Yobu 42 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 42:1-17

Yobu

1Pamenepo Yobu anayankha Yehova kuti,

2“Ndikudziwa kuti Inu mungathe kuchita zinthu zonse;

chimene mufuna kuchita wina sangaletse konse.

3Munandifunsa kuti, ‘Kodi ndiwe yani amene ukufuna kusokoneza uphungu wanga ndi mawu opanda nzeru?

Zoonadi ndinayankhula zimene sindinazimvetse,

zinthu zodabwitsa kwambiri kwa ine zimene sindinazidziwe.

4“Inu munandiwuza kuti, ‘Mvetsetsa tsopano ndipo ndidzayankhula;

ndidzakufunsa

ndipo iwe udzandiyankhe.’

5Ndinkangomva za Inu ndi makutu anga,

koma tsopanonso ndakuonani ndi maso anga.

6Nʼchifukwa chake ndi kuchita manyazi,

ndikulapa podzithira fumbi ndi phulusa.”

Mulungu Adalitsa Yobu

7Yehova atayankhula ndi Yobu mawu amenewa anawuza Elifazi wa ku Temani kuti, “Ine ndakukwiyira pamodzi ndi abwenzi ako awiri, chifukwa simunayankhule zabwino za Ine, monga mmene wayankhulira mtumiki wanga Yobu. 8Kotero tsopano mutenge ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi kupita nazo kwa mtumiki wanga Yobu kuti mukapereke nsembe zopsereza. Mtumiki wanga Yobu adzakupemphererani, ndipo Ine ndidzalandira pemphero lake. Sindidzakuchitirani kanthu molingana ndi uchitsiru wanu. Inu simunayankhule zabwino za Ine, monga anayankhulira Yobu mtumiki wanga.” 9Motero Elifazi wa ku Temani, Bilidadi wa ku Suki ndi Zofari wa ku Naama anachita zimene Yehova anawawuza ndipo Yehova anamvera pemphero la Yobu.

10Yobu atawapempherera abwenzi ake aja, Yehova anamubwezera chuma chake ndipo anamupatsa mowirikiza kuposa zomwe anali nazo kale. 11Abale ake ndi alongo ake onse, kuphatikizapo onse amene ankamudziwa kale, amabwera kwa iye nʼkudzadya naye chakudya mʼnyumba mwake. Iwo anamutonthoza ndi kumupepesa chifukwa cha mavuto onse amene Yehova analola kuti amugwere. Aliyense wa iwowa anamupatsa ndalama ndi mphete yagolide.

12Yehova anadalitsa Yobu pa masiku ake otsirizawa kupambana poyamba paja. Iye anali ndi nkhosa 14,000, ngamira 6,000, ngʼombe zantchito 2,000 ndi abulu aakazi 1,000. 13Anaberekanso ana aamuna asanu ndi awiri ndi ana aakazi atatu. 14Mwana wake wamkazi woyamba anamutcha Yemima, wachiwiri anamutcha Keziya, wachitatu anamutcha Kereni Hapuki. 15Mʼdziko monsemo munalibe akazi okongola ngati ana a Yobu, ndipo abambo awo anawapatsa cholowa pamodzi ndi alongo awo.

16Zitachitika zimenezi, Yobu anakhala ndi moyo zaka 140. Iye anaona zidzukulu zake mpaka mʼbado wachinayi. 17Potsiriza, Yobu anamwalira ali nkhalamba ya zaka zochuluka kwambiri.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

約伯記 42:1-17

1約伯回答耶和華說:

2「我知道你無所不能,

你的旨意無不成就。

3你問,『誰用無知的話使我的旨意晦暗不明?』

誠然,我對自己所談論的事一無所知,

這些事太奇妙,我無法明白。

4你說,『你且聽著,我要發言。

我來提問,你來回答。』

5我從前風聞有你,

現在親眼看見你。

6因此我厭惡自己,

在塵土和爐灰中懺悔。」

結語

7耶和華對約伯說完這些話後,就對提幔以利法說:「你和你的兩個朋友令我憤怒,因為你們對我的議論不如我僕人約伯說的有理。 8現在你們要取七頭公牛和七隻公羊,到我僕人約伯那裡,為自己獻上燔祭,因為你們對我的議論不如我僕人約伯說的有理。我僕人約伯會為你們禱告,我會悅納他的禱告,不按你們的愚妄懲罰你們。」 9於是,提幔以利法書亞比勒達拿瑪瑣法遵命而行,耶和華悅納了約伯的禱告。

10約伯為朋友們禱告後,耶和華恢復了他以前的昌盛,並且耶和華賜給他的比以前多一倍。 11約伯的兄弟姊妹和從前的朋友都來探望他,在他家裡一同吃飯,為他遭受耶和華所降的種種災難而安撫、慰問他。他們每人送他一塊銀子和一個金環。

12耶和華賜給約伯晚年的福分比起初更多:他有一萬四千隻羊、六千隻駱駝、一千對牛和一千頭母驢。 13他還有七個兒子和三個女兒。 14他給長女取名叫耶米瑪、次女叫基洗亞、三女叫基連·哈樸15那地方找不到像約伯三個女兒那樣美麗的女子。約伯讓她們與弟兄一同承受產業。 16此後,約伯又活了一百四十年,得見四代子孫。 17約伯年紀老邁,壽終正寢。