Yoswa 14 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yoswa 14:1-15

Kugawa kwa Dziko la Kumadzulo kwa Yorodani

1Umu ndi mmene Aisraeli analandirira cholowa chawo mʼdziko la Kanaani. Eliezara wansembe, Yoswa mwana wa Nuni pamodzi ndi akuluakulu a mafuko a Israeli ndiwo anagawa dzikolo kugawira Aisraeli. 2Madera anagawidwa mwa maere kwa mafuko asanu ndi anayi ndi theka, monga momwe Yehova analamulira kudzera mwa Mose. 3Mose anapereka kwa mafuko awiri ndi theka dziko la kummawa kwa Yorodani, koma fuko la Levi lokha silinagawiridwe malo. 4Tsono fuko la Yosefe analigawa pawiri, Manase ndi Efereimu. Mose sanawagawire malo mabanja a fuko la Levi, koma iwo anangolandira mizinda imene ankakhalamo pamodzi ndi malo amene ankawetako nkhosa ndi ngʼombe zawo. 5Choncho Aisraeli anagawana dzikolo, monga momwe Yehova analamulira Mose.

Apereka Hebroni kwa Kalebe

6Tsono anthu a fuko la Yuda anabwera kwa Yoswa ku Giligala, ndipo Kalebe mwana wa Yefune Mkeni anati kwa iye, “Inu mukudziwa zimene Yehova ananena kwa Mose munthu wa Mulungu za inu ndi ine ku Kadesi Barinea. 7Nthawi imene Mose mtumiki wa Yehova anandituma kuchokera ku Kadesi Barinea kudzayendera dzikoli ndinali ndi zaka makumi anayi. Ndipo nditabwerako ndinamuwuza zoona zokhazokha monga momwe ndinaonera. 8Koma abale anga amene ndinapita nawo anachititsa anthu mantha. Komabe ine ndinamvera Yehova Mulungu wanga ndi mtima wonse. 9Kotero tsiku limenelo Mose anandilonjeza kuti, ‘Dziko limene unayendamo lidzakhala lako ndiponso la ana ako kwamuyaya chifukwa unamvera Yehova Mulungu wanga ndi mtima wako wonse.’

10“Tsono papita zaka 45 chiyankhulire Yehova zimenezi kwa Mose. Nthawi imeneyo nʼkuti Aisraeli akuyendayenda mʼchipululu. Yehova wandisunga ndipo tsopano ndili ndi zaka 85. 11Komabe ndikanali ndi mphamvu lero, monga ndinalili tsiku lija Mose anandituma. Ndili ndi mphamvu moti ndikhoza kupita ku nkhondo kapena kuchita kanthu kena kalikonse. 12Tsopano ndipatseni dziko la ku mapiri limene Yehova anandilonjeza tsiku lija. Inu munamva nthawi ija kuti Aanaki anali kumeneko ndipo kuti mizinda yawo inali ikuluikulu ndi yotetezedwa. Komabe Yehova atakhala nane ndidzawathamangitsa monga Iye ananenera.”

13Ndipo Yoswa anadalitsa Kalebe mwana wa Yefune ndi kumupatsa Hebroni kukhala dziko lake. 14Choncho dera la Hebroni lakhala lili la Kalebe mwana wa Yefune Mkeni mpaka lero chifukwa anamvera Yehova Mulungu wa Israeli ndi mtima wonse. 15(Hebroni ankatchedwa Kiriati Ariba chifukwa cha Ariba amene anali munthu wamphamvu kwambiri pakati pa Aanaki).

Ndipo kenaka mʼdziko monse munakhala mtendere.