Yobu 5 – CCL & NVI-PT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 5:1-27

1“Itana ngati ungathe, koma ndani adzakuyankhe?

Kodi ndi kwa mngelo uti ungapezeko thandizo?

2Mkwiyo umapha chitsiru,

ndipo njiru imawononga wopusa.

3Ine ndinaona chitsiru chitamera mizu,

koma mwadzidzidzi nyumba yake inatembereredwa.

4Ana ake alibe ndi chitetezo chomwe;

amaponderezedwa mʼbwalo la milandu popanda owateteza.

5Anthu anjala amamudyera zokolola zake,

amamutengera ndi za pa minga pomwe,

ndipo anthu akhwinthi amafunkha chuma chake.

6Pakuti masautso satuluka mʼfumbi,

ndipo kuwukira sikuchokera mʼdothi.

7Komatu munthu amabadwira kuti azunzike

monga momwe mbaliwali zimathethekera mlengalenga.

8“Koma ndikanakhala ine, ndikanamudandawulira Mulungu;

ndikanapereka mlandu wanga kwa Iye.

9Iye amachita zozizwitsa zimene sizimvetsetseka,

zodabwitsa zimene sizingatheke kuwerengedwa.

10Iye amagwetsa mvula pa dziko lapansi,

ndipo amathirira minda ya anthu.

11Iye amakweza anthu wamba,

ndipo iwo amene akulira amawayika pa malo otetezedwa.

12Iyeyo amalepheretsa chiwembu cha anthu ochenjera,

kotero kuti cholinga chawo sichipindula kanthu.

13Iye amakola anthu ochenjera mu msampha wa kuchenjera kwawo,

ndipo zolinga za atambwali amazithetsa msangamsanga.

14Mdima umawagwera nthawi yamasana;

nthawi yamasana amayenda moyambasayambasa monga nthawi ya usiku.

15Mulungu amapulumutsa amphawi ku lupanga la mʼkamwa mwawo;

amawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amphamvu.

16Choncho osauka ali ndi chiyembekezo,

ndipo anthu opanda chilungamo amawatseka pakamwa.

17“Wodala munthu amene Mulungu amamudzudzula;

nʼchifukwa chake usanyoze chilango cha Wamphamvuzonse.

18Pakuti Iye amavulaza koma amamanganso mabalawo;

Iye amakantha munthu, komanso manja ake amachiritsa.

19Pakuti adzakupulumutsa ku masautso nthawi ndi nthawi,

mavuto angachuluke bwanji, sadzakukhudza ndi pangʼono pomwe.

20Pa nthawi ya njala adzakulanditsa ku imfa,

ndipo nthawi ya nkhondo adzakupulumutsa ku lupanga.

21Adzakuteteza kwa anthu osinjirira,

ndipo palibe chifukwa chochitira mantha pamene chiwonongeko chafika.

22Uzidzaseka pa nthawi ya chiwonongeko ndi ya njala,

ndipo palibe chifukwa chochitira mantha ndi zirombo za mʼdziko lapansi.

23Pakuti udzachita pangano ndi miyala ya mʼmunda mwako,

ndipo nyama zakuthengo zidzakhala nawe mwamtendere.

24Udzadziwa kuti nyumba yako ndi malo otetezedwa;

udzawerengera katundu wako ndipo sudzapeza kanthu kamene kasowapo.

25Udzadziwa kuti ana ako adzakhala ambiri,

ndipo zidzukulu zako zidzakhala ngati udzu wa mʼdziko lapansi.

26Udzafika ku manda utakalamba,

monga mitolo ya zokolola pa nyengo yake.

27“Ife tafufuza zimenezi ndipo ndi zoona,

choncho uzimvere ndi kuzitsata.”

Nova Versão Internacional

Jó 5:1-27

1“Clame, se quiser, mas quem o ouvirá?

Para qual dos seres celestes5.1 Hebraico: santos. você se voltará?

2O ressentimento mata o insensato,

e a inveja destrói o tolo.

3Eu mesmo já vi um insensato lançar raízes,

mas de repente a sua casa foi amaldiçoada.

4Seus filhos longe estão de desfrutar segurança,

maltratados nos tribunais, não há quem os defenda.

5Os famintos devoram a sua colheita,

tirando-a até do meio dos espinhos,

e os sedentos sugam a sua riqueza.

6Pois o sofrimento não brota do pó,

e as dificuldades não nascem do chão.

7No entanto, o homem nasce para as dificuldades

tão certamente como as fagulhas voam para cima.

8“Mas, se fosse comigo, eu apelaria para Deus;

apresentaria a ele a minha causa.

9Ele realiza maravilhas insondáveis,

milagres que não se pode contar.

10Derrama chuva sobre a terra

e envia água sobre os campos.

11Os humildes, ele exalta

e traz os que pranteiam a um lugar de segurança.

12Ele frustra os planos dos astutos,

para que fracassem as mãos deles.

13Apanha os sábios na astúcia deles,

e as maquinações dos astutos são malogradas por sua precipitação.

14As trevas vêm sobre eles em pleno dia;

ao meio-dia eles tateiam como se fosse noite.

15Ele salva o oprimido da espada que trazem na boca;

salva-o das garras dos poderosos.

16Por isso os pobres têm esperança,

e a injustiça cala a própria boca.

17“Como é feliz o homem a quem Deus corrige;

portanto, não despreze a disciplina do Todo-poderoso5.17 Hebraico: Shaddai; também em todo o livro de Jó..

18Pois ele fere, mas trata do ferido;

ele machuca, mas suas mãos também curam.

19De seis desgraças ele o livrará;

em sete delas você nada sofrerá.

20Na fome ele o livrará da morte

e na guerra o livrará do golpe da espada.

21Você será protegido do açoite da língua

e não precisará ter medo quando a destruição chegar.

22Você rirá da destruição e da fome

e não precisará temer as feras da terra.

23Pois fará aliança com as pedras do campo,

e os animais selvagens estarão em paz com você.

24Você saberá que a sua tenda é segura;

contará os bens da sua morada e de nada achará falta.

25Você saberá que os seus filhos serão muitos,

e que os seus descendentes serão como a relva da terra.

26Você irá para a sepultura em pleno vigor,

como um feixe recolhido no devido tempo.

27“Verificamos isso e vimos que é verdade.

Portanto, ouça e aplique isso à sua vida”.