Yoswa 18 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yoswa 18:1-28

Kugawa kwa Madera Otsala a Dziko

1Atagonjetsa dziko lonse Aisraeli anasonkhana ku Silo ndipo anayimikako tenti ya msonkhano. 2Koma pa nthawiyo nʼkuti mafuko asanu ndi awiri a Aisraeli asanalandire cholowa chawo.

3Ndipo Yoswa anati kwa Aisraeli, “Kodi mudikira mpaka liti kuti mulowe ndi kulanda dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu wakupatsani? 4Sankhani amuna atatu kuchokera ku fuko lililonse ndipo ine ndidzawatuma kuti akayendere dzikolo ndi kukalilembera bwino kuti ndiligawe kukhala lawo. Akatero, abwererenso kwa ine. 5Aligawe dzikolo mʼzigawo zisanu ndi ziwiri; fuko la Yuda lidzakhale ndi dziko lake la kummwera ndi nyumba ya Yosefe ikhalebe mʼdziko lawo la kumpoto. 6Mudzalembe mawu ofotokoza za zigawo zisanu ndi ziwiri za dzikolo, ndi kubwera nawo kwa ine. Tsono ineyo ndidzakuchitirani maere pamaso pa Yehova Mulungu wanu. 7Alevi asakhale ndi dziko pakati panu, chifukwa gawo lawo ndi kutumikira Yehova pa ntchito ya unsembe. Ndipo Gadi, Rubeni ndi theka la fuko la Manase analandira kale cholowa chawo kummawa kwa Yorodani. Mose mtumiki wa Yehova ndiye anawapatsa.”

8Anthuwo akupita kukalembera dzikolo, Yoswa anawalangiza kuti, “Pitani mukayendere ndi kulembera dzikolo. Kenaka mukabwere kwa ine, ndidzakuchitirani maere kuno ku Silo pamaso pa Yehova.” 9Ndipo anthu anachoka ndi kukayendera dziko lonse. Iwo analemba bwinobwino mʼbuku za dzikolo, mzinda ndi mzinda. Analigawa magawo asanu ndi awiri, ndipo anabwerera kwa Yoswa ku misasa ya ku Silo. 10Pambuyo pake Yoswa anawachitira maere ku Silo pamaso pa Yehova, ndipo fuko lililonse la Israeli analigawira dziko lake.

Dziko la Benjamini

11Maere anagwera mabanja a fuko la Benjamini. Dziko limene anapatsidwa linali pakati pa fuko la Yuda ndi fuko la Yosefe:

12Mbali ya kumpoto malire awo anayambira ku Yorodani nalowera chakumpoto kwa matsitso a ku Yeriko kulowera cha kumadzulo kwa dziko la ku mapiri ndi kukafika ku chipululu cha Beti-Aveni. 13Kuchokera kumeneko malirewo analoza ku Luzi nadutsa mʼmbali mwa mapiri kummwera kwa Luzi (ndiye Beteli) ndipo anatsika mpaka ku Ataroti Adari, ku mapiri a kummwera kwa Beti-Horoni wa Kumunsi.

14Ndipo malirewo analowanso kwina, analunjika kummwera kuchokera kumadzulo kwake kwa phiri loyangʼanana ndi Beti-Horoni, mpaka ku mzinda wa Kiriyati Baala (ndiye Kiriati Yearimu), mzinda wa anthu a fuko la Yuda. Amenewa ndiye anali malire a mbali ya kumadzulo.

15Malire a kummwera anayambira mʼmphepete mwenimweni mwa Kiriati Yearimu napita kumadzulo mpaka kukafika ku akasupe a Nefitowa. 16Malire anatsikira mʼmphepete mwa phiri loyangʼanana ndi chigwa cha Beni Hinomu, kumpoto kwa chigwa cha Refaimu. Anapitirira kutsikira ku chigwa cha Hinomu kummwera kwa chitunda cha Ayebusi mpaka ku Eni Rogeli. 17Kenaka anakhotera kumpoto kupita ku Eni-Semesi, kupitirira mpaka ku Geliloti amene amayangʼanana ndi pokwera pa Adumimu. Kenaka malire anatsikira ku Mwala wa Bohani, mwana wa Rubeni. 18Anabzola cha kumpoto kwa chitunda cha Beti Araba ndi kutsikabe mpaka ku chigwa cha Yorodani. 19Anabzolanso cha kumpoto kwa chitunda cha Beti-Hogila kukafika cha kumpoto ku gombe la Nyanja ya Mchere kumene mtsinje wa Yorodani umathirirako, cha kummwera kwenikweni. Awa anali malire a kummwera.

20Yorodani ndiye anali malire a mbali ya kummawa.

Awa anali malire a dziko limene mabanja a fuko la Benjamini analandira.

21Mabanja a fuko la Benjamini anali ndi mizinda iyi;

Yeriko, Beti-Hogila, Emeki Kezizi, 22Beti-Araba, Zemaraimu, Beteli 23Avimu, Para, Ofiri, 24Kefari-Amoni, Ofini ndi Geba, mizinda khumi ndi awiri ndi midzi yake

25Panalinso Gibiyoni, Rama, Beeroti, 26Mizipa, Kefira, Moza 27Rekemu, Iripeeli, Tarala, 28Zera Haelefu, mzinda wa Ayebusi (ndiye kuti Yerusalemu) Gibeya ndi Kiriati, mizinda 14 ndi midzi yake.

Limeneli ndilo dziko limene mabanja a fuko la Benjamini analandira kuti likhale lawo.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

約書亞記 18:1-28

其餘土地的分配

1征服了這些地方以後,以色列全體會眾都聚集在示羅,把會幕設立在那裡。 2這時,以色列還有七個支派沒有分到產業。 3約書亞對他們說:「你們等到什麼時候才去佔領你們祖先的上帝耶和華賜給你們的土地呢? 4你們每支派要派出三個人,我要差他們去偵察,按各支派應得的土地繪製地圖,然後回來稟告我。 5他們要把土地劃分作七份。猶大要留在南部自己的領土上,約瑟家族要留在北部自己的領土上。 6你們把這七份土地繪成地圖交給我,我要在我們的上帝耶和華面前為你們抽籤。 7你們當中的利未人沒有份,因為做耶和華的祭司這職任就是他們的產業。至於迦得支派、呂便支派和瑪拿西半個支派,摩西已把約旦河東的土地分給他們了。」

8那些畫地圖的人啟程出發的時候,約書亞囑咐他們說:「你們要走遍那裡,繪製地圖,然後回來稟告我,我要在示羅,在耶和華面前為你們抽籤。」 9於是,他們走遍那裡,把所有城邑分作七份,繪在冊上,然後回到示羅約書亞10約書亞便在示羅按照以色列的支派,在耶和華面前為他們抽籤分地。

便雅憫支派分到的土地

11便雅憫支派按宗族抽籤分到的領土,座落在猶大約瑟支派的領土之間。 12他們北部的邊界從約旦河起,沿耶利哥北面的山坡直上,往西穿過山區,直到伯·亞文的曠野; 13從那裡經路斯,即伯特利南面山坡到下伯·和崙南面山區的亞他綠·亞達14西面的邊界自伯·和崙對面山的西側向南直到猶大人的基列·巴力,即基列·耶琳15南部邊界從基列·耶琳的邊界開始向西直到尼弗多亞的水泉, 16又往下到欣嫩子谷對面的山麓,也就是利乏音谷北邊,然後往南,經欣嫩谷到耶布斯山南部,直到隱·羅結17然後,向北先後到隱·示麥亞都冥山坡對面的基利綠呂便的兒子波罕所立的大石, 18以及亞拉巴的對面,再往北下到亞拉巴19又沿著伯·曷拉的北面直到鹽海的北岸,也就是約旦河的南部河口。這是南部的邊界。 20東面以約旦河為界。這是便雅憫人按宗族分到的土地和四周的邊界。

21以下是便雅憫支派按宗族分到的城邑:耶利哥伯·曷拉伊麥·基悉22伯·亞拉巴西瑪蓮伯特利23亞文巴拉俄弗拉24基法·阿摩尼俄弗尼迦巴,共十二座城及其附近的鄉村。 25還有基遍拉瑪比錄26米斯巴基非拉摩撒27利堅伊利毗勒他拉拉28洗拉以利弗耶布斯——即耶路撒冷基比亞基列,共十四座城及其附近的鄉村。

這就是便雅憫各宗族所分到的土地。