Zekariya 7 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zekariya 7:1-14

Chiweruzo Cholungama ndi Chifundo, Osati Kusala Zakudya

1Pa chaka chachinayi cha Mfumu Dariyo, pa tsiku lachinayi la Kisilevi, mwezi wachisanu ndi chinayi, Yehova anayankhula ndi Zekariya. 2Anthu a ku Beteli anali atatuma Sarezeri ndi Regemu-Meleki pamodzi ndi anthu awo, kuti akapemphe chifundo kwa Yehova 3pokafunsa kwa ansembe a ku Nyumba ya Yehova Wamphamvuzonse ndi aneneri kuti, “Kodi ine ndizilira ndi kusala zakudya pa mwezi wachisanu, monga mmene ndakhala ndikuchitira pa zaka zambiri?”

4Pamenepo Yehova Wamphamvuzonse anayankhula nane kuti, 5“Funsa anthu onse a mʼdziko ndi ansembe kuti, ‘Pamene munkasala zakudya pa mwezi wachisanu ndi wachisanu ndi chiwiri pa zaka 70 zapitazi, kodi munkasala chifukwa cha Ine? 6Ndipo pamene munkadya ndi kumwa, kodi simunkachita zimenezi podzisangalatsa nokha? 7Kodi awa si mawu amene Yehova ankanena kudzera mwa aneneri oyamba aja pamene Yerusalemu ndi mizinda yake yozungulira anali pa mtendere ndi pa ulemerero, ndi pamene Negevi ndi ku madera akumadzulo a mʼmbali mwa phiri munali anthu?’ ”

8Ndipo Yehova anayankhulanso ndi Zekariya kuti, 9“Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Muziweruza molungama; muzichitirana chifundo ndi kumverana chisoni. 10Musamazunze akazi amasiye kapena ana amasiye, alendo kapena osauka. Musamaganizirane zoyipa mʼmitima mwanu.’

11“Koma makolo anu anakana kumvera uthenga umenewu; anawumitsa mtima nandifulatira, natseka makutu awo kuti asamve. 12Anawumitsa mitima yawo ngati mwala wa sangalabwi ndipo sanamvere lamulo kapena mawu amene Yehova Wamphamvuzonse anawatumiza mwa Mzimu wake kudzera mwa aneneri oyamba aja. Kotero Yehova Wamphamvuzonse anakwiya kwambiri.

13“ ‘Pamene ndinawayitana, iwo sanamvere; choncho pamene iwo anandiyitana, Ine sindinamverenso,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. 14‘Ndinawamwaza ndi kamvuluvulu pakati pa mitundu yonse ya anthu, kumene anali alendo. Dziko lawo linatsala litasakazidwa kwambiri kotero kuti palibe amene amabwera kapena kupitamo. Umu ndi mmene anasandutsira dziko labwino kukhala chipululu.’ ”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

撒迦利亚书 7:1-14

呼吁公义和怜悯

1大流士王四年九月,即基斯流月四日,耶和华的话传给了撒迦利亚2那时,伯特利人差遣沙利色利坚米勒及其随从去向耶和华求恩。 3他们问万军之耶和华殿里的祭司和先知:“我们还要照多年的惯例在五月哀伤、禁食吗?”

4万军之耶和华的话传给了我,说: 5“你要对境内的民众和祭司说,‘七十年来,你们在五月和七月禁食、哀伤,难道真的是为了我吗? 6你们吃喝,难道不是为自己吃、为自己喝吗? 7这些不是耶和华借从前的先知所宣告的吗?当时耶路撒冷和周围的城邑人口兴盛、繁荣,南地和丘陵都有人居住。’”

8耶和华的话又传给了撒迦利亚,说: 9“万军之耶和华曾对你们的祖先说,‘要秉公行义,彼此以慈爱和怜悯相待。 10不可欺压寡妇、孤儿、寄居者和穷人,不可设阴谋彼此相害。’ 11他们却不理会,背过身去,充耳不闻, 12心如铁石,不遵从律法,也不遵从万军之耶和华借着祂的灵指示从前的先知所说的话。因此,万军之耶和华非常愤怒。 13祂说,‘我曾呼唤他们,他们不听;将来他们呼求我,我也不听。 14我要用旋风把他们吹散到陌生的万国中,使他们的土地荒凉、杳无人迹,因为他们使美好的土地一片荒凉。’”