Yona 3 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yona 3:1-10

Yona Apita ku Ninive

1Ndipo Yehova anayankhula ndi Yona kachiwiri kuti, 2“Nyamuka, pita ku mzinda waukulu wa Ninive ndipo ukalalikire uthenga umene ndikupatsa.”

3Yona anamvera mawu a Yehova ndipo anapita ku Ninive. Tsono Ninive unali mzinda waukulu kwambiri; wofunika masiku atatu kuwudutsa. 4Yona analowa mu mzindawo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi. Iye ankalalikira kuti, “Atsala masiku makumi anayi kuti Ninive awonongedwe.” 5Anthu a ku Ninive anakhulupirira Mulungu. Analengeza kuti aliyense, wamkulu ndi wamngʼono yemwe asale zakudya ndipo avale chiguduli.

6Mfumu ya ku Ninive itamva nkhaniyi, inatsika pa mpando wake waufumu, nivula mkanjo wake waufumu ndipo inavala chiguduli ndi kukhala pansi pa fumbi. 7Tsono mfumuyo inalengeza mu Ninive kuti,

“Mwa lamulo lochokera kwa mfumu ndi akalonga ake:

“Munthu aliyense kapenanso nyama, ngʼombe kapena nkhosa, zisadye kanthu kalikonse; musazilole kuti zidye kapena kumwa. 8Koma anthu avale ziguduli, ndipo nyamanso aziveke ziguduli. Munthu aliyense azifuwula kwa Mulungu ndi mphamvu zake zonse. Anthuwo asiye makhalidwe awo oyipa ndi machitidwe achiwawa. 9Angadziwe ndani? Mwina Mulungu nʼkutikhululukira ndipo mwa chifundo chake nʼkuleka kutikwiyira, ifeyo osawonongedwa.”

10Mulungu ataona zimene anthuwo anachita, ndi mmene anasiyira makhalidwe awo oyipa, anawachitira chifundo ndipo sanabweretse chiwonongeko chimene anawaopseza nacho.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

约拿书 3:1-10

1耶和华第二次对约拿说: 2“你起身前往尼尼微大城,向那里的居民宣告我先前吩咐你的话。” 3约拿便照耶和华的吩咐前往尼尼微城。尼尼微城很大,要三天才能走遍。 4约拿进城走了一天,宣告说:“再过四十天尼尼微就要毁灭了!” 5尼尼微城的人相信了上帝的话,便宣告禁食,所有的人,无论大小贵贱都换上麻衣。 6尼尼微王听到这消息后,便走下宝座,脱下王袍,披上麻衣,坐在炉灰中。 7王又向全城颁布命令,说:“王和大臣有令,所有的人都必须禁食,牛羊牲畜都不许吃草也不许喝水。 8人和牲畜都必须披上麻衣,众人要向上帝恳切呼求,改邪归正,停止作恶。 9上帝或许会施怜悯,收回烈怒,使我们不致灭亡,也未可知。” 10上帝看见他们改邪归正,不再作恶,就怜悯他们,没有像所说的那样毁灭他们。