Yoswa 22 – CCL & KJV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yoswa 22:1-34

Mafuko a Kummawa Abwerera Kwawo

1Pambuyo pake Yoswa anayitanitsa fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase, 2ndipo anawawuza kuti, “Inu mwachita zonse zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulani, ndipo mwamvera mu zonse zimene ndinakulamulirani. 3Aisraeli anzanu simunawasiye nthawi yayitali yonseyi mpaka lero lino. Inu mwaonetsetsa kuti mwachita zonse zimene Yehova anakulamulani. 4Tsono pakuti Yehova Mulungu wanu wapereka mpumulo kwa abale anu monga anayankhulira nawo, bwererani ku nyumba zanu ku dziko limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani, dziko limene lili pa tsidya la Yorodani kummawa. 5Koma samalitsani kuti mumvere malamulo ndi malangizo amene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani: kukonda Yehova Mulungu wanu, kuchita zimene iye amafuna, kumvera malamulo ake, kukhala okhulupirika kwa Iye ndi kumutumikira ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.”

6Ndipo Yoswa anawadalitsa ndi kuwalola kuti apite ndipo anapitadi ku nyumba zawo. 7Apa nʼkuti Mose atapereka dziko la Basani ku theka lina la fuko la Manase. Koma theka lina la fuko la Manase Yoswa analipatsa dziko la kumadzulo kwa Yorodani pamodzi ndi abale awo onse. Pamene Yoswa ankawatumiza kwawo anthu amenewa, anawadalitsa, 8nawawuza kuti, “Mukubwerera kwanu ndi chuma chambiri. Muli ndi ngʼombe zambiri pamodzi ndi siliva, golide, mkuwa ndi chitsulo, ndiponso zovala zambiri. Izi zimene munafunkha kwa adani anu agawireni abale anu.”

9Choncho mafuko a Rubeni, Gadi, pamodzi ndi theka la fuko la Manase anabwerera kwawo. Aisraeli ena onse anawasiya ku Silo mʼdziko la Kanaani. Tsono anapita ku dziko la Giliyadi, dziko limene linali lawo popeza analilandira potsata malamulo a Yehova kudzera mwa Mose.

10Atafika ku Geliloti, malo amene ali mʼmbali mwa mtsinje wa Yorodani mʼdziko la Kanaani, fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase anamanga guwa lansembe lalikulu pamenepo. 11Ndipo pamene Aisraeli ena onse anawuzidwa kuti anthu a fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase amanga guwa lansembe mʼmalire a Kanaani ku Geliloti, ku tsidya lathu lino la Yorodani, 12gulu lonse la Aisraeli linasonkhana ku Silo kuti lipite kukachita nawo nkhondo.

13Choncho Aisraeli anatumiza Finehasi mwana wa wansembe, Eliezara ku dziko la Giliyadi kwa mafuko a Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase. 14Pamodzi ndi Finehasiyo anatumiza akuluakulu khumi ochokera ku fuko lililonse la Aisraeli. Aliyense mwa akuluakulu amenewa anali mtsogoleri wa banja limodzi la mafuko a Aisraeli.

15Atafika ku Giliyadi anawuza fuko la Rubeni, Gadi ndi theka lija la fuko la Manase kuti, 16“Gulu lonse likukufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mwachita chinthu chonyansa chotere potsutsana ndi Mulungu wa Israeli? Nʼchifukwa chiyani mwapatuka ndi kuleka kutsata Yehova podzimangira nokha guwa lansembe? Mwapandukiratu Yehova! 17Kodi tchimo lija la ku Peori ndi lochepa kwa inu? Paja Yehova analanga gulu lonse ndi mliri chifukwa cha tchimolo, ndipo mpaka lero tchimo limene lija tikanazunzika nalobe. 18Kodi inu tsono mufuna kupatuka kuleka kumutsata Yehova?

“ ‘Ngati lero mumupandukira Yehovayo, ndiye kuti mawamawali Iye adzakwiyira gulu lonse wa Israeli. 19Ngati dziko limene inu mwatenga ndi loyipitsidwa, bwerani ku dziko la Yehova kumene kuli chihema chake kuja, ndipo mukhale nafe limodzi. Koma inu musawukire Yehova kapena kutisandutsa ife kukhala opanduka podzimangira guwa lansembe, kuwonjezera pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu. 20Kumbukirani pamene Akani mwana wa Zera anakana kumvera lamulo la zinthu zoyenera kuwonongedwa, kodi suja mkwiyo wa Yehova unagwera gulu lonse la Israeli? Akaniyo sanafe yekha chifukwa cha tchimo lakelo.’ ”

21Tsono mafuko a Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase anawayankha atsogoleri a mabanja a Israeli aja kuti, 22“Wamphamvu uja, Mulungu ndiye Yehova! Wamphamvu uja Mulungu ndiye Yehova. Iyeyu ndiye akudziwa chifukwa chiyani tinachita zimenezi. Tikufunanso kuti inu mudziwe. Ngati tinachita izi mopandukira ndiponso moonetsa kusakhulupirira Yehova, lero lomwe lino musatisiye ndi moyo. 23Ngati tinapandukira Yehova ndi kuleka kumutsata pamene tinadzimangira guwa loti tizipserezerapo nsembe kapena kupereka nsembe zaufa, kapena nsembe za mtendere, Yehova yekha ndiye atilange.

24“Ayi! Ife tinachita izi kuopa kuti tsiku lina zidzukulu zanu zingadzanene kwa zidzukulu zathu kuti, ‘Kodi inu mukufuna chiyani kwa Yehova Mulungu wa Israeli? 25Yehova anayika mtsinje wa Yorodani kukhala malire pakati pa ife ndi inu, anthu a fuko la Rubeni ndi Gadi. Inuyo mulibe gawo mwa Yehova.’ Tsono mwina zidzukulu zanuzo nʼkudzaletsa zathu kupembedza Yehova.

26“Nʼchifukwa chake tinaganiza kuti, ‘Tiyeni timange guwa lansembe, koma osati kuti tiziperekapo nsembe zopsereza kapena zopereka.’ 27Koma mosiyana ndi zimenezi, guwali likhale umboni pakati pa ife ndi inu ndiponso mibado imene ikubwerayo, kuti ife timapembedzanso Yehova ndi nsembe zathu zopsereza, zopereka, ndiponso nsembe za mtendere. Motero mʼtsogolo muno zidzukulu zanu sizidzatha kunena kwa zidzukulu zathu kuti, ‘Inu mulibe gawo mwa Yehova!’

28“Ndipo ife tinati kuti, ‘Ngati iwo adzatiyankhulira kapena kuyankhulira zidzukulu zathu motero mʼtsogolo muno, ife tidzayankha kuti, onani guwa lansembe, lofanana ndi lomwe makolo athu anamanga osati loperekerapo nsembe zopsereza kapena nsembe zina koma ngati umboni pakati pa inu ndi ife.’

29“Sizingatheke konse kuti ife lero nʼkupandukira Yehova. Ife sitingapatuke kuleka kumutsata Yehova ndi kumanga guwa lina la nsembe zopsereza, nsembe za zakudya, ndi nsembe zina zopikisana ndi guwa la Yehova, Mulungu wathu limene lili patsogolo pa Hema ya Yehova mʼmene amakhalamo.”

30Tsono Finehasi wansembe ndi atsogoleri a gululo amene anali naye atamva zimene anthu a fuko la Rubeni, Gadi ndi theka lakummawa la fuko la Manase ananena, anakondwera kwambiri. 31Ndipo Finehasi wansembe, mwana wa Eliezara anati kwa mafuko a Rubeni, Gadi ndi Manase, “Lero tadziwa kuti Yehova ali nafe chifukwa zimene mwachitazi simunawukire nazo Yehova. Inu mwapulumutsa Aisraeli onse ku chilango cha Yehova.”

32Ndipo Finehasi mwana wa wansembe Eliezara, pamodzi ndi atsogoleriwo anachoka ku Giliyadi nasiya anthu a fuko la Rubeni ndi Gadi nabwerera ku Kanaani kwa Aisraeli anzawo, ndipo anakafotokoza zonsezi. 33Mawu amenewa anakondweretsa Aisraeli onse ndipo anayamika Mulungu. Choncho sanakambenso zopita ku nkhondo kukawononga dziko limene Arubeni ndi Agadi ankakhalamo.

34Arubeni ndi Agadi anatcha guwalo kuti Mboni: Mboni pakati pathu kuti Yehova ndi Mulungu.

King James Version

Joshua 22:1-34

1Then Joshua called the Reubenites, and the Gadites, and the half tribe of Manasseh, 2And said unto them, Ye have kept all that Moses the servant of the LORD commanded you, and have obeyed my voice in all that I commanded you: 3Ye have not left your brethren these many days unto this day, but have kept the charge of the commandment of the LORD your God. 4And now the LORD your God hath given rest unto your brethren, as he promised them: therefore now return ye, and get you unto your tents, and unto the land of your possession, which Moses the servant of the LORD gave you on the other side Jordan. 5But take diligent heed to do the commandment and the law, which Moses the servant of the LORD charged you, to love the LORD your God, and to walk in all his ways, and to keep his commandments, and to cleave unto him, and to serve him with all your heart and with all your soul. 6So Joshua blessed them, and sent them away: and they went unto their tents.

7¶ Now to the one half of the tribe of Manasseh Moses had given possession in Bashan: but unto the other half thereof gave Joshua among their brethren on this side Jordan westward. And when Joshua sent them away also unto their tents, then he blessed them, 8And he spake unto them, saying, Return with much riches unto your tents, and with very much cattle, with silver, and with gold, and with brass, and with iron, and with very much raiment: divide the spoil of your enemies with your brethren.

9¶ And the children of Reuben and the children of Gad and the half tribe of Manasseh returned, and departed from the children of Israel out of Shiloh, which is in the land of Canaan, to go unto the country of Gilead, to the land of their possession, whereof they were possessed, according to the word of the LORD by the hand of Moses.

10¶ And when they came unto the borders of Jordan, that are in the land of Canaan, the children of Reuben and the children of Gad and the half tribe of Manasseh built there an altar by Jordan, a great altar to see to.

11¶ And the children of Israel heard say, Behold, the children of Reuben and the children of Gad and the half tribe of Manasseh have built an altar over against the land of Canaan, in the borders of Jordan, at the passage of the children of Israel. 12And when the children of Israel heard of it, the whole congregation of the children of Israel gathered themselves together at Shiloh, to go up to war against them. 13And the children of Israel sent unto the children of Reuben, and to the children of Gad, and to the half tribe of Manasseh, into the land of Gilead, Phinehas the son of Eleazar the priest, 14And with him ten princes, of each chief house a prince throughout all the tribes of Israel; and each one was an head of the house of their fathers among the thousands of Israel.22.14 chief…: Heb. house of the father

15¶ And they came unto the children of Reuben, and to the children of Gad, and to the half tribe of Manasseh, unto the land of Gilead, and they spake with them, saying, 16Thus saith the whole congregation of the LORD, What trespass is this that ye have committed against the God of Israel, to turn away this day from following the LORD, in that ye have builded you an altar, that ye might rebel this day against the LORD? 17Is the iniquity of Peor too little for us, from which we are not cleansed until this day, although there was a plague in the congregation of the LORD, 18But that ye must turn away this day from following the LORD? and it will be, seeing ye rebel to day against the LORD, that to morrow he will be wroth with the whole congregation of Israel. 19Notwithstanding, if the land of your possession be unclean, then pass ye over unto the land of the possession of the LORD, wherein the LORD’s tabernacle dwelleth, and take possession among us: but rebel not against the LORD, nor rebel against us, in building you an altar beside the altar of the LORD our God. 20Did not Achan the son of Zerah commit a trespass in the accursed thing, and wrath fell on all the congregation of Israel? and that man perished not alone in his iniquity.

21¶ Then the children of Reuben and the children of Gad and the half tribe of Manasseh answered, and said unto the heads of the thousands of Israel, 22The LORD God of gods, the LORD God of gods, he knoweth, and Israel he shall know; if it be in rebellion, or if in transgression against the LORD, (save us not this day,) 23That we have built us an altar to turn from following the LORD, or if to offer thereon burnt offering or meat offering, or if to offer peace offerings thereon, let the LORD himself require it; 24And if we have not rather done it for fear of this thing, saying, In time to come your children might speak unto our children, saying, What have ye to do with the LORD God of Israel?22.24 In time…: Heb. To morrow 25For the LORD hath made Jordan a border between us and you, ye children of Reuben and children of Gad; ye have no part in the LORD: so shall your children make our children cease from fearing the LORD. 26Therefore we said, Let us now prepare to build us an altar, not for burnt offering, nor for sacrifice: 27But that it may be a witness between us, and you, and our generations after us, that we might do the service of the LORD before him with our burnt offerings, and with our sacrifices, and with our peace offerings; that your children may not say to our children in time to come, Ye have no part in the LORD. 28Therefore said we, that it shall be, when they should so say to us or to our generations in time to come, that we may say again, Behold the pattern of the altar of the LORD, which our fathers made, not for burnt offerings, nor for sacrifices; but it is a witness between us and you. 29God forbid that we should rebel against the LORD, and turn this day from following the LORD, to build an altar for burnt offerings, for meat offerings, or for sacrifices, beside the altar of the LORD our God that is before his tabernacle.

30¶ And when Phinehas the priest, and the princes of the congregation and heads of the thousands of Israel which were with him, heard the words that the children of Reuben and the children of Gad and the children of Manasseh spake, it pleased them.22.30 pleased…: Heb. was good in their eyes 31And Phinehas the son of Eleazar the priest said unto the children of Reuben, and to the children of Gad, and to the children of Manasseh, This day we perceive that the LORD is among us, because ye have not committed this trespass against the LORD: now ye have delivered the children of Israel out of the hand of the LORD.22.31 now: Heb. then

32¶ And Phinehas the son of Eleazar the priest, and the princes, returned from the children of Reuben, and from the children of Gad, out of the land of Gilead, unto the land of Canaan, to the children of Israel, and brought them word again. 33And the thing pleased the children of Israel; and the children of Israel blessed God, and did not intend to go up against them in battle, to destroy the land wherein the children of Reuben and Gad dwelt. 34And the children of Reuben and the children of Gad called the altar Ed: for it shall be a witness between us that the LORD is God.22.34 Ed: that is, A witness