Zekariya 11 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zekariya 11:1-17

1Tsekula zitseko zako, iwe Lebanoni,

kuti moto unyeketse mikungudza yako!

2Lira mwachisoni, iwe mtengo wa payini, pakuti mkungudza wagwa;

mtengo wamphamvu wawonongeka!

Lirani mwachisoni, inu mitengo ya thundu ya Basani;

nkhalango yowirira yadulidwa!

3Imvani kulira mwachisoni kwa abusa;

msipu wawo wobiriwira wawonongeka!

Imvani kubangula kwa mikango;

nkhalango yowirira ya ku Yorodani yawonongeka!

Abusa Awiri

4Yehova Mulungu wanga akuti, “Dyetsa nkhosa zimene zikukaphedwa. 5Amene amagula nkhosazo amazipha ndipo salangidwa. Amene amazigulitsa amanena kuti, ‘Alemekezeke Yehova, ine ndalemera!’ Abusa ake omwe sazimvera chisoni nkhosazo. 6Pakuti Ine sindidzamveranso chisoni anthu okhala mʼdziko,” akutero Yehova. “Ndidzapereka munthu aliyense mʼmanja mwa mnansi wake ndi mwa mfumu yake. Iwo adzazunza dziko, ndipo Ine sindidzawapulumutsa mʼmanja mwawo.”

7Choncho ine ndinadyetsa nkhosa zokaphedwa, makamaka nkhosa zoponderezedwa. Pamenepo ndinatenga ndodo ziwiri ndipo yoyamba ndinayitcha Kukoma mtima ndipo yachiwiri ndinayitcha Umodzi ndipo ndinadyetsa nkhosazo. 8Pa mwezi umodzi ndinachotsa abusa atatu.

Abusawo anadana nane, ndipo ndinatopa nawo. 9Ndinawuza gulu la nkhosalo kuti, “Sindidzakhalanso mʼbusa wanu. Imene ikufa, ife, ndipo imene ikuwonongeka, iwonongeke, zimene zatsala zizidyana.”

10Kenaka ndinatenga ndodo yanga yotchedwa Kukoma mtima ndi kuyithyola, kuphwanya pangano limene ndinachita ndi mitundu yonse ya anthu. 11Linaphwanyidwa tsiku limenelo ndipo nkhosa zosautsidwa zimene zimandiyangʼanitsitsa zinadziwa kuti anali mawu a Yehova.

12Ndinawawuza kuti, “Ngati mukuganiza kuti zili bwino, patseni malipiro anga; koma ngati si choncho, sungani malipirowo.” Kotero anandipatsa ndalama zasiliva makumi atatu.

13Ndipo Yehova anandiwuza kuti, “Ziponye kwa wowumba mbiya,” mtengo woyenera umene anapereka pondigula Ine! Choncho ndinatenga ndalama zasiliva makumi atatu ndi kuziponya mʼnyumba ya Yehova kwa wowumba mbiya.

14Kenaka ndinathyola ndodo yanga yachiwiri yotchedwa Umodzi, kuthetsa ubale pakati pa Yuda ndi Israeli.

15Pamenepo Yehova anayankhula nane kuti, “Tenganso zida za mʼbusa wopusa. 16Pakuti ndidzawutsa mʼbusa mʼdzikomo amene sadzasamalira zotayika, kapena kufunafuna zazingʼono, kapena zovulala, kapena kudyetsa nkhosa zabwino, koma iye adzadya nyama ya nkhosa zonenepa, nʼkumakukuta ndi ziboda zomwe.

17“Tsoka kwa mʼbusa wopandapake,

amene amasiya nkhosa!

Lupanga limukanthe pa mkono wake ndi pa diso lake lakumanja!

Mkono wake ufote kotheratu,

diso lake lamanja lisaonenso.”