što piše u židovskome Zakonu i u proročkim knjigama. 15Jednako se, kao i oni, pouzdajem u Boga da će uskrsnuti i pravednici i nepravednici. 16Zato se uvijek trudim imati čistu savjest i pred Bogom i pred ljudima.

17Nakon nekoliko godina vratio sam se u Jeruzalem donijeti milodare svojemu narodu i prinijeti žrtvu Bogu. 18Moji su me tužitelji vidjeli u Hramu kad sam dovršavao obred posvećenja, a ne sa svjetinom ni u metežu. 19Ali ondje su bili neki Židovi iz Male Azije—oni bi me, zapravo, trebali doći optužiti pred tobom ako imaju što protiv mene. 20Ili upitaj ove ovdje kakvu su krivnju na meni našli članovi Vijeća 21osim možda jedne jedine riječi što sam ju viknuo stojeći među njima: ‘Danas mi se pred vama sudi jer vjerujem u uskrsnuće mrtvih!’”

22Feliks, koji je mnogo znao o Putu, odgodi preslušanje i reče: “Pričekat ćete da dođe zapovjednik Lizija. On će riješiti vaš spor.” 23Zapovjedi stotniku da i dalje čuva Pavla u zatvoru, ali da mu odobri olakšice i da nikomu od njegovih ne brani da ga poslužuje.

24Nekoliko dana zatim Feliks dođe sa svojom ženom Druzilom koja je bila Židovka. Pošalje po Pavla te ga je slušao kako govori o vjeri u Isusa Krista. 25Kad je Pavao počeo govoriti o pravednosti, uzdržljivosti i sudu što dolazi, Feliks se prestraši. “Idi sada”, reče. “Pozvat ću te kad nađem vremena.” 26Nadao se, osim toga, da će mu Pavao dati novca. Zato ga je često pozivao i razgovarao s njim.

27Tako su prošle dvije godine. Feliksa zatim zamijeni Porcije Fest. Želeći ugoditi Židovima, Feliks ostavi Pavla u zatvoru.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Machitidwe a Atumwi 24:1-27

Felike Amva Mlandu wa Paulo

1Patapita masiku asanu mkulu wa ansembe Hananiya, pamodzi ndi akuluakulu ena ndi katswiri woyankhulira anthu pa milandu wotchedwa Tertuliyo anapita ku Kaisareya ndipo anafotokoza mlandu wa Paulo kwa Bwanamkubwayo. 2Atamuyitana Paulo, ndipo Tertuliyo anafotokozera Felike nkhani yonse ya Paulo. Iye anati, “Wolemekezeka, ife takhala pamtendere nthawi yayitali chifukwa cha inu, ndipo utsogoleri wanu wanzeru wabweretsa kusintha mʼdziko lino. 3Wolemekezeka Felike ife timazilandira zimenezi moyamika kwambiri ponseponse ndi mwa njira iliyonse. 4Koma kuti tisakuchedwetseni, ndikupempha kuti mwa kuleza mtima kwanu mutimvere ife.

5“Ife tapeza kuti munthu uyu amayambitsa mavuto ndi kuwutsa mapokoso pakati pa Ayuda onse a dziko lonse lapansi. Iyeyu ndi mtsogoleri wa mpatuko wa Anazareti. 6Anayesera ngakhale kudetsa Nyumba ya Mulungu wathu. Ndiye ife tinamugwira. 7Koma, mkulu wa asilikali Lusiya anafika mwamphamvu namuchotsa mʼmanja mwathu. 8Ndipo Lusiya analamula kuti amene anali naye ndi mlandu abwere kwa inu. Mukamufunsa ameneyu kwa nokha mudzadziwa choonadi cha zimene ife tikumunenera.”

9Ayuda anavomereza nanenetsa kuti zimenezi zinali zoona.

10Bwanamkubwayo atakodola Paulo ndi kulola kuti ayankhule, Pauloyo anati, “Ine ndikudziwa kuti inu mwakhala mukuweruza dziko lino zaka zambiri, kotero ndikukondwera kuti ndikudziteteza ndekha pamaso panu. 11Inu mukhoza kupeza umboni wake. Sipanapite masiku khumi ndi awiri chipitireni changa ku Yerusalemu kukapembedza. 12Amene akundiyimba mlanduwa sanandipeze mʼNyumba ya Mulungu ndi kutsutsana ndi wina aliyense kapena kuyambitsa chisokonezo mʼsunagoge kapena pena paliponse mu mzindamo. 13Ndipo sangathe kupereka umboni wa mlandu umene akundiyimba inewu. 14Komatu ine ndikuvomera kuti ndimapembedza Mulungu wa makolo athu, monga wotsatira wa Njirayo, imene iwo akuyitchula mpatuko. Ine ndimakhulupirira chilichonse chimene chimagwirizana ndi malamulo ndiponso zimene zinalembedwa ndi Aneneri. 15Ine ndili nacho chiyembekezo chomwecho chimene iwo ali nacho mwa Mulungu, kuti kudzakhala kuuka kwa akufa kwa olungama ndiponso kwa ochimwa. 16Kotero ine ndimayesetsa kuti ndikhale ndi chikumbumtima chosanditsutsa pamaso pa Mulungu ndi anthu onse.

17“Patapita zaka zambiri, ndinabwera ku Yerusalemu kudzapereka mphatso kwa anthu osauka a mtundu wanga komanso kudzapereka nsembe. 18Pamene ndinkachita zimenezi, iwo anandipeza mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu nditachita mwambo wodziyeretsa. Panalibe gulu la anthu kapena kuti ndimachita za chisokonezo chilichonse. 19Koma pali Ayuda ena ochokera ku Asiya, amene amayenera kukhala pano pamaso panu, kundiyimba mlandu ngati ali ndi kalikonse konditsutsa ine. 20Kapena awa amene ali panowa anene mlandu umene anapeza mwa ine, pamene ndinayima pamaso pa Bwalo lawo Lalikulu. 21Koma cholakwa changa chingathe kukhala chokhachi chakuti, nditayima pamaso pawo ndinafuwula kuti, ‘Mukundiweruza ine lero chifukwa ndimakhulupirira kuti akufa adzauka.’ ”

22Kenaka Felike, amene amadziwa bwino za Njirayo, anayamba wayimitsa mlanduwo, nati, “Ndidzagamula mlandu wako akabwera mkulu wa asilikali Lusiya.” 23Iye analamulira woyangʼanira asilikali 100 kuti alondere Paulo, koma azimupatsako ufulu ndiponso kulola abwenzi ake kuti adzimusamalira.

24Patapita masiku angapo Felike anabwera pamodzi ndi mkazi wake Drusila, amene anali Myuda. Anayitana Paulo ndipo anamvetsera zimene amayankhula za chikhulupiriro mwa Khristu Yesu. 25Paulo atayankhula za chilungamo, za kudziretsa ndiponso za chiweruzo chimene chikubwera, Felike anachita mantha ndipo anati, “Basi tsopano! Pita. Tidzakuyitanitsa tikadzapeza mpata.” 26Pa nthawi imeneyi amayembekeza kuti Paulo adzamupatsa ndalama, nʼchifukwa chake amamuyitanitsa kawirikawiri ndi kumayankhula naye.

27Patapita zaka ziwiri, Porkiyo Festo analowa mʼmalo mwa Felike, koma anamusiya Paulo mʼndende, chifukwa amafuna kuti Ayuda amukonde.