Zekariya 12 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zekariya 12:1-14

Kuphedwa kwa Adani a Yerusalemu

Ulosi

1Uthenga wa Yehova kwa Israeli. Yehova, amene amayala mlengalenga, amene amayika maziko a dziko lapansi, ndiponso amene amalenga mzimu wokhala mwa munthu, akunena kuti, 2“Taonani, ndidzasandutsa Yerusalemu kukhala chakumwa choledzeretsa chimene chidzasokoneza mitundu yonse ya anthu yomuzungulira. Yuda adzazingidwa pamodzinso ndi Yerusalemu. 3Pa tsiku limenelo, pamene mitundu yonse ya anthu a dziko lapansi idzasonkhana kulimbana naye, ndidzasandutsa Yerusalemu thanthwe losatheka kusunthidwa ndi mitundu yonse ya anthu. Onse oyesa kumusuntha adzadzipweteka. 4Pa tsiku limenelo kavalo aliyense ndidzamuchititsa mantha kuti asokonezeke, ndipo wokwerapo wake ndidzamuchititsa misala,” akutero Yehova. “Ndidzayangʼanira nyumba ya Yuda koma ndidzachititsa khungu akavalo onse a anthu a mitundu ina. 5Pamenepo atsogoleri a Yuda adzayankhula mʼmitima mwawo kuti, ‘Anthu a ku Yerusalemu ndi amphamvu, chifukwa Yehova Wamphamvuzonse ndiye Mulungu wawo.’

6“Pa tsiku limenelo ndidzasandutsa atsogoleri a Yuda kukhala ngati mbawula yotentha pakati pa nkhuni, ngati sakali yoyaka pa mitolo ya tirigu. Adzatentha mitundu yonse ya anthu yowazungulira, kumanja ndi kumanzere, koma Yerusalemu sadzasuntha pa malo ake.

7“Yehova adzapulumutsa malo okhala Yuda poyamba, kuti ulemu wa nyumba ya Davide ndi wa anthu okhala mu Yerusalemu usapambane ulemu wa Yuda. 8Pa tsiku limenelo Yehova adzatchinjiriza onse okhala mu Yerusalemu, kotero kuti anthu ofowoka kwambiri pakati pawo adzakhala ngati Davide, ndipo nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mngelo wa Yehova wowatsogolera. 9Pa tsiku limenelo ndidzawononga mitundu yonse yofuna kuthira nkhondo Yerusalemu.

Kulirira amene Anamulasa

10“Ndipo pa nyumba ya Davide ndi pa anthu okhala mu Yerusalemu ndidzakhuthulirapo mzimu wachisomo ndi wopemphera. Iwo adzandiyangʼana Ine, amene anamubaya, ndipo adzamulirira kwambiri monga momwe munthu amalirira mwana wake mmodzi yekhayo, ndiponso adzamva chisoni kwambiri monga momwe amachitira ndi mwana woyamba kubadwa. 11Pa tsiku limenelo mudzakhala kulira kwakukulu mu Yerusalemu, monga kulira kwa ku Hadadi-Rimoni ku chigwa cha Megido. 12Dziko lidzalira kwambiri, fuko lililonse pa lokha, akazi awo pa okhanso: fuko la Davide pamodzi ndi akazi awo, fuko la Natani pamodzi ndi akazi awo, 13nyumba ya Levi pamodzi ndi akazi awo, fuko la Simei pamodzi ndi akazi awo, 14ndiponso mafuko onse pamodzi ndi akazi awo.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

撒迦利亞書 12:1-14

耶路撒冷必蒙拯救

1以下是耶和華關於以色列的啟示。

鋪展穹蒼、奠立大地的根基、塑造人靈魂的耶和華說: 2「看啊,我要使耶路撒冷成為令周圍萬民昏醉的酒杯。耶路撒冷被圍困時,猶大也必受困。 3到那天,當地上的列國聚集起來攻擊耶路撒冷的時候,我要使耶路撒冷成為一塊沉重的石頭。凡試圖舉起它的,必傷自己。 4到那天,我要使所有的戰馬驚恐,使馬上的騎士癲狂。我必看顧猶大家,使列邦的馬匹瞎眼。這是耶和華說的。 5那時,猶大的族長必心裡說,『耶路撒冷的居民從他們的上帝——萬軍之耶和華那裡得到了力量。』

6「到那天,我必使猶大的族長像木柴中的火盆,像禾捆中的火把,吞噬左右四圍的列邦,但耶路撒冷人必仍在原處——耶路撒冷安居。

7「耶和華必首先拯救猶大的帳篷,免得大衛家和耶路撒冷居民的榮耀超過猶大8到那天,耶和華必保護耶路撒冷的居民,使他們當中最軟弱的像大衛一樣剛強,使大衛家像上帝一樣,像耶和華的天使一樣帶領他們。 9到那天,我必毀滅前來攻擊耶路撒冷的列國。

10「我必將施恩和禱告的靈澆灌在大衛家和耶路撒冷的居民身上。他們必仰望我——他們所刺的那位,如喪獨子一般為祂哀傷,如喪長子一般為祂痛哭。 11到那天,耶路撒冷必一片哀聲,猶如米吉多平原的哈達臨門的哀聲。 12境內家家戶戶都必哀哭。大衛家的男子在一處,女子在一處;拿單家的男子在一處,女子在一處; 13利未家的男子在一處,女子在一處;示每家的男子在一處,女子在一處。 14其餘各家也都哀哭,男女分開。