Zekariya 14 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zekariya 14:1-21

Yehova Akubwera ndipo Akulamulira

1Taonani tsiku la Yehova likubwera pamene zinthu zimene adani ako anakulanda azidzagawana iwe ukuona.

2Ndidzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse kuti adzathire nkhondo Yerusalemu; mzindawu udzalandidwa, nyumba zidzaphwasulidwa, ndipo akazi adzagwiriridwa. Theka la anthu a mu mzindamu lidzapita ku ukapolo, koma ena onse otsala mu mzindamu sadzachotsedwa.

3Pamenepo Yehova adzabwera kudzamenyana ndi mitundu ya anthu imeneyi, ngati mmene amachitira pa nthawi ya nkhondo. 4Tsiku limenelo adzayimirira pa Phiri la Olivi, kummawa kwa Yerusalemu, ndipo Phiri la Olivilo lidzagawikana pawiri kuyambira kummawa mpaka kumadzulo, kupanga chigwa chachikulu, kuchititsa kuti theka la phiri lisunthire kumpoto ndi linalo kummwera. 5Inu mudzathawa podzera mʼchigwa chapakati pa phirilo, pakuti chidzafika mpaka ku Azeli. Mudzathawa monga munachitira pa tsiku la chivomerezi nthawi ya Uziya mfumu ya Yuda. Kenaka Yehova Mulungu wanga adzabwera, pamodzi ndi oyera ake onse.

6Tsiku limenelo sipadzakhala kuwala, kuzizira kapena chisanu. 7Lidzakhala tsiku lapaderadera, silidzakhala usana kapena usiku; tsiku limeneli akulidziwa ndi Yehova yekha. Ikadzafika nthawi ya madzulo, kudzakhala kukuwalabe.

8Tsiku limenelo madzi amoyo adzatuluka mu Yerusalemu, theka lidzapita ku nyanja ya kummawa ndipo theka lina ku nyanja ya kumadzulo, nthawi yachilimwe ndi nthawi yozizira yomwe.

9Ndipo Yehova adzakhala mfumu pa dziko lonse lapansi. Tsiku limenelo padzakhala Ambuye mmodzi yekha, ndipo dzina lidzakhala limodzi lomwelo.

10Dziko lonse, kuyambira ku Geba mpaka ku Rimoni, kummwera kwa Yerusalemu, lidzakhala ngati Araba. Koma Yerusalemu adzakwezedwa ndipo adzakhala pamalo pakepo, kuyambira ku Chipata cha Benjamini mpaka ku malo amene ali ku Chipata Choyamba, ku Chipata Chapangodya, ndipo kuyambira ku Nsanja ya Hananeli mpaka ku malo opsinyira mphesa za mfumu. 11Mʼmenemo mudzakhala anthu; sadzawonongedwanso. Yerusalemu adzakhala pa mtendere.

12Mliri umene Yehova adzakanthire nawo mitundu yonse ya anthu imene inkamenyana ndi Yerusalemu ndi uwu: Matupi awo adzawola iwo eni akuyenda, maso awo adzawola ali mʼmalo mwake, ndipo malilime awo adzawola ali mʼkamwa mwawo. 13Pa tsiku limenelo Yehova adzasokoneza anthu akuluakulu. Munthu aliyense adzagwira dzanja la mnzake, ndi kuyamba kumenyana okhaokha. 14Yuda nayenso adzachita nkhondo ku Yerusalemu. Chuma chonse cha anthu a mitundu yozungulira adzachisonkhanitsa pamodzi; golide, siliva ndi zovala zochuluka kwambiri. 15Mliri womwewo udzapha akavalo ndi nyulu, ngamira ndi abulu, pamodzi ndi nyama zonse zokhala ku misasako.

16Kenaka opulumuka ochokera mwa mitundu yonse ya anthu amene anathira nkhondo Yerusalemu, azidzapita chaka ndi chaka kukapembedza Mfumu Yehova Wamphamvuzonse, ndiponso kukachita Chikondwerero cha Misasa. 17Ngati mitundu ina ya anthu pa dziko lapansi sidzapita ku Yerusalemu kukapembedza Mfumu Yehova Wamphamvuzonse, idzakhala wopanda mvula. 18Ndipo ngati anthu a ku Igupto sadzapita ndi kukakhala nawo kumeneko, adzakhala wopanda mvula. Yehova adzabweretsa pa iwo mliri umene analangira mitundu ina ya anthu imene sinapite ku Chikondwerero cha Misasa. 19Chimenechi chidzakhala chilango cha Igupto ndiponso mitundu ina yonse imene sidzapita ku Chikondwerero cha Misasa.

20Pa tsiku limenelo pa maberu a akavalo padzalembedwa mawu oti wopatulikira Yehova, ndipo miphika ya mʼNyumba ya Yehova idzakhala yopatulika ngati mbale za ku guwa. 21Mʼphika uliwonse ku Yerusalemu ndi ku Yuda udzakhala wopatulikira Yehova Wamphamvuzonse, ndipo onse amene adzabwera kudzapereka nsembe adzatenga miphika ina ndi kuphikiramo. Ndipo nthawi imeneyo simudzakhalanso Akanaani mʼNyumba ya Yehova Wamphamvuzonse.