Yohane 20 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yohane 20:1-31

Yesu Auka kwa Akufa

1Mmamawa tsiku loyamba la sabata, kukanali kamdimabe, Mariya wa ku Magadala anapita ku manda ndipo anaona kuti mwala unali utachotsedwa pa khomo la manda. 2Choncho anabwerera akuthamanga kwa Simoni Petro ndi wophunzira winayo, amene Yesu anamukonda, ndipo anati, “Iwo amuchotsa Ambuye mʼmanda, ndipo ife sitikudziwa kumene iwo amuyika Iye!”

3Choncho Petro ndi wophunzira winayo ananyamuka kupita ku manda. 4Onse awiri anathamanga pamodzi koma wophunzira winayo anamupitirira Petro, nafika ku manda moyambirira. 5Ndipo mmene anawerama nasuzumira mʼkati mwa manda anaona nsalu zili potero koma sanalowemo. 6Kenaka Simoni Petro, amene anali pambuyo pake, anafika ndi kulowa mʼmanda. Iye anaona nsaluzo zili pamenepo, 7pamodzinso ndi nsalu imene anakulungira nayo mutu wa Yesu. Nsaluyi inali yopindidwa pa yokha yosiyanitsidwa ndi inayo. 8Pomaliza wophunzira winayo, amene anafika ku manda moyambirira, analowanso mʼkati, iye anaona ndi kukhulupirira. 9(Iwo sanazindikire kuchokera mʼmalemba kuti Yesu anayanera kuuka kuchokera kwa akufa).

Yesu Aonekera kwa Mariya wa ku Magadala

10Kenaka ophunzira anabwerera ku nyumba zawo, 11koma Mariya anayima kunja kwa manda akulira. Pamene akulira, anawerama ndi kusuzumira mʼmanda 12ndipo anaona angelo awiri atavala zoyera, atakhala pamene panali mtembo wa Yesu, mmodzi kumutu ndi wina kumapazi.

13Iwo anamufunsa iye kuti, “Amayi, nʼchifukwa chiyani mukulira?”

Iye anati, “Amuchotsa Mbuye wanga, ndipo ine sindikudziwa kumene iwo amuyika.” 14Atanena izi, iye anatembenuka ndipo anaona Yesu atayima potero koma iye sanazindikire kuti anali Yesu.

15Iye anati, “Amayi, mukulira chifukwa chiyani? Ndani amene mukumufunafuna?”

Poganiza kuti anali mwini munda, iye anati, “Bwana, ngati inu mwamuchotsa, ndiwuzeni kumene mwamuyika, ndipo ine ndikamutenga.”

16Yesu anati kwa iye, “Mariya.”

Anatembenukira kwa Iye nafuwula mu Chiaramaiki kuti, “Raboni!” (kutanthauza Mphunzitsi).

17Yesu anati, “Usandigwire Ine, pakuti sindinapite kwa Atate. Mʼmalo mwake pita kwa abale anga ndikukawawuza kuti, ndikupita kwa Atate ndi kwa Atate anunso, kwa Mulungu wanga ndi Mulungu wanunso.”

18Mariya wa ku Magadala anapita kwa ophunzira ndi uthenga wakuti, “Ndamuona Ambuye!” Iye anawawuza iwo kuti Yesu ananena zinthu izi kwa iye.

Yesu Aonekera kwa Ophunzira ake Tomasi Palibe

19Madzulo a tsiku limenelo limene linali loyamba la Sabata ophunzira ake ali pamodzi, atatseka ndi kukhoma zitseko chifukwa choopa Ayuda, Yesu anabwera ndi kuyima pakati pawo nati, “Mtendere ukhale nanu!” 20Iye atatha kunena izi, anawaonetsa manja ake ndi mʼnthiti mwake. Ophunzira anasangalala kwambiri pamene anaona Ambuye.

21Yesu anatinso, “Mtendere ukhale nanu! Monga Atate anandituma Ine, Inenso ndikukutumani.” 22Ndi mawu amenewo Iye anawapumira ndipo anati, “Landirani Mzimu Woyera. 23Ngati mukhululukira aliyense machimo ake, iwo akhululukidwa; ngati simuwakhululukira, iwo sanakhululukidwe.”

Yesu Aonekera kwa Tomasi

24Koma Tomasi (otchedwa Didimo), mmodzi wa khumi ndi awiriwo, sanali ndi ophunzira pamene Yesu anabwera. 25Ophunzira enawo atamuwuza Tomasi kuti iwo anaona Ambuye, iye ananenetsa kuti, “Pokhapokha nditaona zizindikiro za misomali mʼmanja ake ndi kuyikamo chala changa mʼmene munali misomali ndi kukhudza dzanja langa mʼnthiti mwake, ine sindidzakhulupirira.”

26Patapita sabata, ophunzira ake analinso mʼnyumbamo ndipo Tomasi anali nawo. Ngakhale makomo anali otsekedwa, Yesu anabwera nayima pakati pawo, ndipo anati, “Mtendere ukhale nanu!” 27Kenaka anati kwa Tomasi, “Ika chala chako apa; ona manja anga. Tambasula dzanja lako ndi kukhudza mʼnthiti mwanga. Leka kukayika, khulupirira.”

28Tomasi anati kwa Iye, “Ambuye wanga ndi Mulungu wanga!”

29Kenaka Yesu anamuwuza kuti, “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiona Ine? Ndi odala amene amakhulupirira ngakhale asanaone.”

Cholinga cha Uthenga Wabwino wa Yohane

30Yesu anachita zodabwitsa zambiri pamaso pa ophunzira ake zimene sizinalembedwe mʼbuku lino. 31Koma izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndi Khristu, Mwana wa Mulungu, ndi kuti mukakhulupirira mukhale nawo moyo mʼdzina lake.