Yohane 8 – CCL & SNC

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yohane 8:1-59

1Koma Yesu anapita ku phiri la Olivi. 2Mmamawa Iye anaonekeranso ku Nyumba ya Mulungu kumene anthu onse anamuzungulira ndipo Iye anakhala pansi nawaphunzitsa. 3Aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi anabweretsa mkazi amene anagwidwa akuchita chigololo. Iwo anamuyimiritsa patsogolo pa anthu ndipo 4anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, mkazi uyu tinamugwira akuchita chigololo. 5Mʼmalamulo a Mose anatilamulira kuti akazi otere tiwagende ndi miyala. Tsopano Inu mukuti chiyani?” 6Iwo anagwiritsa ntchito funsoli ngati msampha, ndi cholinga choti apeze chifukwa cha kumuneneza Iye.

Koma Yesu anawerama pansi ndi kuyamba kulemba pa dothi ndi chala chake. 7Pamene iwo anapitirira kumufunsa, Iye anaweramuka ndipo anawawuza kuti, “Ngati wina wa inu alipo wopanda tchimo, ayambe iyeyo kumugenda ndi miyala mkaziyu.” 8Iye anaweramanso pansi ndi kulemba pa dothi.

9Iwo atamva izi anayamba kuchoka mmodzimmodzi, akuluakulu poyamba, mpaka Yesu anatsala yekha ndi mkaziyo atayimirira pomwepo. 10Yesu anaweramuka ndipo anamufunsa iye kuti, “Akuluakulu aja ali kuti? Kodi palibe amene wakutsutsa?”

11Iye anati, “Ambuye, palibe ndi mmodzi yemwe.”

“Inenso sindikukutsutsa iwe. Pita kuyambira tsopano usakachimwenso.”

Za Umboni wa Yesu

12Yesu atayankhulanso kwa anthu, anati, “Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi. Aliyense amene anditsata Ine sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuwala kotsogolera anthu ku moyo.”

13Afarisi anamutsutsa Iye nati, “Iwe ukudzichitira umboni wa Iwe mwini, umboni wako siwoona.”

14Yesu anayankha kuti, “Ngakhale Ine ndidzichitire umboni, umboni wangawu ndi woona, pakuti Ine ndikudziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndikupita. Koma inu simukudziwa ndi pangʼono pomwe kumene ndinachokera kapena kumene ndikupita. 15Inu mumaweruza potsata maganizo a anthu chabe. Ine sindiweruza munthu wina aliyense. 16Koma Ine ndikati ndiweruze, ndimaweruza molondola, chifukwa Ine sindili ndekha koma ndili ndi Atate amene anandituma. 17Mʼmalamulo anu munalembedwa kuti umboni wa anthu awiri ndi wovomerezeka. 18Ine ndikudzichitira ndekha umboni; ndipo mboni inanso ndi Atate amene anandituma.”

19Kenaka iwo anamufunsa Iye kuti, “Kodi Atate anuwo ali kuti?”

Yesu anayankha kuti, “Inu simundidziwa Ine. Atate anganso simuwadziwa. Mukanandidziwa Ine, mukanawadziwanso Atate anga.” 20Iye anayankhula mawu awa pamene amaphunzitsa Nyumba ya Mulungu pafupi ndi malo amene amaponyapo zopereka. Komabe palibe amene anamugwira Iye, chifukwa nthawi yake inali isanakwane.

Mkangano Woti Yesu Ndani

21Kenakanso Yesu anawawuza kuti, “Ine ndikupita, ndipo mudzandifunafuna, koma mudzafa muli mʼmachimo anu. Kumene ndikupita, inu simungabwereko.”

22Izi zinachititsa Ayuda kufunsa kuti, “Kodi adzadzipha yekha? Kodi ndicho chifukwa chake akuti, ‘Kumene ndikupita, inu simungabwereko?’ ”

23Koma Iye anapitiriza kuti, “Inu ndi ochokera pansi pano. Ine ndine wochokera kumwamba. Inu ndinu anthu a dziko la pansi. Ine sindine wa dziko lapansi lino. 24Ine ndinakuwuzani kuti mudzafera mʼmachimo anu ngati simukhulupirira kuti Ine Ndine. Ndithu inu mudzafera mʼmachimo anu.”

25Iwo anafunsa kuti, “Ndinu ndani?”

Yesu anayankha kuti, “Monga Ine ndakhala ndikunena nthawi yonseyi, 26ndili ndi zambiri zoti ndinene zoweruza inu. Koma Iye amene anandituma ndi woona, ndipo chimene Ine ndamva kuchokera kwa Iye, ndi chimene ndimaliwuza dziko lapansi.”

27Iwo sanazindikire kuti Iye amawawuza za Atate ake. 28Choncho Yesu anati, “Inu mukadzapachika Mwana wa Munthu, pamenepo mudzadziwa kuti Ine Ndine. Mudzadziwa kuti sindichita kalikonse pa Ine ndekha koma ndimayankhula zokhazo zimene Atate anandiphunzitsa. 29Iye amene anandituma Ine ali nane pamodzi. Iye sanandisiye ndekha popeza nthawi zonse ndimachita zomwe zimamukondweretsa Iye.” 30Pamene Iye ankayankhula zimenezi, ambiri anamukhulupirira.

Ana a Abrahamu

31Kwa Ayuda amene anamukhulupirira, Yesu anati, “Ngati inu mutsatira chiphunzitso changa, ndithu ndinu ophunzira anga. 32Tsono mudzadziwa choonadi, ndipo choonadicho chidzakumasulani.”

33Iwo anamuyankha Iye kuti, “Ife ndife zidzukulu za Abrahamu ndipo sitinakhalepo akapolo a wina aliyense. Kodi mukunena bwanji kuti, ‘Ife tidzamasulidwa?’ ”

34Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimolo. 35Pajatu kapolo alibe malo wokhazikika mʼbanja, koma mwana ndi wa mʼbanjamo nthawi zonse. 36Nʼchifukwa chake ngati Mwana adzakumasulani, mudzakhala mfulu ndithu. 37Ine ndikudziwa kuti inu ndinu zidzukulu za Abrahamu. Chonsecho inu mwakonzeka kundipha Ine, chifukwa mawu anga alibe malo mwa inu. 38Ine ndikukuwuzani zimene ndaziona pamaso pa Atate, ndipo inu mukuchita zimene mwazimva kwa abambo anu.”

39Iwo anayankha kuti, “Ife abambo athu ndi Abrahamu.”

Yesu anati, “Inu mukanakhala ana a Abrahamu, bwenzi mukuchita zinthu zimene Abrahamuyo ankachita. 40Koma mmene zililimu, inu mwatsimikiza kundipha Ine, munthu amene ndinakuwuzani choonadi chimene Ine ndinachimva kuchokera kwa Mulungu. Abrahamu sanachite zinthu zoterezi. 41Inu mukuchita zinthu zimene abambo anu amachita.”

Iwo anatsutsa kuti, “Ife si ana amʼchigololo, Atate amene tili nawo ndi Mulungu yekha.”

Ana a Mdierekezi

42Yesu anawawuza kuti, “Mulungu akanakhala Atate anu, inu mukanandikonda Ine, pakuti Ine ndinachokera kwa Mulungu ndipo tsopano ndili pano. Ine sindinabwere mwa Ine ndekha. 43Nʼchifukwa chiyani simukumvetsetsa mawu anga? Chifukwa chake nʼchakuti simungathe kumva zoyankhula zanga. 44Inu ndinu ana a mdierekezi. Iye ndiye abambo anu ndipo mukufuna kuchita zimene abambo anuwo amakhumba. Iye anali wakupha kuyambira pachiyambi, sanasunge choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene Iye anena bodza, amayankhula chiyankhulo chobadwa nacho, popeza ndi wabodza ndipo ndi bambo wa mabodza. 45Koma chifukwa ndikuwuzani choonadi, inu simukundikhulupirira Ine! 46Ndani mwa inu angatsimikize kuti ndine wochimwa? Ngati Ine ndikunena choonadi, nʼchifukwa chiyani simukundikhulupirira? 47Munthu wochokera kwa Mulungu amamva zimene Mulungu amanena. Chifukwa chimene simumvera nʼchakuti, inuyo sindinu ochokera kwa Mulungu.”

Zomwe Yesu Ananena za lye Mwini

48Ayuda anamuyankha Iye kuti, “Kodi ife sitikulondola ponena kuti Inu ndi Msamariya ndi wogwidwa ndi chiwanda?”

49Yesu anati, “Ine sindinagwidwe ndi chiwanda, koma ndimalemekeza Atate anga, koma inu mukundinyoza. 50Ine sindidzifunira ndekha ulemu; koma alipo wina amene amandifunira, ndipo Iyeyo ndiye woweruza. 51Ine ndikukuwuzani choonadi, munthu akasunga mawu anga, sadzafa konse.”

52Pamenepo Ayuda anafuwula kuti, “Tsopano ife tadziwadi kuti Inu ndi wogwidwa ndi chiwanda! Abrahamu anafa ndiponso aneneri, koma Inu mukunena kuti, ‘Ngati munthu asunga mawu anga, sadzafa.’ 53Kodi ndinu wa mkulu kuposa abambo athu Abrahamu? Iye anafa, ndiponso aneneri onse. Inu mukuganiza kuti ndinu yani?”

54Yesu anayankha kuti, “Ngati Ine ndidzilemekeza ndekha, ulemu wangawo ndi wosatanthauza kanthu. Atate anga amene inu mukuti ndi Mulungu wanu, ndiye amene amandilemekeza Ine. 55Ngakhale kuti inuyo simukumudziwa, Ineyo ndikumudziwa. Ngati Ine nditanena kuti sindikumudziwa, Ineyo nditha kukhala wabodza ngati inuyo, koma Ine ndimamudziwa ndipo ndimasunga mawu ake. 56Abambo anu Abrahamu anakondwera poyembekezera kubwera kwanga. Iwo anandiona ndipo anasangalala.”

57Ayuda anati kwa Iye, “Inu sumunafike nʼkomwe zaka makumi asanu, ndipo mukuti munamuona Abrahamu!”

58Yesu anayankha kuti, “Ine ndikukuwuzani choonadi, Abrahamu asanabadwe, Ine Ndine!” 59Pamenepo iwo anatola miyala kuti amugende, koma Yesu anabisala, nachoka mozemba mʼNyumba ya Mulungu.

Slovo na cestu

Jan 8:1-59

Ježíš odpouští cizoložné ženě

1Ježíš odešel na Olivovou horu. 2Brzy ráno se do chrámu vrátil, sedl si tam a začal učit shromážděný dav. 3Za chvíli k němu znalci zákona a farizejové přivedli jednu ženu přistiženou při nevěře.

4„Mistře,“ oslovili Ježíše, „tuto ženu jsme přistihli při cizoložství. 5Mojžíšův zákon je přísný. Odsuzuje ji k smrti ukamenováním. Co ty tomu říkáš?“

6Čekali, že jim Ježíšova odpověď poskytne záminku k jeho odsouzení. Ježíš však mlčel, sklonil se k zemi a psal něco prstem v prachu. 7Žalobci stále dotírali, aby odpověděl. Ježíš se vzpřímil a řekl: „Kdo z vás je bez hříchu, ať po ní hodí první kamenem!“ 8Pak se znovu sklonil a psal po zemi.

9Jeho slovy byli zahanbeni. Ozvalo se v nich svědomí, a tak jeden po druhém odcházeli – ti nejváženější jako první. Nakonec zůstal Ježíš s provinilou ženou sám. 10Znovu se vzpřímila zeptal se ženy: „Kam se poděli tvoji žalobci? Žádný z nich tě neodsoudil?“

11„Ne, Pane,“ odpověděla žena.

„Já tě také neodsuzuji,“ řekl Ježíš. „Jdi, ale už nehřeš!“

Ježíš je světlo světa

12Jindy Ježíš řekl: „Já jsem světlo světa, kdo mne následuje, nebude tápat ve tmě, ale bude mít světlo na cestu života.“

13Nato mu farizejové řekli: „Mluvíš stále jen sám o sobě. Kdo to potvrdí?“

14Ježíš jim odpověděl: „Říkám jen pravdu, i když se týká mne samotného. Já vím, odkud jsem přišel a kam jdu, ale vy to nevíte. 15Vy mne posuzujete nesprávně – jen podle svého zdání. Já tak nesoudím. 16Můj úsudek odpovídá skutečnosti, protože není jen můj, ale i Boží. 17A když se dva svědci shodnou ve výpovědi, vaše zákony považují takové svědectví za platné. 18Nemluvím tedy o sobě jen sám, ale svědčí o mně i Otec, který mne poslal.“

19„A kde je ten tvůj Otec?“ ptali se farizejové. Řekl jim: „Když neznáte mne, nemůžete znát ani mého Otce. Kdybyste znali mne, znali byste i jeho.“

20Tato slova Ježíš řekl v blízkosti chrámových pokladen, kde byla stráž. Přesto ho nezatkli, protože ještě nepřišel čas, kdy se to mělo stát.

Ježíš varuje před přicházejícím soudem

21„Opustím vás,“ pokračoval Ježíš. „Budete mne hledat, ale bude pro vás pozdě. Zemřete v zajetí svých hříchů a tam, kam jdu, nebudete moci přijít.“

22„Chce snad spáchat sebevraždu?“ ptali se mezi sebou. „Proč by jinak říkal, že za ním nemůžeme přijít tam, kam jde?“

23Ježíš jim řekl: „Já jsem od Boha, vy jste ze světa, který je Bohu odcizen. 24Proto zemřete v hříchu, když mi neuvěříte.“ 25„Tak nám tedy řekni, kdo vlastně jsi!“ naléhali na Ježíše. 26„Už jsem vám to jasně řekl. Jsem ten, za koho se od začátku prohlašuji,“ odpověděl. „Ale o vás bych mohl říci mnoho, co vás odsuzuje. A není to můj úsudek. Každé mé slovo pochází od toho, který mne poslal. On je pravda sama.“ 27Nikdo v té chvíli nepochopil, že Ježíš mluví o Bohu. 28Proto na vysvětlenou dodal: „Poznáte mne, až mne přibijete na kříž, teprve pak si uvědomíte, že všechno, co jsem vám říkal a co jsem udělal, nebylo ode mne, ale od mého Otce. To on mne naučil všemu, co jsem vám řekl. 29Je stále se mnou. Neopouští mne, protože dělám jen to, co mu je milé.“ 30Po těch slovech mnozí v něho uvěřili.

Ježíš hovoří o Božích nevěrných dětech

31Těm Ježíš řekl: „Držte se mých slov a budete opravdu mými učedníky. 32Poznáte pravdu a pravda vás osvobodí.“

33„Jsme potomci Abrahama,“ ozvali se. „Nikdy jsme nebyli otroky, proč tedy říkáš, že budeme osvobozeni?“

34Ježíš jim řekl: „Nemyslete si, že jako potomci Abrahamovi to máte u Boha jisté. Každý člověk je otrokem hříchu 35a otrok nemá právo na nic. 36-38Musíte se stát svobodnými členy Boží rodiny, a to vám může darovat jedině Syn. Nabízím vám takový dar, ale vy ho odmítáte a chcete se mne zbavit. Nedorozumění mezi námi je v tom, že nemáme stejného Otce.“ 39„Naším otcem je Abraham,“ řekli jednomyslně Židé. „Byl by vaším otcem,“ odpověděl jim Ježíš, „kdybyste ho svými životy následovali. 40Chcete mne zabít, přestože vám říkám pravdu, kterou mi sdělil Bůh. Abraham by tak nejednal. 41Projevujete se jako děti svého skutečného otce.“ To je rozhněvalo a jízlivě mu odsekli: „Nenarodili jsme se ze smilstva jako ty. Kdo myslíš, že je naším otcem? Kdo jiný, než Abrahamův Bůh! Nezpronevěřili jsme se mu.“

42Ježíš však namítl: „Kdyby Abrahamův Bůh byl opravdu vaším otcem, milovali byste mne. V něm je můj původ. Nepřicházím sám od sebe, ale on mne k vám posílá. 43Proč nechápete, co říkám? 44Protože váš otec je ďábel a vy děláte, co vám našeptává. Jeho lži od počátku přinášejí smrt a nic jiného, protože v něm není ani trochu pravdy. Nemůže si pomoci, lhaní je jeho přirozenost. A je původcem každé lži.

45-46Kdo z vás mne může usvědčit z hříchu? Nikdo! Proč mi tedy nevěříte, když říkám pravdu? 47Kdo je opravdu Božím dítětem, ten rád přijímá Boží slovo. Vy je odmítáte, a to dokazuje, že z Boha nepocházíte.“

Ježíš prohlašuje, že je věčný

48„Vždyť to říkáme, jsi odrodilec a blázen,“ křičeli na něj Židé.

49„Nejsem,“ odpověděl jim Ježíš klidně. „Já Otci vzdávám čest, ale vy mu ji upíráte, když mne nepřijímáte. 50Nemyslete si, že toužím po slávě a velikosti. Mne chce oslavit Bůh. Odsoudí každého, kdo mne odmítne. 51Budete-li žít podle mého slova, nemusíte se bát smrti.“

52„Teď se ukázalo, jaký jsi blázen!“ posmívali se. „Abraham zemřel, proroci zemřeli, a ty tvrdíš, že kdo dá na tebe, unikne smrti. 53Myslíš si snad, že jsi významnější než náš otec Abraham a větší než proroci? Co to ze sebe děláš? Vždyť ti všichni zem-řeli!“

54Ježíš jim odpověděl: „Kdybych se chválil sám, má slova by neměla žádnou váhu, ale chválí mne můj Otec, kterého uznáváte za svého Boha. 55Nikdy jste ho však nepoznali, ale já ho znám dobře. Kdybych to zapřel, byl bych stejný lhář jako vy. Opravdu ho dobře znám a ve všem ho poslouchám. 56Jakou radost by měl váš otec Abraham, kdyby se dočkal mého příchodu. Už tehdy věděl, že přijdu, a jak se z toho radoval.“ 57„Teď jsi se projevil. Není ti ani padesát, a pamatuješ Abrahama?“ smáli se Židé.

58Ježíš odpověděl: „Žil jsem dávno před tím, než se narodil Abraham.“ 59To rozpálilo jejich hněv a chtěli ho ukamenovat. V rozruchu, který nastal, se Ježíš vytratil z chrámu.