Yohane 13 – CCL & SNC

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yohane 13:1-38

Yesu Asambitsa Mapazi a Ophunzira Ake

1Inali pafupifupi nthawi ya phwando la Paska. Yesu anadziwa kuti nthawi yafika yoti achoke mʼdziko lapansi ndi kupita kwa Atate. Atawakonda ake amene anali mʼdziko lapansi, Iye anawaonetsa chikondi chake chonse.

2Atayamba kudya mgonero, mdierekezi anali atalowa kale mu mtima wa Yudasi Isikarioti mwana wa Simoni, kuti amupereke Yesu. 3Yesu podziwa kuti Atate anamupatsa Iye zonse mʼmanja mwake, ndi kuti Iye anachokera kwa Mulungu ndipo amabwerera kwa Mulunguyo; 4anayimirira kuchoka pa chakudya navula zovala zake natenga nsalu yopukutira nadzimanga mʼchiwuno mwake. 5Atachita izi, anathira madzi mʼbeseni ndi kuyamba kusambitsa mapazi a ophunzira ake, ndi kuwapukuta ndi chopukutira chimene anachimanga mʼchiwuno mwake.

6Atafika pa Petro, Petroyo anati kwa Iye, “Ambuye, kodi mudzandisambitsa mapazi anga?”

7Yesu anayankha kuti, “Iwe sukuzindikira tsopano chimene ndikuchita, koma udzazindikira mʼtsogolo.”

8Petro anati, “Ayi, Inu simudzandisambitsa konse mapazi anga.”

Yesu anayankha kuti, “Ngati Ine sindisambitsa mapazi ako, ulibe gawo mwa Ine.”

9Simoni Petro anayankha kuti, “Ambuye, osati mapazi okha komanso manja anga ndi mutu wanga womwe!”

10Yesu anayankha kuti, “Munthu amene wasamba amangofunika kusamba mapazi ake okha chifukwa thupi lake lonse ndi loyera. Ndipo inu ndinu oyera, ngakhale kuti si aliyense mwa inu.” 11Pakuti Iye anadziwa amene adzamupereka, ndipo nʼchifukwa chake anati saliyense wa inu ali woyera.

12Iye atamaliza kusambitsa mapazi awo anavala zovala zake ndi kubwerera pamalo pake. Iye anawafunsa kuti, “Kodi mukuzindikira zimene ndakuchitirani inu? 13Inu mumanditcha Ine, ‘Mphunzitsi’ ndi ‘Mbuye,’ ndipo mumakhoza mukamatero, pakuti ichi ndi chimene Ine ndili. 14Tsono ngati Ine, Mbuye wanu ndi Mphunzitsi wanu, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi anu. 15Ine ndakupatsani chitsanzo kuti muzichita monga Ine ndachitira. 16Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti wantchito saposa mbuye wake, kapena wotumidwa kuposa amene wamutuma. 17Ngati inu mudziwa zinthu zimenezi, mudzakhala odala mukamazichita.

Yesu Aneneratu za Kuperekedwa Kwake

18“Ine sindikunena za inu nonse. Ine ndikudziwa amene ndinawasankha. Koma izi zikukwaniritsa malemba: ‘Iye amene akudya nawo chakudya changa, ndiye amene anandiwukira.’

19“Ine ndikukuwuzani tsopano zisanachitike zimenezi, kuti pamene zachitika, mudzakhulupirire kuti Ine Ndine. 20Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene alandira amene Ine ndamutuma, alandiranso Ine. Aliyense amene alandira Ine, alandiranso amene anandituma.”

Yesu Aneneratu za Kuperekedwa Kwake

21Yesu atanena izi, anavutika kwambiri mu mzimu ndipo anachitira umboni kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mmodzi mwa inu adzandipereka.”

22Ophunzira ake anapenyetsetsana wina ndi mnzake, posadziwa kuti amanena za yani. 23Mmodzi wa ophunzira ake amene Yesu anamukonda, anali atatsamira pachifuwa chake. 24Simoni Petro anamukodola wophunzirayo ndi kuti, “Mufunseni akunena za yani.”

25Atamutsamiranso Yesuyo, anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi ndani?”

26Yesu anayankha kuti, “Iye amene ndidzamupatsa buledi amene ndanyema ndikususa ndi ameneyo.” Kenaka, atasunsa gawo la buledi, Iye anapereka kwa Yudasi Isikarioti, mwana wa Simoni. 27Nthawi yomweyo Yudasi atangodya bulediyo, Satana analowa mwa Iye.

Yesu anamuwuza Iye kuti, “Chomwe ukufuna kuchita, chita msanga.” 28Koma panalibe ndi mmodzi yemwe pa chakudyapo amene anamvetsa chifukwa chimene Yesu ananenera izi kwa iye. 29Popeza Yudasi amasunga ndalama, ena amaganiza kuti Yesu amamuwuza iye kuti akagule zomwe zimafunika pa phwando, kapena kukapereka kanthu kena kake kwa osauka. 30Nthawi yomweyo Yudasi atangodya buledi, anatuluka, ndipo unali usiku.

Yesu Aneneratu kuti Petro Adzamukana

31Yudasi atatuluka, Yesu anati, “Tsopano Mwana wa Munthu walemekezedwa, ndipo mwa Iyeyu Mulungu walemekezedwanso. 32Ngati Mulungu walemekezedwa mwa Iye, Mulungu mwini adzalemekezanso Mwana, ndipo amulemekeza nthawi yomweyo.

33“Ana anga, Ine ndikhala nanu kwa nthawi yochepa chabe. Inu mudzandifunafuna Ine, ndipo monga momwe ndinawawuzira Ayuda, choncho Ine ndikukuwuzani tsopano kuti, kumene Ine ndikupita, inu simungabwereko.

34“Lamulo latsopano limene ndikukupatsani ndi lakuti: Kondanani wina ndi mnzake, monga momwe Ine ndinakonda inu. Nanunso mukondane wina ndi mnzake. 35Mukamakondana aliyense adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga.”

36Simoni Petro anafunsa kuti, “Ambuye, kodi mukupita kuti?”

Yesu anayankha kuti, “Kumene Ine ndikupita iwe sunganditsatire tsopano, koma udzanditsatira mʼtsogolo.”

37Petro anafunsa kuti, “Ambuye, nʼchifukwa chiyani ine sindingakutsatireni tsopano? Ine ndidzapereka moyo wanga chifukwa cha Inu.”

38Kenaka Yesu anayankha kuti, “Kodi iwe udzalolera kutaya moyo chifukwa cha Ine? Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti tambala asanalire, iwe udzandikana katatu!”

Slovo na cestu

Jan 13:1-38

Ježíš umývá učedníkům nohy

1Ježíš věděl, že nastávající Velikonoce jsou posledními dny jeho života na zemi, než se vrátí k Otci. Miloval ty, mezi nimiž žil, a prokazoval jim lásku až do konce. 2V předvečer svátků večeřel Ježíš společně se svými učedníky. To už Jidáš pojal ďábelský záměr zradit svého Mistra. 3Ježíš si byl vědom velikosti svého poslání a moci jako ten, kdo byl a bude rovný Bohu. Když viděl, že se nikdo z učedníků nechtěl snížit k službě, kterou obvykle konali otroci, vstal od stolu, 4odložil svrchní oděv a opásal se ručníkem. 5Nalil vodu do umývadla a začal učedníkům umývat a utírat zaprášené nohy. 6Když došlo na Petra, ten se začal bránit: „Pane, ty mi přece nebudeš mýt nohy!“

7Ježíš odpověděl: „Jestliže tě neočistím, ztratíš se mnou spojení a odcizíš se mi.“

8-9A tak Petr najednou obrátil: „Když je to tak, Pane, umyj mne celého.“

10-11Ježíš mu na to řekl: „Koho Bůh už jednou očistil, ten se potřebuje zbavovat jen každodenní špíny a vy jste čistí, ale ne všichni.“ Tím myslel na svého zrádce.

12Když umyl nohy poslednímu, oblékl se, vrátil se ke stolu a zeptal se jich: „Pochopili jste, proč jsem to udělal? 13-14Jestliže jsem vám umyl nohy já, váš Pán a Mistr, i vy si máte navzájem sloužit v pokorné lásce. 15Dal jsem vám příklad. A vy se jím řiďte a jednejte jako já. 16Je nepochybné, že sluha není větší než jeho pán a vyslanec není významnější než hlava státu. 17Tak teď to víte, a když se podle toho budete řídit, přinese vám to radost.

18-20Na jedno se můžete spolehnout: kdo přijímá moje posly, přijímá mne, a tím i Otce.

To, co jsem řekl, netýká se všech. Vím, koho jsem vyvolil. Plní se výrok Písma: ‚Ten, kdo se mnou jídal, podrazil mi nohy.‘ Až se to stane, pochopíte, že to byla řeč o mně a mém zrádci.“

Ježíš naposledy večeří s učedníky

21Když to Ježíš řekl, teprve to na něj v plné síle dolehlo a dodal otevřeně: „Je to tak, jeden z vás mne zradí.“ 22Učedníci se tázavě dívali jeden na druhého, o kom to vlastně mluví. 23-25Petr se naklonil k učedníkovi, který byl u stolu Ježíšovi nejblíže, a naznačil mu, aby se zeptal. Ten se obrátil k Mistrovi: „Pane, kdo to je?“

26„Ten, kterému podám chléb,“ odpověděl Ježíš. Namočil kousek chleba do omáčky a podával ho Jidášovi.

27V tu chvíli naplnil Jidáše hněv. Ježíš mu řekl: „Neotálej a proveď rychle, co chceš.“ 28Učedníci nechápali, o čem je řeč. Někteří si dokonce mysleli, že Jidáš má nakoupit nějaké jídlo na svátky nebo že má rozdat peníze chudým; 29byl totiž jejich pokladníkem. 30Jidáš přijal podávaný chléb, zvedl se a odešel. Byla noc.

Ježíš předpovídá Petrovo zapření

31-33Po Jidášově odchodu Ježíš řekl: „Je rozhodnuto, půjdu poslušně cestou, která se líbí Bohu, cestou Božího vítězství. Moji milí, už s vámi dlouho nebudu. Marně mne budete hledat. Na mojí cestě mne nemůžete doprovodit. 34Odkazuji vám, abyste se navzájem milovali, jako jsem já miloval vás. 35Vaše vzájemná láska dokáže světu, že jste mými žáky.“

36„Mistře, kam chceš odejít?“ zeptal se Petr.

„Teď se mnou nemůžeš jít,“ odpověděl mu Ježíš, „budeš mne následovat později.“

37„Proč s tebou nemohu jít už teď?“ ptal se znovu Petr. „Jsem ochoten dát za tebe život!“

38„Život za mne chceš dát?“ zeptal se Ježíš. „Uvidíš, že mne třikrát zapřeš, než ráno zakokrhá kohout.“