Yobu 41 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 41:1-34

1“Kodi ungathe kukoka ngʼona ndi mbedza ya nsomba

kapena kukanikiza lilime lake pansi ndi chingwe?

2Kodi ungathe kumanga chingwe mʼmphuno mwake,

kapena kubowola nsagwada zake ndi mbedza?

3Kodi ngʼonayo idzakupempha kuti uyichitire chifundo?

Kodi idzakuyankhula ndi mawu ofatsa?

4Kodi idzachita nawe mgwirizano

kuti uyisandutse kapolo wako mpaka muyaya?

5Kodi udzasewera nayo ngati mbalame,

kapena kuyimangirira kuti atsikana ako asewere nayo?

6Kodi anthu adzayitsatsa malonda?

Nanga amalondawo nʼkugawanagawana nyama yake kuti akagulitse?

7Kodi chikopa chake ungathe kuchilasa ndi zisonga,

kapena kubowola mutu wake ndi nthungo zophera nsomba?

8Ukayiputa udziwe kuti pali nkhondo,

ndipo iweyo sudzabwereranso.

9Chiyembekezo choti nʼkuyigonjetsa ndi chabodza;

kungoyiona kokha, ndithu iwe kumangodzigwera wekha.

10Palibe wolimba mtima kuti ndi kuyiputa.

Ndani angalimbe mtima kulimbana ndi Ine?

11Kodi ndani anandipatsa kanthu kuti ndimubwezere?

Zonse za pansi pa thambo ndi zanga.

12“Sindidzaleka kuyankhula za ziwalo zake za chirombocho,

za mphamvu zake ndiponso za maonekedwe a thupi lake.

13Ndani angasende chikopa chake?

Ndani angayiyandikire kuti abowole chikopa chake cholimbacho?

14Ndani angatsekule kukamwa kwake,

pakamwa pamene pazunguliridwa ndi mano ochititsa mantha?

15Kumsana kwake kuli mizere ya mamba

onga zishango zolumikizanalumikizana;

16Mambawo ndi olukanalukana

kotero kuti mpweya sungathe kulowa pakati pake.

17Ndi olumikizanalumikizana;

ndi omatirirana kwambiri kotero kuti sangathe kulekana.

18Kuyetsemula kwake kumatulutsa mbaliwali;

maso ake amawala ngati kuwala kwa mʼbandakucha.

19Mʼkamwa mwake mumatuluka nsakali zamoto ndipo

mumathetheka mbaliwali zamoto.

20Mʼmphuno mwake mumatuluka utsi

ngati wa mʼnkhali yowira yomwe ili pa moto wa bango.

21Mpweya wake umayatsa makala,

ndipo malawi amoto amatuluka mʼkamwa mwake.

22Mphamvu zake zili mʼkhosi mwake;

aliyense wokumana nayo amangoti njenjenje ndi mantha.

23Minyewa ya thupi lake ndi yolumikizana ndipo

ndi yokhwima kwambiri ndi yolimba.

24Pachifuwa pake ndi powuma ngati mwala,

ndi pa gwaa, ngati mwala wamphero.

25Ngʼonayo ikangovuwuka,

ndi anthu amphamvu omwe amaopa; amabwerera mʼmbuyo, kuthawa.

26Ngakhale ikanthidwe ndi lupanga, lupangalo silichita kanthu,

ngakhale mkondo, muvi ndi nthungo, zonse zimalephera.

27Chitsulo imachiyesa ngati phesi chabe

ndi mkuwa ngati chikuni chowola.

28Muvi sungathe kuyithawitsa,

miyala imene ayilasa nayo imangoyinyenyanyenya.

29Zibonga zimakhala ngati ziputu;

imangoseka pamene akuyibaya ndi nthungo.

30Mamba a ku mimba kwake ali ngati chopunthira chakunthwa ndipo

imasiya mkukuluzi mʼmatope ngati galeta lopunthira tirigu.

31Imagadutsa madzi ozama ngati madzi a mʼnkhali,

imachititsa nyanja kuti iwire ngati mbiya yoyengera mafuta.

32Kumbuyo kwake imasiya nthubwitubwi zambee,

kotero kuti munthu angaganize kuti nyanja yachita imvi.

33Pa dziko lapansi palibe china chofanana nacho,

nʼcholengedwa chopanda mantha.

34Chimanyoza nyama zina zonse;

icho chija ndi mfumu ya nyama zonse.”