Yoswa 19 – CCL & CARSA

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yoswa 19:1-51

Dziko la Simeoni

1Maere achiwiri anagwera mabanja a fuko la Simeoni. Dziko lawo linali mʼkati mwenimweni mwa dziko la Yuda. 2Dzikolo linaphatikiza zigawo izi:

Beeriseba (ndi Seba), Molada, 3Hazari-Suwali, Bala, Ezemu, 4Elitoladi, Betuli, Horima, 5Zikilagi, Beti-Marikaboti, Hazari-Susa, 6Beti-Lebaoti ndi Saruheni. Yonse pamodzi inali mizinda 13 ndi midzi yawo.

7Panalinso mizinda inayi iyi: Aini, Rimoni, Eteri ndi Asani pamodzi ndi midzi yawo. 8Dzikolo linaphatikizanso midzi yonse yozungulira mizinda imeneyi mpaka ku Baalati-Beeri, ndiye kuti Rama wa kummwera.

Ili ndi dziko limene mabanja a fuko la Simeoni analandira kukhala lawo. 9Cholowa cha fuko la Simeoni chinatengedwa kuchokera ku gawo la Yuda chifukwa fuko la Yuda linali lalikulu kwambiri. Izi zinachititsa fuko la Simeoni kukhala mʼkati mwenimweni mwa dziko la Yuda.

Dziko la Zebuloni

10Maere achitatu anagwera mabanja a fuko la Zebuloni:

Malire a dziko lawo anafika mpaka ku Saridi. 11Malirewo anakwera kupita cha kumadzulo ku Marala nakafika ku Dabeseti ndi ku mtsinje wa kummawa kwa Yokineamu. 12Kuchokera ku mbali ina ya Saridi malire anakhota kupita kummawa ku malire a Kisiloti-Tabori mpaka ku Daberati nakwera mpaka ku Yafiya. 13Kuchokera kumeneko anabzola kulowa cha kummawa mpaka ku Gati-Heferi ndi ku Eti Kazini ndi kumaloza ku Neya njira ya ku Rimoni. 14Mbali ya kumpoto malirewo analoza ku Hanatoni ndipo anakathera ku chigwa cha Ifita Eli. 15Anaphatikizapo Katati, Nahalala, Simironi, Idala ndi Betelehemu. Mizinda yonse inakwana khumi ndi iwiri pamodzi ndi midzi yake.

16Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yake ndi imene mabanja a fuko la Zebuloni analandira.

Dziko la Isakara

17Maere achinayi anagwera mabanja a fuko la Isakara. 18Dziko lawo linaphatikiza zigawo izi:

Yezireeli, Kesuloti, Sunemu, 19Hafaraimu, Sioni, Anaharati, 20Rabiti, Kisoni, Ebezi, 21Remeti, Eni Ganimu, Eni Hada ndi Beti-Pazezi. 22Malirewa anakafikanso ku Tabori, Sahazuma ndi Beti-Semesi ndipo anakathera ku Yorodani. Mizinda yonse inalipo 16 ndi midzi yake.

23Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yake ndiyo inali cholowa cha mabanja a fuko la Isakara.

Dziko la Aseri

24Maere achisanu anagwera mabanja a fuko la Aseri. 25Gawo lawo linaphatikiza

Helikati, Hali, Beteni, Akisafu, 26Alameleki, Amadi ndi Misali. Kumadzulo malire anafika ku Karimeli ndi Sihori Libinati. 27Kenaka anakhotera kummawa kulowera ku Beti-Dagoni nafika ku dziko la Zebuloni ndi ku chigwa cha Ifita Eli, ndipo anapita kumpoto ku Beti-Emeki ndi Neieli. Anapitirirabe kumpoto mpaka kukafika ku Kabuli, 28Ebroni, Rehobu, Hamoni, ndi Kana, mpaka ku Sidoni Wamkulu. 29Kenaka malirewo anakhotera ku Rama ndi kupita ku mzinda wotetezedwa wa ku Turo. Kuchokera pamenepo malirewo anakhota kupita ku Hosa nakatulukira ku Nyanja, mʼchigawo cha Akizibu, 30Uma, Afeki ndi Rehobu. Mizinda yonse inalipo 22 pamodzi ndi midzi yake.

31Mizinda yonseyi pamodzi ndi midzi yake ndiyo inali cholowa cha mabanja a fuko la Aseri.

Dziko la Nafutali

32Maere achisanu ndi chimodzi anagwera mabanja a fuko la Nafutali.

33Malire awo anayambira ku Helefu mpaka ku mtengo wa thundu wa ku Zaananimu, ndipo anapitirira nʼkukafika ku Adami Nekebu, Yabineeli mpaka ku Lakumi ndi kukathera ku Yorodani. 34Tsono malirewo anakhotera kumadzulo kupita ku Azinoti-Tabori. Kuchoka kumeneko anapita ku Hukoki, modutsa Zebuloni cha kummwera, Aseri cha kumadzulo ndi mtsinje wa Yorodani cha kummawa. 35Mizinda yotetezedwa inali Zidimi, Zeri, Hamati, Rakati, Kinereti, 36Adama, Rama, Hazori, 37Kedesi, Ederi, Eni Hazori, 38Yironi, Migidali Eli, Horemu, Beti-Anati ndi Beti-Semesi. Yonse pamodzi inalipo mizinda 19 ndi midzi yake.

39Mizinda yonseyi pamodzi ndi midzi yawo ndiyo inali cholowa cha mabanja a fuko la Nafutali.

Dziko la Dani

40Maere achisanu ndi chiwiri anagwera mabanja a fuko la Dani. 41Gawo lawo linaphatikiza mizinda iyi:

Zora, Esitaoli, Iri Semesi, 42Saalabini, Ayaloni, Itira, 43Eloni, Timna, Ekroni, 44Eliteke, Gibetoni, Baalati, 45Yehudi, Beni Beraki, Gati-Rimoni, 46Me-Yarikoni ndi Rakoni, pamodzi ndi dera loyangʼanana ndi Yopa.

47Anthu a fuko la Dani atalandidwa dziko lawo, anapita kukathira nkhondo Lesemu. Iwo anapha anthu ake onse, nawulandiratu mzindawo, kuwusandutsa wawo ndi kumakhalamo. Tsono anatcha mzindawo dzina loti Dani popeza ndilo linali dzina la kholo lawo.

48Mizinda yonseyi pamodzi ndi midzi yake ndiyo inali cholowa cha mabanja a fuko la Dani.

Dziko la Yoswa

49Atatha kugawana zigawo zosiyanasiyana za dzikolo, Aisraeli anamupatsa Yoswa mwana wa Nuni chigawo chake. 50Potsata zimene Yehova anawalamula, anamupatsa mzinda wa Timnati-Sera umene anawupempha. Mzindawu unali mʼdziko lamapiri la Efereimu. Iye anawumanga mzindawu ndi kukhazikikako.

51Wansembe Eliezara, Yoswa ndi atsogoleri a mabanja onse a Israeli anagawa dziko lija zigawozigawo pogwiritsa ntchito maere pamaso pa Yehova. Izi zinachitika ku Silo pa khomo la tenti ya msonkhano. Choncho anamaliza kugawa dzikolo.

Священное Писание (Восточный перевод), версия с «Аллахом»

Иешуа 19:1-51

Надел Шимона

(1 Лет. 4:28-33)

1Второй жребий выпал кланам рода Шимона. Его надел находился среди земель Иуды. 2В него входили:

Беэр-Шева (или Шева), Молада, 3Хацар-Шуал, Бала, Эцем, 4Элтолад, Бетул, Хорма, 5Циклаг, Бет-Маркавот, Хацар-Суса, 6Бет-Леваот и Шарухен – тринадцать городов с окрестными поселениями;

7Аин, Риммон, Этер и Ашан – четыре города с окрестными поселениями, 8и также все другие поселения вокруг этих городов до самого Баалат-Беэра (Рама, что в Негеве).

Таким был надел рода шимонитов, по кланам. 9Надел шимонитов был взят из доли Иуды, потому что земля Иуды была для него слишком велика. Так шимониты получили свой надел в землях Иуды.

Надел Завулона

10Третий жребий выпал роду Завулона, по кланам:

Граница его надела простиралась до Сарида. 11На запад она шла до Маралы, примыкала к Даббешету и тянулась до реки, которая рядом с Иокнеамом. 12От Сарида она поворачивала на восток, к восходу солнца, к землям Кислот-Фавора, тянулась до Даверата и поднималась к Иафие. 13Затем она шла на восток к Гат-Хеферу и Ет-Кацину, тянулась к Риммону и поворачивала к Нее. 14Там граница сворачивала на север к Ханнатону и заканчивалась в долине Ифтах-Ил. 15В надел входили Каттат, Нахалал, Шимрон, Идала и Вифлеем. Всего – двенадцать городов с окрестными поселениями.

16Эти города с окрестными поселениями были наделом рода Завулона, по кланам.

Надел Иссахара

17Четвёртый жребий выпал роду Иссахара, по кланам:

18В его земли входили: Изреель, Кесуллот, Шунем, 19Хафараим, Шион, Анахарат, 20Раббит, Кишион, Эвец, 21Ремет, Ен-Ганним, Ен-Хадда и Бет-Пацец. 22Граница примыкала к Фавору, Шахацуме и Бет-Шемешу и заканчивалась у Иордана. Всего – шестнадцать городов с окрестными поселениями.

23Эти города с окрестными поселениями были наделом рода Иссахара, по кланам.

Надел Ашира

24Пятый жребий выпал роду Ашира, по кланам. 25В его земли входили:

Хелкат, Хали, Бетен, Ахшаф, 26Аллам-Малик, Амад и Мишал. На западе граница примыкала к Кармилу и к Шихор-Ливнату. 27Затем она поворачивала на восток к Бет-Дагону, примыкала к земле Завулона и долине Ифтах-Ил и шла на север к Бет-Емеку и Неиилу, проходя слева от Кавула. 28Она шла к Авдону, Рехову, Хаммону и Кане до великого Сидона. 29Затем граница поворачивала назад к Раме и шла к укреплённому городу Тиру, сворачивала к Хосе и оканчивалась у моря. Мехевел, Ахзив, 30Умма, Афек и Рехов. Всего – двадцать два города с окрестными поселениями.

31Эти города с окрестными поселениями были наделом рода Ашира, по кланам.

Надел Неффалима

32Шестой жребий выпал роду Неффалима, по кланам:

33Его граница шла от Хелефа и великого дерева в Цаананниме, пересекала Адами-Некев и Иавнеил до Лаккума и оканчивалась у Иордана. 34Граница поворачивала на запад к Азнот-Фавору и шла оттуда к Хуккоку, примыкая на юге к землям Завулона, к землям Ашира на западе и Иордану19:34 Или: «…западе, и к землям Иуды, Иордану». на востоке. 35Укреплёнными городами были Циддим, Цер, Хаммат, Раккат, Киннерет, 36Адама, Рама, Хацор, 37Кедеш, Эдреи, Ен-Хацор, 38Иреон, Мигдал-Ил, Хорем, Бет-Анат и Бет-Шемеш. Всего – девятнадцать городов с окрестными поселениями.

39Эти города с окрестными поселениями были наделом рода Неффалима, по кланам.

Надел Дана

40Седьмой жребий выпал роду Дана, по кланам. 41В земли его надела входили:

Цора, Эштаол, Ир-Шемеш, 42Шаалаббин, Аялон, Итла, 43Елон, Тимна, Экрон, 44Элтеке, Гиббетон, Баалат, 45Иехуд, Бене-Берак, Гат-Риммон, 46Ме-Иаркон и Раккон с областью, что напротив Иоппии.

Когда данитяне потеряли свою землю19:46 См. Суд. 1:34-35., 47они пошли и напали на Лаиш19:47 Букв.: «Лешем» – вариант названия Лаиш (см. Суд. 18:27-29).. Взяв город и предав его мечу, они заняли его. Они поселились в Лаише и назвали его Дан, в честь своего предка.

48Эти города с окрестными поселениями были наделом рода Дана, по кланам.

Надел Иешуа

49Закончив делить землю на наделы, исраильтяне дали среди себя надел Иешуа, сыну Нуна, 50как повелел Вечный. Они дали ему город, который он просил, – Тимнат-Серах в нагорьях Ефраима. Он отстроил город и поселился в нём.

51Таковы земли, которые священнослужитель Элеазар, Иешуа, сын Нуна, и главы семейств из родов Исраила раздали по жребию в Шило перед Вечным, у входа в шатёр встречи. И на этом они закончили делить землю.