Yohane 15 – CCL & KJV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yohane 15:1-27

Mpesa ndi Nthambi

1“Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate anga ndiye mwini munda. 2Iye amadula nthambi iliyonse ya mwa Ine imene sibala chipatso, koma nthambi iliyonse imene imabala chipatso amayisadzira bwino kuti ibale zipatso zambiri. 3Inu ndinu oyera kale chifukwa cha mawu amene ndayankhula inu. 4Khalani mwa Ine, monga Ine ndili mwa inu. Palibe nthambi imene ingabereke chipatso pa yokha ngati sinalumikizike ku mpesa. Chomwechonso inu simungathe kubereka chipatso pokhapokha mutakhala mwa Ine.

5“Ine ndine mpesa; inu ndinu nthambi zake. Ngati munthu akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye, adzabereka zipatso zambiri; popanda Ine simungathe kuchita kanthu. 6Ngati wina aliyense sakhala mwa Ine, iyeyo ali ngati nthambi imene yatayidwa ndi kufota. Nthambi zotero zimatoledwa, kuponyedwa pa moto ndi kupsa. 7Ngati inu mukhala mwa Ine ndipo mawu anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene mukufuna ndipo mudzapatsidwa. 8Atate anga amalemekezedwa mukamabereka zipatso zochuluka, ndipo potero mudzionetsa kuti ndinu ophunzira anga.

9“Monga momwe Atate amandikondera Ine, Inenso ndakukondani. Tsopano khalani mʼchikondi changa. 10Ngati mumvera malamulo anga, mudzakhala mʼchikondi changa, monga Ine ndimamvera malamulo a Atate anga, ndipo ndimakhala mʼchikondi chawo. 11Ine ndakuwuzani izi kuti chimwemwe changa chikhale mwa Inu, kuti chimwemwe chanu chikhale chokwanira. 12Lamulo langa ndi ili: ‘Kondanani wina ndi mnzake monga Ine ndakonda inu.’ 13Palibe munthu ali ndi chikondi choposa ichi, choti munthu nʼkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. 14Inu ndinu abwenzi anga ngati muchita zimene Ine ndikulamulani. 15Ine sindikutchulaninso antchito, chifukwa wantchito sadziwa zimene bwana wake akuchita. Mʼmalo mwake Ine ndakutchani abwenzi pakuti zilizonse zimene ndinaphunzira kwa Atate, Ine ndakudziwitsani. 16Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani kuti mupite ndi kukabereka zipatso, zipatso zake za nthawi yayitali. Choncho Atate adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa. 17Lamulo langa ndi ili: ‘Muzikondana.’

Dziko Lapansi Limada Ophunzira a Yesu

18“Ngati dziko lapansi lidana nanu, dziwani kuti linayamba kudana ndi Ine. 19Inu mukanakhala anthu a dziko lapansi, dziko lapansi likanakukondani ngati anthu ake omwe. Koma mmene zilili, inu si anthu a dziko lapansi. Ine ndakusankhani kuchokera mʼdziko lapansi, nʼchifukwa chake dziko lapansi limakudani. 20Kumbukirani mawu amene ndinayankhula nanu akuti, ‘Palibe wantchito amene amaposa bwana wake.’ Ngati anandizunza Ine, iwo adzakuzunzaninso inu. Ngati anamvera chiphunzitso changa, iwo adzamvera chanunso. 21Iwo adzakuchitani zimenezi chifukwa cha dzina langa, popeza sakudziwa amene anandituma Ine. 22Ine ndikanapanda kubwera ndi kuyankhula nawo, sakanakhala ndi mlandu. Koma tsopano alibe choti nʼkukanira mlandu wawo. 23Iye amene amadana ndi Ine amadananso Atate anga. 24Ine ndikanapanda kuchita pakati pawo zinthu zimene wina aliyense sanachitepo, iwo sakanakhala ochimwa. Koma tsopano aona zodabwitsa izi, komabe akundida Ine pamodzi ndi Atate anga. 25Koma zatere kuti zikwaniritse zimene zinalembedwa mʼmalamulo awo: ‘Iwo anandida Ine popanda chifukwa.’

Ntchito ya Mzimu Woyera

26“Nkhoswe ikadzabwera imene Ine ndidzakutumizireni kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu Woyera wachoonadi amene achokera kwa Atate, Iyeyo adzandichitira umboni Ine. 27Inunso mudzandichitira umboni Ine, popeza mwakhala nane kuchokera pachiyambi.”

King James Version

John 15:1-27

1I am the true vine, and my Father is the husbandman. 2Every branch in me that beareth not fruit he taketh away: and every branch that beareth fruit, he purgeth it, that it may bring forth more fruit. 3Now ye are clean through the word which I have spoken unto you. 4Abide in me, and I in you. As the branch cannot bear fruit of itself, except it abide in the vine; no more can ye, except ye abide in me. 5I am the vine, ye are the branches: He that abideth in me, and I in him, the same bringeth forth much fruit: for without me ye can do nothing. 6If a man abide not in me, he is cast forth as a branch, and is withered; and men gather them, and cast them into the fire, and they are burned. 7If ye abide in me, and my words abide in you, ye shall ask what ye will, and it shall be done unto you. 8Herein is my Father glorified, that ye bear much fruit; so shall ye be my disciples. 9As the Father hath loved me, so have I loved you: continue ye in my love. 10If ye keep my commandments, ye shall abide in my love; even as I have kept my Father’s commandments, and abide in his love. 11These things have I spoken unto you, that my joy might remain in you, and that your joy might be full. 12This is my commandment, That ye love one another, as I have loved you. 13Greater love hath no man than this, that a man lay down his life for his friends. 14Ye are my friends, if ye do whatsoever I command you. 15Henceforth I call you not servants; for the servant knoweth not what his lord doeth: but I have called you friends; for all things that I have heard of my Father I have made known unto you. 16Ye have not chosen me, but I have chosen you, and ordained you, that ye should go and bring forth fruit, and that your fruit should remain: that whatsoever ye shall ask of the Father in my name, he may give it you. 17These things I command you, that ye love one another. 18If the world hate you, ye know that it hated me before it hated you. 19If ye were of the world, the world would love his own: but because ye are not of the world, but I have chosen you out of the world, therefore the world hateth you. 20Remember the word that I said unto you, The servant is not greater than his lord. If they have persecuted me, they will also persecute you; if they have kept my saying, they will keep yours also. 21But all these things will they do unto you for my name’s sake, because they know not him that sent me. 22If I had not come and spoken unto them, they had not had sin: but now they have no cloke for their sin. 23He that hateth me hateth my Father also. 24If I had not done among them the works which none other man did, they had not had sin: but now have they both seen and hated both me and my Father. 25But this cometh to pass, that the word might be fulfilled that is written in their law, They hated me without a cause. 26But when the Comforter is come, whom I will send unto you from the Father, even the Spirit of truth, which proceedeth from the Father, he shall testify of me: 27And ye also shall bear witness, because ye have been with me from the beginning.