Yoweli 2 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yoweli 2:1-32

Chilango cha Mulungu

1Lizani lipenga mu Ziyoni.

Chenjezani pa phiri langa loyera.

Onse okhala mʼdziko anjenjemere,

pakuti tsiku la Yehova likubwera,

layandikira;

2tsiku la mdima ndi chisoni,

tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani.

Ngati mʼbandakucha umene wakuta mapiri,

gulu lalikulu ndi la ankhondo amphamvu likubwera,

gulu limene nʼkale lomwe silinaonekepo

ngakhale kutsogolo kuno silidzaonekanso.

3Patsogolo pawo moto ukupsereza,

kumbuyo kwawo malawi amoto akutentha zinthu.

Patsogolo pawo dziko lili ngati munda wa Edeni,

kumbuyo kwawo kuli ngati chipululu,

kulibe kanthu kotsalapo.

4Maonekedwe awo ali ngati akavalo;

akuthamanga ngati akavalo ankhondo.

5Akulumpha pamwamba pa mapiri

ndi phokoso ngati la magaleta,

ngati moto wothetheka wonyeketsa ziputu,

ngati gulu lalikulu la ankhondo lokonzekera nkhondo.

6Akangowaona, anthu a mitundu ina amazunzika mu mtima;

nkhope iliyonse imagwa.

7Amathamanga ngati ankhondo;

amakwera makoma ngati asilikali.

Onse amayenda pa mizere,

osaphonya njira yawo.

8Iwo sakankhanakankhana,

aliyense amayenda molunjika.

Amadutsa malo otchingidwa

popanda kumwazikana.

9Amakhamukira mu mzinda,

amathamanga mʼmbali mwa khoma.

Amakwera nyumba ndi kulowamo;

amalowera pa zenera ngati mbala.

10Patsogolo pawo dziko limagwedezeka,

thambo limanjenjemera,

dzuwa ndi mwezi zimachita mdima,

ndipo nyenyezi zimaleka kuwala.

11Yehova amabangula

patsogolo pawo,

gulu lake lankhondo ndi losawerengeka,

ndipo amphamvu ndi amene amamvera kulamula kwake.

Tsiku la Yehova ndi lalikulu;

ndi loopsa.

Ndani adzapirira pa tsikulo?

Ngʼambani Mtima Wanu

12“Ngakhale tsopano,

bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonse

posala zakudya ndi kukhetsa misozi,” akutero Yehova.

13Ngʼambani mtima wanu

osati zovala zanu.

Bwererani kwa Yehova Mulungu wanu,

pakuti Iye ndi wokoma mtima ndi wachifundo,

wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka,

ndipo amaleka kubweretsa mavuto.

14Akudziwa ndani? Mwina adzasintha maganizo nʼkutimvera chisoni,

nʼkutisiyira madalitso,

a chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa

kwa Yehova Mulungu wanu.

15Lizani lipenga mu Ziyoni,

lengezani tsiku losala zakudya,

itanitsani msonkhano wopatulika.

16Sonkhanitsani anthu pamodzi,

muwawuze kuti adziyeretse;

sonkhanitsani akuluakulu,

sonkhanitsani ana,

sonkhanitsani ndi oyamwa omwe.

Mkwati atuluke mʼchipinda chake,

mkwatibwi atuluke mokhala mwake.

17Ansembe amene amatumikira pamaso pa Yehova,

alire pakati pa guwa lansembe ndi khonde la Nyumba ya Yehova.

Azinena kuti, “Inu Yehova, achitireni chifundo anthu anu.

Musalole kuti cholowa chanu chikhale chinthu chonyozeka,

kuti anthu a mitundu ina awalamulire.

Kodi nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina amanena kuti,

‘Ali kuti Mulungu wawo?’ ”

Yankho la Yehova

18Pamenepo Yehova adzachitira nsanje dziko lake

ndi kuchitira chisoni anthu ake.

19Yehova adzawayankha kuti,

“Ine ndikukutumizirani tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta

ndipo mudzakhuta ndithu;

sindidzakuperekaninso kuti mukhale chitonzo

kwa anthu a mitundu ina.

20“Ine ndidzachotsa ankhondo akumpoto kuti apite kutali ndi inu,

kuwapirikitsira ku dziko lowuma ndi lachipululu,

gulu lawo lakutsogolo ndidzalipirikitsira ku nyanja ya kummawa

ndi gulu lawo lakumbuyo, ku nyanja ya kumadzulo.

Ndipo mitembo yawo idzawola,

fungo lake lidzamveka.”

Zoonadi Yehova wachita zinthu zazikulu.

21Iwe dziko usachite mantha;

sangalala ndipo kondwera.

Zoonadi Yehova wachita zinthu zazikulu.

22Inu nyama zakuthengo, musachite mantha,

pakuti msipu wa ku chipululu ukuphukira.

Mitengo ikubala zipatso zake;

mitengo ya mkuyu ndi mpesa ikubereka kwambiri.

23Inu anthu a ku Ziyoni sangalalani,

kondwerani mwa Yehova Mulungu wanu,

pakuti wakupatsani

mvula yoyambirira mwachilungamo chake.

Iye wakutumizirani mivumbi yochuluka,

mvula yoyambirira ndi mvula ya nthawi ya mphukira, monga poyamba paja.

24Pa malo opunthira padzaza tirigu;

mʼmitsuko mudzasefukira vinyo watsopano ndi mafuta.

25“Ine ndidzakubwezerani zonse zimene zinawonongedwa ndi dzombe,

dzombe lalikulu ndi dzombe lalingʼono,

dzombe lopanda mapiko ndi dzombe lowuluka;

gulu langa lalikulu la nkhondo limene ndinalitumiza pakati panu.

26Mudzakhala ndi chakudya chambiri, mpaka mudzakhuta,

ndipo mudzatamanda dzina la Yehova Mulungu wanu,

amene wakuchitirani zodabwitsa;

ndipo anthu anga sadzachitanso manyazi.

27Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndili mu Israeli,

kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu,

ndi kuti palibenso wina;

ndipo anthu anga sadzachitanso manyazi.

Tsiku la Yehova

28“Ndipo patapita nthawi,

ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse.

Ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenera,

nkhalamba zanu zidzalota maloto,

anyamata anu adzaona masomphenya.

29Ngakhalenso pa antchito anga aamuna ndi aakazi

ndidzakhuthulira Mzimu wanga masiku amenewo.

30Ndidzaonetsa zodabwitsa mlengalenga

ndi pa dziko lapansi,

ndizo magazi, moto ndi utsi watolotolo.

31Dzuwa lidzadetsedwa

ndipo mwezi udzaoneka ngati magazi

lisanafike tsiku lalikulu ndi loopsa la Ambuye.

32Ndipo aliyense amene adzayitana

pa dzina la Ambuye adzapulumuka;

pakuti chipulumutso chidzakhala pa Phiri la Ziyoni

ndi mu Yerusalemu,

monga Yehova wanenera,

pakati pa otsala

amene Yehova wawayitana.