Yoswa 8 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yoswa 8:1-35

Kuwonongedwa kwa Mzinda wa Ai

1Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, “Usachite mantha kapena kutaya mtima. Tenga gulu lonse la nkhondo, ndipo upite ku Ai. Taona, ndapereka mfumu ya Ai pamodzi ndi anthu ake, mzinda wake ndi dziko lake lonse mʼmanja mwako. 2Mzinda wa Ai ndi mfumu yake muchite monga munachita ndi mzinda wa Yeriko ndi mfumu yake, koma katundu wa mumzindamo ndi zoweta mukazitenge ndi kuzisunga kuti zikhale zanu. Mukalalire mzinda wa Ai ndi kuwuthira nkhondo kuchokera kumbuyo.”

3Kotero Yoswa ndi gulu lonse la nkhondo anakonzeka kupita ku Ai. Iye anasankha amuna 30,000 odziwa kumenya nkhondo bwino ndipo anawatumiza usiku 4nawapatsa malamulo awa kuti, “Mvetsani bwino; mukabisale kuseri kwa mzindawo. Musakapite patali ndi mzindawo, koma nonsenu mukakhale okonzekera nkhondo. 5Ine ndi gulu langa lonse tikayamba kuwuputa mzindawu, ndipo akadzangotuluka kudzalimbana nafe, ife tidzawathawa monga tinachitira poyamba. 6Iwo adzatithamangitsa mpaka titawakokera kutali ndi mzindawo, pakuti iwo adzati, ‘Akutithawa monga anachitira poyamba.’ Pamene ife tizidzathawa, 7inu mudzatuluke pamene mwabisalapo ndi kulanda mzindawo. Yehova Mulungu wanu adzakupatsani mzindawo. 8Mukakawulanda mzindawo mudzawuyatse moto. Mukachite monga mwa mawu a Yehova. Amenewa ndiwo malamulo amene ndakupatsani.”

9Yoswa atawatumiza, anapita ku malo wokabisalakowo ndipo anadikirira kumeneko. Malowa anali pakati pa Beteli ndi Ai, kumadzulo kwa Ai. Koma Yoswa anagona usiku umenewu pakati pa gulu lake lankhondo.

10Mmawa mwake, Yoswa anadzuka nayitana asilikali ake. Tsono iye pamodzi ndi akuluakulu a Aisraeli anatsogola kupita ku Ai. 11Gulu lonse la nkhondo limene linali ndi iye linatsogolako ndi kukamanga zithando pafupi ndi mzindawo chakumpoto mopenyana nawo. Pakati pa iwo ndi mzindawo panali chigwa. 12Yoswa anali atatenga asilikali 5,000 ndi kuwabisa pakati pa Ai ndi Beteli, kumadzulo kwa mzindawo. 13Anakhazika anthuwo mokonzekera nkhondo. Gulu lalikulu la nkhondo linakamanga zithando zawo kumpoto kwa mzinda, ndipo gulu lina linakamanga zithando zawo kumadzulo kwa mzindawo. Usiku umenewo Yoswa anakagona ku chigwa.

14Mfumu ya Ai itaona ankhondo a Yoswa, inachita zinthu mofulumira. Inadzuka mmamawa ndipo inapita pamodzi ndi anthu ake ku malo otsika oyangʼanana ndi Araba kuti akachite nkhondo ndi Aisraeli. Koma iyo sinadziwe kuti ayithira nkhondo kudzera kumbuyo kwa mzindawo. 15Yoswa ndi Aisraeli onse anachita ngati agonja ndi kumathawira ku chipululu. 16Anthu onse a ku Ai anawuzidwa kuti awapirikitse. Ndipo iwo anapirikitsadi Yoswa uja, ndi kupita kutali ndi mzinda wawo. 17Palibe munthu wamwamuna wa mzinda wa Ai kapena wa Beteli amene sanatuluke kukapirikitsa Aisraeli. Iwo anasiya mzinda wosatseka ndi kumapirikitsa Aisraeli.

18Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, “Loza mkondo uli mʼdzanja lako ku Ai pakuti ine ndipereka mʼdzanja lanu mzindawo.” Kotero Yoswa analoza mkondowo ku Ai. 19Atangotambalitsa dzanja lake, anthu amene anabisala aja ananyamuka msangamsanga pamalo pawo ndi kuthamangira kutsogolo. Iwo analowa mu mzindamo ndi kuwulanda ndipo anawutentha mofulumira.

20Anthu a ku Ai aja atangochewukira mʼmbuyo anaona utsi uli tolotolo. Koma mpata woti athawireko panalibe pakuti Aisraeli amene amathawira ku chipululu anabwerera nayamba kuwathamangitsa. 21Yoswa ndi Aisraeli onse ataona kuti obisalira aja alanda mzinda ndipo kuti utsi unali tolotolo, iwo anatembenuka ndi kuyamba kupha anthu a ku Ai. 22Nawonso Aisraeli amene anali mu mzindamo anatuluka kudzalimbana ndi anthu a ku Ai. Choncho iwo anazingidwa mbali zonse ndi Aisraeli ndipo onse anaphedwa. Palibe amene anatsala wamoyo kapena wothawa 23kupatula mfumu ya ku Ai yokha imene anayigwira nabwera nayo kwa Yoswa.

24Aisraeli aja atatha kupha anthu onse a ku Ai amene anali mʼthengo ndi mʼchipululu kumene anawapirikitsira, onse anabwerera ku Ai ndi kupha onse amene anali mu mzindamo. 25Chiwerengero cha anthu onse a ku Ai, amuna ndi akazi, amene anaphedwa pa tsiku limeneli chinali 12,000. 26Yoswa sanatsitse dzanja lake limene ananyamula mkondo mpaka ataona kuti onse amene amakhala mu mzinda wa Ai aphedwa. 27Tsono Aisraeli anatenga zoweta ndi katundu yense wa anthu ophedwa aja, monga momwe Yehova analamulira Yoswa.

28Pambuyo pake Yoswa anawutentha mzinda wa Ai ndi kuwusiya bwinja monga ulili leromu. 29Iye anapachika pa mtengo mfumu ya Ai ndipo anayisiya mpaka madzulo. Pomwe dzuwa linalowa Yoswa analamula kuti akachotse mtembowo ndi kukawutaya ku chipata cha mzindawo. Pamwamba pa mtembowo anawunjikapo mulu waukulu wa miyala. Muluwo ulipobe mpaka lero lino.

Kuchitanso Pangano pa Phiri la Ebala

30Ndipo Yoswa anamanga guwa lansembe la Yehova Mulungu wa Israeli pa phiri la Ebala. 31Analimanga motsata zimene Mose mtumiki wa Yehova analamulira Aisraeli, ndiponso potsata zomwe zinalembedwa mʼbuku la malamulo a Mose kuti guwa lansembe likhale la miyala yosasemedwa ndi chitsulo. Pa guwalo anapereka kwa Yehova nsembe yopsereza ndi nsembe yachiyanjano. 32Kenaka anthu onse akupenya, Yoswa analemba pa miyala chitsanzo cha malamulo amene Mose analemba. 33Aisraeli onse, akuluakulu awo, atsogoleri awo ndi oweruza awo, alendo pamodzi ndi mbadwa, anayimirira mbali zonse ziwiri za Bokosi la Chipangano la Yehova, ena uku ena uku moyangʼanana ndi ansembe a Chilevi. Theka la anthu linayima patsogolo pa phiri la Gerizimu ndipo theka lina patsogolo pa phiri la Ebala, monga momwe Mose mtumiki wa Yehova anawalamulira mʼmbuyomo pamene anawapatsa malangizo podalitsa Aisraeli.

34Pambuyo pake Yoswa anawerenga mawu onse a malamulo, madalitso ndi matemberero monga momwe zinalembedwera mʼbuku la malamulo a Mose. 35Yoswa anawerenga mawu onse amene Mose analamula, gulu lonse la Israeli limene linasonkhana likumva. Amayi, ana ndi alendo omwe okhala pakati pawo anali pomwepo.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

约书亚记 8:1-35

艾城之战

1耶和华对约书亚说:“不要害怕,也不用沮丧。只管率领全军去攻打城,我已经将城的王、他的人民、城池和土地都交在你手里了。 2你怎样对待耶利哥耶利哥王,也要照样对待城和城的王。不过你们可以拿去城中的财物和牲畜。你要在城后设下伏兵。”

3于是,约书亚率领全军前往城。他挑选了三万精兵,派他们在黑夜出发, 4并吩咐他们说:“你们要在城后埋伏,不可离城太远,要随时准备行动。 5我会率领军队正面攻城,当敌人像上次那样出城应战时,我们便逃跑。 6他们必定乘胜追击,我们便引他们离城,因为敌人一定会以为我们又像上次一样临阵逃跑。 7那时,你们便从埋伏的地方冲出来攻占城,你们的上帝耶和华一定会把城交在你们手里。 8你们攻陷城以后,要照耶和华的话放火焚城。这是我的命令。” 9于是,约书亚派遣他们出去。他们去埋伏在伯特利城之间,就是城的西面。那一夜,约书亚住在民众当中。

10第二天清早,约书亚召集民众,与以色列的众首领率领全军前往城。 11他们来到城外,在城的北面扎营,与城相隔一个山谷。 12约书亚选了五千人,让他们埋伏在城和伯特利之间,就是城的西面。 13于是,城北的主力军队和城西的伏兵都部署好了。当晚,约书亚在山谷里过夜。 14城的王见以色列人兵临城下,清早便急忙和全城的人起来出城迎战,在亚拉巴谷附近跟以色列军交锋,他不知道城后有伏兵。 15约书亚带领以色列军诈败,沿着通往旷野的路逃跑。 16城的人都被召去追赶以色列人,他们都被诱出城。 17这样,伯特利城的人倾巢而出,追杀以色列人,他们的城门大开。

18耶和华对约书亚说:“把你手中的矛指向城,因为我要将这城交在你手里。”约书亚就把手中的矛指向城。 19他一伸手,城后的伏兵立即行动,迅速冲进城去,一举占领城,并放火烧城。 20城的人回头发现城内烟气冲天,却无路可逃,因为那些诈败的以色列人已掉头攻击他们。 21约书亚和全军见伏兵已经占领城,城中浓烟滚滚,便掉头攻击城的人。 22伏兵也出城追击城的人。以色列军前后夹攻,把敌人围困在中间全部歼灭,无一漏网。 23他们生擒了城的王,将他押到约书亚那里。

24以色列军在田间和旷野杀尽了追赶他们的城人后,又进城杀了留在城里的人, 25当天被杀的城人男男女女共有一万二千人。 26一直到城所有的人都被杀光了,约书亚才收回手中的矛。 27以色列人照耶和华对约书亚的吩咐,只带走了城中的牲畜和财物。 28约书亚烧毁全城,使城永远成为一堆废墟,至今仍一片荒凉。 29约书亚又将城王的尸体挂在树上示众。黄昏时,他才吩咐人把尸体取下来丢在城门口,又在尸体上堆了一大堆石头。石堆至今还在。

重申律法

30-31约书亚照耶和华的仆人摩西在律法书上吩咐以色列人的话,用未经铁器凿过的完整石头,在以巴路山上为以色列的上帝耶和华筑了一座祭坛。以色列人就在这坛上把燔祭和平安祭献给耶和华。 32约书亚又在众人面前,将摩西所写的律法刻在石头上。 33所有的以色列人,无论本族人、外族人、长老、官员或审判官,都站在耶和华的约柜两旁,面对着抬约柜的利未祭司。照耶和华的仆人摩西从前祝福他们时的吩咐,他们一半人站在基利心山前,一半人站在以巴路山前。 34随后,约书亚向民众宣读记在摩西律法书上的一切祝福和咒诅。 35他在全体会众,包括妇女、小孩以及住在他们中间的外族人面前,一字不漏地宣读摩西的一切吩咐。