Yohane 14 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yohane 14:1-31

Yesu Atonthoza Ophunzira Ake

1“Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu; khulupirirani Inenso. 2Mʼnyumba mwa Atate anga muli zipinda zambiri. Kukanakhala kuti mulibemo ndikanakuwuzani. Ine ndikupita kumeneko kukakukonzerani malo. 3Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti kumene kuli Ineko, inunso mukakhale komweko. 4Inu mukudziwa njira ya kumene Ine ndikupita.”

Yesu Njira ya kwa Atate

5Tomasi anati kwa Iye, “Ambuye ife sitikudziwa kumene Inu mukupita, nanga tingadziwe bwanji njirayo?”

6Yesu anayankha kuti, “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine. 7Mukanandidziwadi Ine, mukanadziwanso Atate anga. Kuyambira tsopano, mukuwadziwa ndipo mwawaona.”

8Filipo anati, “Ambuye, tionetseni Atatewo ndipo ife tikhutitsidwa.”

9Yesu anayankha kuti, “Kodi iwe Filipo, ndakhala pakati panu nthawi yonseyi ndipo iwe sukundidziwabe? Aliyense amene waona Ine, waonanso Atate. Tsono ukunena bwanji kuti, ‘Tionetseni Atate?’ 10Kodi sukukhulupirira kuti Ine ndili mwa Atate, ndipo Atate ali mwa Ine? Mawu amene Ine ndiyankhula kwa inu si mawu anga okha koma ndi mawu Atate wokhala mwa Ine, amene akugwira ntchito yake. 11Khulupirirani Ine pamene ndi kuti Ine ndili mwa Atate ndipo Atate ali mwa Ine. Koma ngati si chomwecho, khulupiriranitu Ine chifukwa cha ntchito zanga zodabwitsa. 12Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene akhulupirira Ine adzachita zimene Ine ndakhala ndikuchita. Iye adzachita ngakhale zinthu zazikulu kuposa zimenezi, chifukwa ndikupita kwa Atate. 13Ndipo Ine ndidzachita chilichonse chimene inu mudzapempha mʼdzina langa kuti Atate alemekezedwe mwa Mwana. 14Ngati mudzapempha kanthu kalikonse mʼdzina langa, Ine ndidzachita.

Lonjezo la Mzimu Woyera

15“Ngati mundikonda Ine, sungani malamulo anga. 16Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthawi zonse. 17Nkhosweyo ndiye Mzimu wachoonadi. Dziko lapansi silingalandire Nkhosweyi chifukwa samuona kapena kumudziwa. Koma inu mumamudziwa pakuti amakhala nanu ndipo adzakhala mwa inu. 18Ine sindikusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ine ndidzabweranso kwa inu. 19Patsala nthawi yochepa dziko lapansi silidzandionanso koma inu mudzandiona. Popeza kuti Ine ndili ndi moyo, inunso mudzakhala ndi moyo. 20Tsiku limenelo inu mudzazindikira kuti Ine ndili mwa Atate, ndipo inu muli mwa Ine, ndipo Ine ndili mwa inu. 21Iye amene amadziwa malamulo anga ndi kuwasunga ndiye amene amandikonda. Wokonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga ndipo Inenso ndidzamukonda ndikudzionetsa ndekha kwa iye.”

22Kenaka Yudasi (osati Yudasi Isikarioti) anati, “Koma Ambuye, nʼchifukwa chiyani mukufuna kudzionetsa nokha kwa ife, osati ku dziko lapansi?”

23Yesu anamuyankha kuti, “Ngati wina aliyense andikonda Ine, adzasunga mawu anga. Atate wanga adzamukonda, ndipo Ife tidzabwera ndi kukhala naye. 24Iye amene sandikonda Ine sasunga mawu anga. Mawu awa amene mukumva si anga ndi a Atate amene anandituma Ine.

25“Ndayankhula zonsezi ndikanali nanu. 26Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamutumiza mʼdzina langa adzakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndinakuwuzani. 27Ine ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Ine sindikukupatsani monga dziko lapansi limaperekera. Mtima wanu usavutike ndipo musachite mantha.

28“Inu munamva Ine ndikunena kuti, ‘Ine ndikupita ndipo ndidzabweranso kwa inu.’ Mukanandikonda, mukanasangalala kuti Ine ndikupita kwa Atate, pakuti Atate ndi wamkulu kuposa Ine. 29Ine ndakuwuzani tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika mudzakhulupirire. 30Ine sindiyankhulanso nanu zambiri nthawi yayitali popeza wolamulira dziko lapansi akubwera. Iye alibe mphamvu pa Ine, 31koma kuti dziko lapansi lizindikire kuti Ine ndimakonda Atate ndi kuti ndimachita zokhazokha zimene Atate wandilamulira Ine.

“Nyamukani; tizipita.”

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

約翰福音 14:1-31

耶穌是道路、真理、生命

1耶穌繼續說:「你們心裡不要憂愁,你們要信上帝,也要信我。 2我父的家裡有許多住處,不然我就不會說去為你們安排地方了。 3我安排好了以後,必定回來接你們到我那裡。我在哪裡,讓你們也在哪裡。 4你們知道通往我要去的地方的路。」

5多馬說:「主啊,你要去哪裡,我們還不知道,又怎麼會知道路呢?」

6耶穌說:「我就是道路、真理、生命,若不藉著我,沒有人能到父那裡。 7你們若認識我,也會認識我的父。從現在起,你們不但認識祂,而且也看見祂了。」

8腓力說:「主啊!求你讓我們看看父,我們就心滿意足了。」

9耶穌說:「腓力,我和你們相處了這麼久,你還不認識我嗎?人看見了我,就看見了父,你怎麼說『讓我們看看父』呢? 10難道你不相信我在父裡面,父也在我裡面嗎?我這些話不是憑自己講的,而是住在我裡面的父在做祂自己的工作。 11你們應當相信我在父裡面,父也在我裡面。即使你們不信,也應該因我所做的而信我。 12我實實在在地告訴你們,我所做的事,信我的人也要做,而且要做更大的事,因為我要回到父那裡。 13你們奉我的名無論求什麼,我必應允,好讓父在子身上得到榮耀。 14你們若奉我的名向我求什麼,我必應允。

應許賜下聖靈

15「你們若愛我,就必遵守我的命令。 16我要求父另外賜一位護慰者給你們,祂要永遠和你們同在。 17祂是真理的靈,世人不接受祂,因為他們看不見祂,也不認識祂;但你們卻認識祂,因祂常與你們同在,並且要住在你們裡面。 18我不會撇下你們為孤兒,我必到你們這裡來。 19不久,世人就看不見我了,而你們卻能看見我,因為我活著,你們也要活著。 20到了那一天,你們就知道我在父裡面,你們在我裡面,我也在你們裡面。 21接受我的命令又遵行的,就是愛我的人。愛我的,父必定愛他,我也要愛他,並且要親自向他顯現。」

22猶大,不是後來出賣耶穌的猶大,問耶穌:「主啊,你為什麼只向我們顯現而不向世人顯現呢?」

23耶穌回答說:「愛我的人必遵行我的道,我父也必愛他,並且我們要到他那裡與他同住。 24不愛我的人不會遵行我的道。你們所聽見的道不是出於我自己,而是出於差我來的父。 25我還與你們在一起的時候,將這些事情都告訴了你們。 26但護慰者,就是父為我的名而差來的聖靈,將教導你們一切的事,並使你們想起我對你們說的一切話。 27我把平安留給你們,把我的平安賜給你們,我賜給你們的平安不像世人給的平安。你們心裡不要憂愁,也不要害怕。

28「我對你們說過,我去了還要再回到你們這裡。如果你們真的愛我,就應當為我去父那裡而歡喜快樂,因為父比我大。 29現在事情還沒有發生,我便先告訴你們,到了事情發生的時候,你們就會相信。 30我不再跟你們多談,因為世界的王快要來了。他根本沒有力量勝過我, 31但這是為了讓世人知道我愛父,父怎麼吩咐我,我就怎麼做。起來,我們走吧!」