Yoswa 16 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yoswa 16:1-10

Madera amene Efereimu ndi Manase Analandira

1Dziko limene linapatsidwa kwa fuko la Yosefe linayambira ku mtsinje wa Yorodani ku Yeriko, kummawa kwa akasupe a Yeriko, ndiponso kuyambira mtsinje wa Yorodaniwo nʼkumakwera, kudutsa mʼchipululu mpaka ku mapiri a ku Beteli. 2Kuchokera ku Beteli malire ake anakafika ku Luzi, kudutsa dziko la Ataroti kumene kumakhala Aariki. 3Malirewo anatsikira cha kumadzulo kwa dziko la Yafuleti mpaka ku chigawo cha kumunsi kwa Beti-Horoni. Kuchokera kumeneko anapitirira mpaka ku Gezeri nʼkuthera ku Nyanja.

4Choncho Manase ndi Efereimu, ana a Yosefe analandira cholowa chawo.

5Dziko la mabanja a fuko la Efereimu ndi ili:

Malire a dzikolo anachokera kummawa kwa Ataroti Adari mpaka ku mtunda kwa Beti-Horoni. 6Malirewo anapitirira mpaka ku nyanja. Mikimetati anali kumpoto kwake. Kuchokera kumeneko anakhotera cha kummawa kuloza ku Taanati Silo ndi kudutsa kumeneko cha kummawa mpaka ku Yanowa. 7Ndipo kuchokera ku Yanowa anatsikira ku Ataroti ndi Naara, nakafika ku Yeriko ndi kukathera ku mtsinje wa Yorodani. 8Kuchokera ku Tapuwa anapita kumadzulo mpaka ku mtsinje wa Kana ndi kukathera ku nyanja. Dziko ili linali cholowa cha mabanja afuko la Efereimu, 9kuphatikizapo mizinda yonse ndi midzi yake yopatsidwa kwa Efereimu, koma yokhala mʼkati mwa dziko la Manase.

10Iwo sanapirikitse Akanaani amene amakhala ku Gezeri ndipo mpaka lero Akanaani akukhala pakati pa Aefereimu koma amagwira ntchito ngati akapolo.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

約書亞記 16:1-10

約瑟子孫分到的土地

1約瑟的子孫抽籤所得的地方是從耶利哥附近的約旦河,就是耶利哥水泉的東面開始,穿過曠野,直到伯特利山區; 2又從伯特利,即路斯,沿著亞基人的邊境,直到亞他綠3然後西下至押利提人的疆土,遠至伯·和崙地區,經基色直到地中海。 4約瑟的兒子瑪拿西以法蓮得了自己的產業。

5以下是以法蓮的子孫按宗族分到的土地:東面從亞他綠·亞達到上伯·和崙6地中海,又向北至密米他,然後向東繞到他納·示羅,到雅挪哈東部, 7再到亞他綠拿拉,經耶利哥直到約旦河; 8又從他普亞往西到加拿河,直到地中海。這就是以法蓮的子孫按宗族所分的產業。 9此外,他們又從瑪拿西人的產業中,分到部分城邑以及附近的鄉村。 10他們沒有趕走住在基色迦南人,迦南人至今還住在以法蓮人當中,為他們服勞役。