Yohane 17 – CCL & HOF

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yohane 17:1-26

Yesu Adzipempherera Yekha

1Yesu atatha kunena izi, anayangʼana kumwamba ndipo anapemphera:

“Atate, nthawi yafika. Lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanuyo akulemekezeni Inu. 2Pakuti Inu munamupatsa Iye ulamuliro pa anthu onse kuti apereke moyo wosatha kwa onse amene mwamupatsa. 3Tsono moyo wosathawo ndi uwu: Iwo akudziweni Inu, Mulungu yekhayo woona, ndi Yesu Khristu, amene Inu mwamutuma. 4Ine ndabweretsa ulemerero wanu pa dziko pamene ndamaliza ntchito imene munandipatsa kuti ndi igwire. 5Ndipo tsopano, Atate, ndilemekezeni Ine pamaso panu ndi ulemerero uja umene ndinali nawo kwa Inu dziko lapansi lisanayambe.

Yesu Apempherera Ophunzira Ake

6“Ine ndawadziwitsa za Inu anthu amene munandipatsa mʼdziko lapansi. Iwo anali anu. Inu munawapereka kwa Ine ndipo amvera mawu anu. 7Tsopano akudziwa kuti zonse zimene munandipatsa nʼzochokera kwa Inu. 8Pakuti Ine ndiwapatsa mawu amene Inu munandipatsa ndipo awalandira. Iwo akudziwa ndithu kuti Ine ndinachokera kwa Inu, ndipo akukhulupirira kuti Inu ndiye amene munandituma Ine. 9Ine ndikuwapempherera. Ine sindikupempherera dziko lapansi, koma anthu amene Inu mwandipatsa, pakuti ndi anu. 10Zonse zimene Ine ndili nazo ndi zanu, ndipo zonse zimene Inu muli nazo ndi zanga. Choncho Ine ndalemekezedwa mwa iwowo. 11Ine sindikukhalanso mʼdziko lapansi nthawi yayitali, koma iwo akanali mʼdziko lapansi. Ine ndikubwera kwa Inu. Atate Woyera, atetezeni ndi mphamvu za dzina lanu. Dzina limene munandipatsa Ine, kuti iwo akhale amodzi monga Ife tili amodzi. 12Pamene ndinali nawo, ndinawateteza ndi kuwasunga mosamala mʼdzina limene munandipatsa. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatayika kupatula yekhayo amene anayenera kuwonongeka kuti malemba akwaniritsidwe.

13“Tsopano ndikubwera kwa Inu. Ndikunena izi ndikanali mʼdziko lapansi, kuti iwo akhale ndi muyeso wodzaza wachimwemwe changa mʼkati mwawo. 14Ine ndawapatsa mawu anu ndipo dziko lapansi likudana nawo, pakuti sali a dziko lapansi monga Ine sindilinso wa dziko lapansi. 15Sindikupempha kuti muwachotse mʼdziko lapansi koma kuti muwateteze kwa woyipayo. 16Iwo si a dziko lapansi, monga Ine sindilinso wa dziko lapansi. 17Ayeretseni ndi choonadi chanu. Mawu anu ndiye choonadi. 18Monga Inu munandituma Ine mʼdziko lapansi, Inenso ndikuwatuma mʼdziko lapansi. 19Chifukwa cha iwowa Ine ndikudziyeretsa, kuti iwo ayeretsedwenso kwenikweni.

Yesu Apempherera Okhulupirira Onse

20“Ine sindikupempherera iwo okhawa, komanso amene adzandikhulupirira chifukwa cha uthenga wawo. 21Ndikuwapempherera kuti onsewa akhale amodzi. Monga Inu Atate muli mwa Ine ndi Ine mwa Inu, iwonso akhale mwa Ife kuti dziko lapansi likhulupirire kuti Inu munandituma Ine. 22Ine ndawapatsa ulemerero umene munandipatsa Ine, kuti akhale amodzi monga Ife tili amodzi. 23Ine ndikhale mwa iwo ndipo Inu mwa Ine kuti umodzi wawo ukhale wangwiro. Choncho dziko lapansi lidzadziwa kuti Inu munandituma Ine ndipo Inu mwawakonda iwowa monga momwe Inu munandikondera Ine.

24“Atate, Ine ndikufuna kuti anthu amene mwandipatsa Ine adzakhale ndi Ine kumene kuli Ine, ndi kuona ulemerero wanga, ulemerero umene munandipatsa chifukwa Inu munandikonda dziko lapansi lisanalengedwe.

25“Atate wolungama, ngakhale kuti dziko lapansi silikudziwani Inu, Ine ndimakudziwani, ndipo iwo amadziwa kuti Inu munandituma Ine. 26Ine ndawadziwitsa dzina lanu, ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzina lanulo, kuti chikondi chomwe munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndipo Ine mwa iwo.”

Hoffnung für Alle

Johannes 17:1-26

Jesus betet …

… für sich selbst

1Nach diesen Worten sah Jesus zum Himmel auf und betete: »Vater, die Zeit ist da! Lass jetzt die Herrlichkeit deines Sohnes sichtbar werden, damit der Sohn deine Herrlichkeit offenbart. 2Du hast ihm ja Macht über die Menschen gegeben, damit er allen das ewige Leben schenkt, die du ihm anvertraut hast. 3Und genau darin besteht das ewige Leben: dich, den einen wahren Gott, zu erkennen und Jesus Christus, den du gesandt hast. 4Ich habe hier auf der Erde deine Herrlichkeit sichtbar gemacht und alles getan, was du mir aufgetragen hast. 5Und nun, Vater, wenn ich wieder bei dir bin, dann schenk mir die Herrlichkeit, die ich bereits vor Erschaffung der Welt bei dir hatte.

6Ich habe den Menschen gezeigt, wer du bist, und zwar allen, die du aus der Welt herausgerufen und mir anvertraut hast. Dir gehörten sie schon immer, und du hast sie mir gegeben. Sie haben sich deine Worte zu Herzen genommen, 7und jetzt wissen sie, dass alles, was ich bekommen habe, von dir ist. 8Denn was du mir gesagt hast, habe ich ihnen weitergegeben. Sie haben deine Botschaft angenommen und wirklich erkannt, dass ich von dir hergekommen bin; sie glauben daran, dass du mich gesandt hast.«

… für seine Jünger

9»Für sie bitte ich dich jetzt: nicht für die ganze Welt, sondern für die Menschen, die du mir anvertraut hast. Denn sie gehören zu dir. 10Alles, was ich habe, das gehört dir, und was du hast, das gehört auch mir. An ihnen zeigt sich meine Herrlichkeit. 11Ich verlasse jetzt die Welt und komme zu dir. Sie aber bleiben zurück. Vater, du heiliger Gott, erhalte sie in der Gemeinschaft mit dir,17,11 Wörtlich: Bewahre sie in deinem Namen, den du mir gegeben hast. – So auch im nächsten Vers. damit sie eins sind wie wir. 12Solange ich bei ihnen war, habe ich sie in der Gemeinschaft mit dir erhalten, alle, die du mir anvertraut hast. Ich habe sie bewahrt, und keiner von ihnen ist verloren gegangen – außer dem einen, der verloren gehen musste, damit sich die Voraussage der Heiligen Schrift erfüllte.

13Jetzt komme ich zu dir zurück. Ich sage all das, solange ich noch bei ihnen in dieser Welt bin, damit meine Freude auch sie ganz erfüllt. 14Ich habe ihnen deine Botschaft weitergegeben, und die Welt hasst sie deswegen, weil sie ebenso wie ich nicht zu ihr gehören. 15Ich bitte dich nicht, sie aus der Welt zu nehmen, aber schütze sie vor der Macht des Bösen! 16Sie gehören ebenso wenig zur Welt wie ich. 17Lass ihnen deine Wahrheit leuchten, damit sie in immer engerer Gemeinschaft mit dir leben!17,17 Wörtlich: Heilige sie in der/durch die Wahrheit! Dein Wort ist die Wahrheit! 18Wie du mich in die Welt gesandt hast, so sende ich sie in die Welt. 19Für sie gebe ich mein Leben hin, damit ihr Leben ganz dir gehört.17,19 Wörtlich: Ich heilige mich selbst für sie, damit auch sie Geheiligte sind durch die Wahrheit.«

… für alle, die noch zum Glauben finden werden

20»Ich bitte aber nicht nur für sie, sondern für alle, die durch ihre Worte von mir hören werden und an mich glauben. 21Sie alle sollen eins sein, genauso wie du, Vater, mit mir eins bist. So wie du in mir bist und ich in dir bin, sollen auch sie in uns fest miteinander verbunden sein. Dann wird die Welt glauben, dass du mich gesandt hast. 22Deshalb habe ich ihnen auch die Herrlichkeit gegeben, die du mir anvertraut hast, damit sie die gleiche enge Gemeinschaft haben wie wir. 23Ich bleibe in ihnen, und du bleibst in mir. Genauso sollen auch sie vollkommen eins sein. Dann wird die Welt erkennen, dass du mich gesandt hast und dass du meine Jünger liebst, wie du mich liebst.

24Vater, ich möchte, dass alle, die du mir gegeben hast, mit mir dort sind, wo ich sein werde. Sie sollen meine Herrlichkeit sehen, die du mir gegeben hast. Denn du hast mich geliebt, lange bevor die Welt geschaffen wurde. 25Vater, du gerechter Gott! Wenn die Welt dich auch nicht kennt, ich kenne dich, und diese hier haben erkannt, dass du mich gesandt hast. 26Ich habe ihnen gezeigt, wer du bist. Das werde ich auch weiter tun, damit deine Liebe zu mir auch sie erfüllt, ja, damit ich selbst in ihnen lebe.«