Yuda 1 – CCL & NIVUK

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yuda 1:1-25

1Ndine Yuda, mtumiki wa Yesu Khristu, komanso mʼbale wake wa Yakobo.

Kwa inu amene Mulungu Atate anakuyitanani, amene amakukondani ndikukusungani mwa Yesu Khristu.

2Chifundo, mtendere ndi chikondi zikhale nanu mochuluka.

Tchimo ndi Kuwonongeka kwa Osapembedza

3Okondedwa, ngakhale ndinkafunitsitsa kukulemberani za chipulumutso cha tonsefe, ndakakamizidwa kuti ndikulembereni ndi kukupemphani kolimba kuti mumenye ndithu nkhondo yotchinjiriza chikhulupiriro chimene Mulungu anachipereka kamodzi kokha kwa anthu onse oyera mtima. 4Pakuti anthu ena amene za chilango chawo zinalembedwa kale, alowa mobisika pakati panu. Amenewa ndi anthu osapembedza Mulungu, amene amapotoza chisomo cha Mulungu wathu kuchisandutsa ufulu ochitira zonyansa ndiponso amakana Yesu Khristu amene Iye ndiye Mbuye ndi Mfumu yathu.

5Ngakhale munazidziwa kale zonsezi, ndafuna kuti ndikukumbutseni kuti Ambuye anapulumutsa anthu ake ndi kuwatulutsa mʼdziko la Igupto, koma pambuyo pake anawononga amene sanakhulupirire. 6Ndipo mukumbukire angelo amene sanakhutire ndi maudindo awo, koma anasiya malo awo. Angelo amenewa Mulungu anawamanga ndi maunyolo osatha, ndipo akuwasunga mʼmalo a mdima mpaka tsiku lalikulu lachiweruzo. 7Musayiwale mizinda ya Sodomu ndi Gomora ija, ndi mizinda yoyandikana nayo. Anthu mʼmenemo anadziperekanso kuchita zadama ndi kuchita zonyansa zachilendo. Mizinda imeneyi yakhala ngati chitsanzo cha amene adzalangidwa ndi moto wosatha.

8Nʼchimodzimodzinso zimene akuchita anthu amenewa potsata maloto awo, amadetsa matupi awo, amakana ulamuliro wa Mulungu ndiponso amachitira chipongwe angelo akumwamba. 9Koma ngakhale mkulu wa angelo Mikayeli, pamene ankalimbana ndi Mdierekezi za mtembo wa Mose, sanamunene kuti wachipongwe, koma anati, “Ambuye akudzudzule iwe!” 10Koma anthu awa amachita chipongwe zinthu zimene sakuzidziwa. Ndipo zinthu zimene amazidziwa ndi nzeru zachibadwa, monga za nyama, ndizo zimene zimawawononga.

11Tsoka kwa iwo chifukwa anatsatira njira ya Kaini. Iwo athamangira phindu, nʼchifukwa chake anagwa mʼtchimo la Baalamu. Iwo anawonongedwa chifukwa chowukira monga anachitira Kora.

12Anthu amenewa ndiwo amayipitsa maphwando anu achikondi. Amadya nanu mopanda manyazi ndipo ali ngati abusa amene amangodzidyetsa okha. Anthuwa ali ngati mitambo yowuluzika ndi mphepo, yopanda mvula. Ali ngati mitengo ya nthawi ya masika, yopanda zipatso, yozuka mizu, mitengo yoferatu. 13Iwowa ali ngati mafunde awukali apanyanja, amene amatulutsa thovu la zonyansa zawo. Amenewa ali ngati nyenyezi zosochera, ndipo Mulungu akuwasungira mdima wandiweyani mpaka muyaya.

14Enoki, wachisanu ndi chiwiri kuyambira pa Adamu, ananeneratu za anthu amenewa kuti, “Onani, Ambuye akubwera ndi oyera ake osawerengeka 15kuti adzaweruze aliyense, ndi kudzagamula kuti onse osapembedza ndi olakwa, chifukwa cha ntchito zawo zosalungama zimene anachita mʼmoyo wawo osaopa Mulungu. Adzawatsutsa chifukwa cha mawu onse achipongwe amene osapembedzawa ananyoza nawo Ambuye.” 16Anthu amenewa amangʼungʼudza ndi kudandaula. Amatsatira zilakolako zawo zoyipa. Amayankhula zodzitamandira ndipo amanamiza ena pofuna kupeza phindu.

Awalimbikitsa kuti Apirire

17Koma okondedwa, kumbukirani zimene atumwi a Ambuye athu Yesu Khristu ananeneratu. 18Iwo anakuwuzani kuti, “Mʼmasiku otsiriza kudzafika anthu onyoza, otsatira zofuna zawo zoyipa.” 19Anthu amenewa ndi amene akubweretsa mipatuko pakati panu, amatsatira nzeru zachibadwa ndipo alibe Mzimu Woyera.

20Koma inu okondedwa, muthandizane kuti mukule pa chikhulupiriro chanu choyera, ndipo muzipemphera ndi mphamvu ya Mzimu Woyera. 21Khalani mʼchikondi cha Mulungu pamene mukudikira chifundo cha Ambuye athu Yesu Khristu kuti akubweretsereni moyo wosatha.

22Muwachitire chifundo amene akukayika. 23Ena muwapulumutse powalanditsa ku moto. Enanso muwachitire chifundo, koma mwa mantha, ndipo muzidana ngakhale ndi mwinjiro yomwe yayipitsidwa ndi machimo.

Mawu Olemekeza Mulungu

24Kwa Iye amene angathe kukusungani kuti mungagwe mʼmachimo, ndiponso amene angathenso kukufikitsani pamaso pake pa ulemerero wopanda cholakwa muli okondwa, 25kwa Mulungu yekhayo, Mpulumutsi wathu, kwa Iye kukhale ulemerero, ukulu, mphamvu ndi ulamuliro, mwa Yesu Khristu Ambuye athu, kuyambira isanayambe nthawi, tsopano mpaka muyaya. Ameni.

New International Version – UK

Jude 1:1-25

1Jude, a servant of Jesus Christ and a brother of James,

To those who have been called, who are loved in God the Father and kept for1:1 Or by; or in Jesus Christ:

2Mercy, peace and love be yours in abundance.

The sin and doom of ungodly people

3Dear friends, although I was very eager to write to you about the salvation we share, I felt compelled to write and urge you to contend for the faith that was once for all entrusted to God’s holy people. 4For certain individuals whose condemnation was written about1:4 Or individuals who were marked out for condemnation long ago have secretly slipped in among you. They are ungodly people, who pervert the grace of our God into a licence for immorality and deny Jesus Christ our only Sovereign and Lord.

5Though you already know all this, I want to remind you that the Lord1:5 Some early manuscripts Jesus at one time delivered his people out of Egypt, but later destroyed those who did not believe. 6And the angels who did not keep their positions of authority but abandoned their proper dwelling – these he has kept in darkness, bound with everlasting chains for judgment on the great Day. 7In a similar way, Sodom and Gomorrah and the surrounding towns gave themselves up to sexual immorality and perversion. They serve as an example of those who suffer the punishment of eternal fire.

8In the very same way, on the strength of their dreams these ungodly people pollute their own bodies, reject authority and heap abuse on celestial beings. 9But even the archangel Michael, when he was disputing with the devil about the body of Moses, did not himself dare to condemn him for slander but said, ‘The Lord rebuke you!’1:9 Jude is alluding to the Jewish Testament of Moses (approximately the first century a.d.). 10Yet these people slander whatever they do not understand, and the very things they do understand by instinct – as irrational animals do – will destroy them.

11Woe to them! They have taken the way of Cain; they have rushed for profit into Balaam’s error; they have been destroyed in Korah’s rebellion.

12These people are blemishes at your love feasts, eating with you without the slightest qualm – shepherds who feed only themselves. They are clouds without rain, blown along by the wind; autumn trees, without fruit and uprooted – twice dead. 13They are wild waves of the sea, foaming up their shame; wandering stars, for whom blackest darkness has been reserved for ever.

14Enoch, the seventh from Adam, prophesied about them: ‘See, the Lord is coming with thousands upon thousands of his holy ones 15to judge everyone, and to convict all of them of all the ungodly acts they have committed in their ungodliness, and of all the defiant words ungodly sinners have spoken against him.’1:15 From the Jewish First Book of Enoch (approximately the first century b.c.) 16These people are grumblers and fault-finders; they follow their own evil desires; they boast about themselves and flatter others for their own advantage.

A call to persevere

17But, dear friends, remember what the apostles of our Lord Jesus Christ foretold. 18They said to you, ‘In the last times there will be scoffers who will follow their own ungodly desires.’ 19These are the people who divide you, who follow mere natural instincts and do not have the Spirit.

20But you, dear friends, by building yourselves up in your most holy faith and praying in the Holy Spirit, 21keep yourselves in God’s love as you wait for the mercy of our Lord Jesus Christ to bring you to eternal life.

22Be merciful to those who doubt; 23save others by snatching them from the fire; to others show mercy, mixed with fear – hating even the clothing stained by corrupted flesh.1:23 The Greek manuscripts of these verses vary at several points.

Doxology

24To him who is able to keep you from stumbling and to present you before his glorious presence without fault and with great joy – 25to the only God our Saviour be glory, majesty, power and authority, through Jesus Christ our Lord, before all ages, now and for evermore! Amen.