Zekariya 13 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zekariya 13:1-9

Kuyeretsedwa ku Tchimo

1“Pa tsiku limenelo nyumba ya Davide adzayitsekulira kasupe wa madzi pamodzi ndi okhala mu Yerusalemu, kuti awachotsere tchimo lawo ndi chodetsa chawo.

2“Pa tsiku limenelo, ndidzafafaniziratu mayina a mafano mʼdziko, ndipo sadzawakumbukiranso,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Ndidzachotsa mʼdziko aneneri pamodzi ndi mzimu wonyansa. 3Ndipo ngati wina aliyense adzafuna kunenera, abambo ndi amayi ake amene anamubereka, adzamuwuza kuti, ‘Uyenera kufa, chifukwa wayankhula bodza mʼdzina la Yehova.’ Pamene anenera, makolo ake omwe adzamubaya.

4“Pa tsiku limenelo mneneri aliyense adzachita manyazi chifukwa cha masomphenya ake. Sadzavala chovala chake chaubweya ndi cholinga chonamiza anthu. 5Iye adzati, ‘Sindine mneneri. Ndine mlimi; ndakhala ndi kulima munda kuyambira ubwana wanga.’ 6Ngati wina adzamufunsa, ‘Zilonda zili mʼthupi lakoli ndi chiyani?’ Iye adzayankha kuti, ‘Zilondazi ndinazilandira mʼnyumba ya abwenzi anga.’

Kukantha Mʼbusa, Nkhosa Kubalalika

7“Dzambatuka iwe lupanga, ukanthe mʼbusa wanga,

ukanthe munthu amene ali pafupi ndi Ine!”

akutero Yehova Wamphamvuzonse.

Kantha mʼbusa

ndipo nkhosa zidzabalalika,

ndipo ndidzatambalitsa dzanja langa kuwononga zazingʼono.

8Mʼdziko monse, akutero Yehova Wamphamvuzonse,

“zigawo ziwiri mwa zigawo zitatu za anthu zidzakanthidwa ndi kuwonongeka;

koma chigawo chimodzi chidzatsala mʼdzikomo.

9Chigawo chachitatuchi ndidzachiyika pa moto;

ndidzawayeretsa monga momwe amayeretsera siliva

ndi kuwayesa monga momwe amayesera golide.

Adzayitana pa dzina langa

ndipo Ine ndidzawayankha;

Ine ndidzanena kuti, ‘Awa ndi anthu anga,’

ndipo iwo adzanena kuti, ‘Yehova ndiye Mulungu wathu.’ ”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

撒迦利亚书 13:1-9

1“到那天,必为大卫家和耶路撒冷的居民开一个泉源,洗净他们的罪恶和污秽。

2“到那天,我必铲除地上偶像的名号,使它们被人遗忘;我必除去地上的假先知和污秽的灵。这是万军之耶和华说的。 3若有人再说预言,他的亲生父母必对他说,‘你不得活命,因为你奉耶和华的名说谎。’他说预言的时候,他的亲生父母必把他刺死。 4到那天,先知必因自己所讲的异象而羞愧,不再穿着毛皮衣欺骗人。 5他必说,‘我不是先知,我是农夫,我从小便以种田为生。’ 6若有人问他,‘你胸口上的伤是怎么回事?13:6 异教的先知有用利器自割或自刺的习惯。’他必回答说,‘是在我朋友家弄伤的。’”

牧人被杀

7万军之耶和华说:

“刀剑啊,醒来吧,

要攻击我的牧人和同伴,

要击打牧人,羊群将四散,

我必出手攻击小羊。

8地上三分之二的人必遭铲除、毁灭,

只剩下三分之一的人存活。

这是耶和华说的。

9我必使这三分之一的人受到火一般的考验;

我必像熬炼银子一样熬炼他们,

像试炼金子一样试炼他们。

他们必呼求我的名,

我必回应他们。

我必说,‘这是我的子民。’

他们必说,‘耶和华是我们的上帝。’”