Yobu 7 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 7:1-21

1“Kodi munthu sakhala ndi ntchito yowawa pa dziko lapansi?

Kodi masiku ake sali ngati munthu waganyu?

2Monga ngati kapolo wolakalaka mthunzi wa nthawi yamadzulo,

kapena ngati munthu waganyu woyembekezera malipiro ake,

3choncho ine ndapatsidwa nthawi yongovutika pachabe,

ndiponso usiku wamasautso wapatsidwa kwa ine.

4Ndikamagona ndimaganiza kuti, ‘Kodi kucha liti?’

Usikuwo umatalika ndipo sindigona tulo mpaka mmawa.

5Thupi langa ladzala mphutsi ndi zipsera,

khungu langa langʼambika ndipo likutuluka mafinya.

6“Masiku anga ndi othamanga kupambana makina wolukira nsalu,

ndipo amatha wopanda chiyembekezo.

7Inu Mulungu kumbukirani kuti moyo wanga uli ngati mpweya;

sindidzaonanso masiku achisangalalo.

8Amene akundiona tsopano akundiona;

mudzandifunafuna koma sindidzapezekanso.

9Monga mtambo umazimirira ndi kukanganuka,

momwemonso munthu amene walowa mʼmanda sabwerera.

10Iye sadzabweranso ku nyumba kwake

ndipo onse omudziwa adzamuyiwala.

11“Nʼchifukwa chake ine sindidzakhala chete;

ndidzayankhula mopsinjika mtima,

ndidzadandaula mowawidwa mtima.

12Kodi ine ndine nyanja kapena chirombo chamʼnyanja

kuti inu mundiyikire alonda?

13Pamene ndikuganiza kuti ndidzapeza chitonthozo pa bedi panga

ndipo pogona panga padzachepetsa madandawulo anga,

14ngakhale nthawi imeneyo mumandiopseza ndi maloto

ndi kundichititsa mantha ndi masomphenya,

15kotero kuti ndimalakalaka kudzikhweza kapena kufa,

kupambana kupirira zowawa zimene ndikuzimva mʼthupi mwanga.

16Ine ndatopa nawo moyo wanga; sindingakonde kukhala moyo nthawi zonse.

Ndisiyeni ndekha pakuti moyo wanga ulibe tanthauzo.

17“Kodi munthu nʼchiyani kuti muzimuganizira chotere,

kuti muzisamala zochita zake,

18kuti muzimusanthula mmawa uliwonse

ndi kumamuyesa nthawi yonse?

19Kodi simudzaleka kumandizonda

kuti ndipezeko mpata wopumula?

20Ngati ine ndachimwa, ndachita chiyani kwa Inu,

Inu wopenyetsetsa anthu?

Chifukwa chiyani mwachititsa kuti ndikhale ngati choponyera chandamale chanu?

Kodi ndasanduka katundu wolemera kwa Inu?

21Chifukwa chiyani simukundikhululukira zolakwa zanga

ndi kundichotsera machimo anga?

Pakuti posachedwa ndilowa mʼmanda;

mudzandifunafuna ine koma simudzandionanso.”