Zefaniya 2 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zefaniya 2:1-15

1Sonkhanani pamodzi, sonkhanani pamodzi,

inu mtundu wochititsa manyazi,

2isanafike nthawi yachiweruzo,

nthawi yanu isanawuluke ngati mungu,

usanakufikeni mkwiyo woopsa wa Yehova,

tsiku la ukali wa Yehova lisanafike pa inu.

3Funafunani Yehova, inu nonse odzichepetsa a mʼdziko,

inu amene mumachita zimene amakulamulani.

Funafunani chilungamo, funafunani kudzichepetsa;

mwina mudzatetezedwa

pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.

Za Afilisti

4Gaza adzasiyidwa

ndipo Asikeloni adzasanduka bwinja.

Nthawi yamasana Asidodi adzakhala wopanda anthu

ndipo Ekroni adzazulidwa.

5Tsoka inu okhala mʼmbali mwa nyanja,

inu mtundu wa Akereti;

mawu a Yehova akutsutsa

iwe Kanaani, dziko la Afilisti.

“Ndidzakuwononga

ndipo palibe amene adzatsale.”

6Dziko la mʼmbali mwa nyanja, kumene kumakhala Akereti,

lidzakhala malo a abusa ndi la makola a nkhosa.

7Malowa adzakhala a anthu otsala a nyumba ya Yuda;

adzapezako msipu.

Nthawi ya madzulo adzagona

mʼnyumba za Asikeloni.

Yehova Mulungu wawo adzawasamalira;

adzabwezeretsa mtendere wawo.

Za Mowabu ndi Amoni

8“Ndamva kunyoza kwa Mowabu

ndi chipongwe cha Amoni,

amene ananyoza anthu anga

ndi kuopseza kuti alanda dziko lawo.

9Choncho, pali Ine Wamoyo,”

akutero Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli,

“Ndithu, Mowabu adzasanduka ngati Sodomu,

Amoni adzasanduka ngati Gomora;

malo a zomeramera ndi maenje a mchere,

dziko la bwinja mpaka muyaya.

Anthu anga otsala adzawafunkha;

opulumuka a mtundu wanga adzalandira dziko lawo.”

10Ichi ndi chimene adzalandire chifukwa cha kunyada kwawo,

chifukwa chonyoza ndi kuchitira chipongwe anthu a Yehova Wamphamvuzonse.

11Yehova adzawachititsa mantha kwambiri

pamene adzawononga milungu yonse ya mʼdzikomo.

Ndipo mitundu ya anthu pa dziko lonse idzamulambira,

uliwonse ku dziko la kwawo.

Za Kusi

12“Inunso anthu a ku Kusi,

mudzaphedwa ndi lupanga.”

Za Asiriya

13Yehova adzatambasulira dzanja lake kumpoto

ndi kuwononga Asiriya,

kusiya Ninive atawonongekeratu

ndi owuma ngati chipululu.

14Nkhosa ndi ngʼombe zidzagona pansi kumeneko,

pamodzi ndi nyama zakuthengo za mtundu uliwonse.

Akadzidzi a mʼchipululu ndi akanungu

adzakhala pa nsanamira zake.

Kulira kwawo kudzamveka mʼmazenera,

mʼmakomo mwawo mudzakhala zinyalala zokhazokha,

nsanamira za mkungudza zidzakhala poonekera.

15Umenewu ndiye mzinda wosasamala

umene kale unali wotetezedwa.

Unkanena kuti mu mtima mwake,

“Ine ndine, ndipo palibenso wina wondiposa.”

Taonani lero wasanduka bwinja,

kokhala nyama zakutchire!

Onse owudutsa akuwunyoza

ndi kupukusa mitu yawo.