Yoswa 7 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yoswa 7:1-26

Tchimo la Akani

1Koma Aisraeli anachita zachinyengo ndi lamulo lija loti asatenge kalikonse koyenera kuwonongedwa. Akani mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda anatengako zinthu zina. Choncho Yehova anakwiyira Israeli kwambiri.

2Tsono Yoswa anatuma anthu kuchokera ku Yeriko kukazonda ku mzinda wa Ai umene uli pafupi ndi mzinda wa Beti-Aveni kummawa kwa Beteli, ndipo anawawuza kuti, “Pitani mukazonde chigawochi.” Anthuwo anapitadi kukazonda Ai.

3Atabwera kwa Yoswa, anamuwuza kuti, “Sikofunika kuti apite anthu onse kukathira nkhondo mzinda wa Ai. Mutumizeko anthu 2,000 kapena 3,000 kuti akatenge mzindawo. Musawatume anthu onse kumeneko popeza kuli anthu ochepa.” 4Choncho kunapita anthu 3,000. Koma iwo anathamangitsidwa ndi anthu a ku Ai. 5Anthu a ku Ai anathamangitsa Aisraeli kuchokera pa chipata cha mzindawo mpaka ku ngwenya ndipo anapha anthu 36. Iwowa anawapha pamene ankatsika phiri. Choncho mitima ya anthu inasweka ndipo analibenso mphamvu.

6Tsono Yoswa anangʼamba zovala zake nagwada nʼkuweramitsa mutu wake pansi patsogolo pa Bokosi la Yehova. Akuluakulu a Israeli nawonso anadzigwetsa pansi ndipo anakhala pomwepo mpaka madzulo atadziwaza fumbi kumutu kwawo. 7Ndipo Yoswa anati, “Kalanga ine, Ambuye Wamphamvuzonse chifukwa chiyani munatiwolotsa Yorodani? Kodi mumalinga zotipereka mʼmanja mwa Aamori kuti atiwononge chotere? Kukanakhala kwabwino ife tikanakhala tsidya linalo la Yorodani! 8Tsono Ambuye, ine ndinene chiyani, pakuti tsopano Israeli anathamangitsidwa ndi adani ake? 9Akanaani ndi anthu ena a dziko lino adzamva zimenezi ndipo adzatizinga ndi kutiwonongeratu. Nanga inu mudzatani ndi dzina lanu lamphamvulo?”

10Koma Yehova anati kwa Yoswa, “Imirira! Chifukwa chiyani wagwada pansi chotere? 11Aisraeli achimwa. Iwo aphwanya pangano limene ndinawalamula kuti asunge. Anatengako zinthu zina zofunika kuwonongedwa. Choncho anabako, ananena bodza ndi kuyika zinthu zakubazo pamodzi ndi katundu wawo. 12Nʼchifukwa chake Aisraeli sangathe kulimbana ndi adani awo. Iwo anathawa pamaso pa adani awo chifukwa ndiwo oyenera kuwonongedwa. Ine sindikhalanso ndi inu pokhapokha mutawononga chilichonse choyenera kuwonongedwa pakati panu.

13“Nyamuka, ukawawuze anthu kuti, ‘Mudzipatule nokha kukonzekera kuonana nane mawa; pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti choyenera kuwonongedwa chija chili pakati panu, inu Aisraeli. Simungathe kulimbana ndi adani anu mpaka mutachichotsa.’

14“Mawa mmamawa adzabwere pamaso pa Yehova fuko limodzilimodzi. Fuko limene Yehova adzaliloze lidzabwere patsogolo mbumba imodziimodzi. Tsono mbumba imene Yehova adzayiloze idzabwere patsogolo banja limodzilimodzi. Banja limene Yehova adzaliloze lidzabwere patsogolo munthu mmodzimmodzi. 15Iye amene adzagwidwe ndi zinthu zoyenera kuwonongedwazo adzawotchedwa ndi moto, pamodzi ndi banja lake lonse ndi zinthu zake zonse. Iyeyutu wachita chinthu chonyansa pakati pa Aisraeli ndi kuphwanya pangano limene anthu anga anachita ndi Ine!”

16Mmawa mwake Yoswa anabweretsa Israeli fuko limodzilimodzi ndipo fuko la Yuda linalozedwa. 17Anabweretsa poyera mbumba zonse za fuko la Yuda, ndipo mbumba ya Zera inagwidwa. Kenaka anatulutsa poyera mabanja onse a mbumba ya Zera ndipo banja la Zabidi linagwidwa. 18Potsiriza anatulutsa anthu onse a banja la Zabidi ndipo Akani anagwidwa. Iyeyu anali mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera wa fuko la Yuda.

19Ndipo Yoswa anati kwa Akani, “Mwana wanga pereka ulemerero kwa Yehova Mulungu wa Israeli ndipo umuyamike Iye. Ndiwuze zimene wachita, ndipo usandibisire.”

20Akani anayankha kuti, “Zoona! Ine ndachimwira Yehova Mulungu wa Israeli. Chimene ndachita ine ndi ichi: 21Ndinaona mwa zinthu zolanda ku nkhondo zija, mkanjo wokongola wa ku Babuloni, makilogalamu awiri a siliva ndiponso golide wolemera theka la kilogalamu. Zimenezi ndinazikhumba ndipo ndinazitenga. Ndazibisa mʼkati mwa tenti yanga, ndipo siliva ali pansi pake.”

22Motero Yoswa anatuma anthu, ndipo anathamanga kupita ku tenti. Anthuwo anakapeza kuti zinthuzo zinabisidwadi mʼtenti yake, ndipo siliva analidi pansi pake. 23Iwo anazichotsa zinthuzo mu tenti yake nabwera nazo kwa Yoswa ndi kwa Aisraeli onse ndipo anaziyika pamaso pa Yehova.

24Kenaka Yoswa pamodzi ndi Aisraeli onse anatenga Akani mwana wa Zera pamodzi ndi siliva, mkanjo, golide zimene anapezeka nazo zija. Anatenganso ana ake aamuna ndi aakazi, ngʼombe zake, abulu ndi nkhosa, tenti yake ndi zonse anali nazo, kupita nazo ku chigwa cha Akori. 25Yoswa anati “Chifukwa chiyani wabweretsa mavuto awa pa ife? Yehova ndiye abweretse mavuto pa iwe lero.”

Kenaka Aisraeli onse anaponya miyala Akani, namupha. Anaponyanso miyala banja lake lonse, nʼkulipha. Pambuyo pake anatentha Akani uja, banja lake ndi zonse zimene anali nazo. 26Anawunjika mulu waukulu wa miyala pa Akani, imene ilipobe mpaka lero. Nʼchifukwa chake malowa amatchedwa chigwa cha Akori mpaka lero. Ndipo Yehova anachotsa mkwiyo wake.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

约书亚记 7:1-26

亚干犯罪

1以色列人在当毁灭之物的事上犯了罪。因为犹大支派中谢拉的曾孙、撒底的孙子、迦米的儿子亚干拿了一些本该毁灭的东西,耶和华便向以色列人发怒。

2当时,约书亚耶利哥派人去侦察伯特利东边靠近伯·亚文城。 3他们侦察回来后对约书亚说:“那里的居民很少,我们不必劳师动众派所有的人上去,只要派两三千人上去便可以攻取城。” 4于是,大约有三千以色列人去攻打城,不料却被城人击溃。 5城的人杀了他们三十六人,从城门前追杀他们,一直到示巴琳,在下坡处杀败他们。以色列人吓得心惊胆战。

6约书亚以色列的长老便撕裂衣服,把灰撒在头上,俯伏在耶和华的约柜面前,直到晚上。 7约书亚说:“唉!主耶和华啊,你让我们过了约旦河,为什么把我们交在亚摩利人手上,让他们毁灭我们呢?倒不如让我们住在约旦河对岸! 8主啊,现在以色列人被仇敌打败,我还有什么话可说呢? 9迦南人和这一带的人听到这消息以后,必从四面八方来围攻我们,将我们从地上斩尽杀绝。那时候,你的威名又何在呢?”

10耶和华对约书亚说:“起来吧!你为何俯伏在地? 11以色列人犯了罪,违背了我吩咐他们应守的约,偷拿了本该毁灭的东西放在自己的行囊里,还撒谎。 12所以,以色列人受咒诅,无法抵挡敌人,掉头败逃。你必须将那些本该毁灭的东西从你们中间除掉,不然我就不再与你们同在。 13起来吧!去吩咐民众洁净自己,让他们为明天洁净自己,因为以色列的上帝耶和华这样说,‘以色列啊!你们中间有本该毁灭的东西,你们不除掉这些东西就无法抵挡敌人。 14明天早上,你们要按支派一个一个前来,耶和华指出哪个支派,哪支派的各宗族便要前来。耶和华指出哪个宗族,哪宗族的各家族便要前来。耶和华指出哪个家族,哪家族的各成员便要前来。 15哪个人被指出拿了本该毁灭的东西,哪个人及其所有的东西就要被火焚烧。因为他违背了耶和华的约,在以色列人中做了可耻的事。’”

16第二天清早,约书亚按照支派召来以色列人,结果抽中犹大支派; 17他让犹大支派各宗族前来,结果抽中谢拉宗族;他让谢拉宗族前来,结果抽中撒底家族; 18他让撒底家族的人一个一个前来,结果抽中迦米的儿子亚干19约书亚亚干说:“孩子啊,我劝你把荣耀归给以色列的上帝耶和华,向祂认罪,把你所做的事告诉我,不要隐瞒。” 20亚干答道:“我的确得罪了以色列的上帝耶和华。事情是这样的, 21在夺得的财物中,我看上了一件漂亮的示拿外衣、两千二百克银子和五百五十克金子,我一时贪心便拿去了,藏在我帐篷的地底下,银子就放在衣服下面。”

22约书亚派人跑到他的帐篷里,果然在那里找到了那件衣服和衣服下面的银子。 23他们将这些东西带到约书亚和民众那里,摆在耶和华面前。 24约书亚和全体以色列人把谢拉家族的亚干、那些银子、衣服和金子及其儿女、牛、驴、羊、帐篷和一切所有都带到亚割谷。 25约书亚亚干说:“你为什么给我们惹祸呢?今天耶和华要降祸给你。”于是,以色列人便拿石头打死了他和他一切的人畜,将其烧毁。 26他们在亚干身上堆起一大堆石头,那些石头今天还在。耶和华这才息怒,因此那地方至今还叫亚割7:26 亚割”意思是“连累”。谷。