Yobu 40 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 40:1-24

1Yehova anati kwa Yobu:

2“Kodi iwe ufuna kukangana ndi Wamphamvuzonse?

Iwe amene unatsutsana ndi Mulungu umuyankhe Iyeyo!”

3Pamenepo Yobu anayankha Yehova:

4“Ine sindili kanthu konse,

kodi ndingathe kukuyankhani chiyani? Ndagwira pakamwa panga.

5Ndinayankhula kamodzi, koma pano ndilibe yankho,

ndinayankha kawiri, koma sindiwonjezeranso mawu ena.”

6Ndipo Yehova anayankha Yobu mʼkamvuluvulu kuti,

7“Tsopano vala dzilimbe ngati mwamuna;

ndikufunsa mafunso

ndipo iwe undiyankhe.

8“Kodi iwe unganyoze chiweruzo changa cholungama?

Kodi ungandidzudzule kuti iweyo ukhale wolungama?

9Kodi uli ndi dzanja monga la Mulungu,

ndipo mawu ako angagunde ngati mphenzi monga a Mulungu?

10Ngati zili choncho udzikometsere ndi ulemerero ndi kukongola,

ndipo udziveke ulemu ndi ulemerero waufumu.

11Tsanula ukali wako wosefukirawo,

uyangʼane aliyense wodzikuza ndipo umuchepetse,

12Uyangʼane aliyense wodzikweza ndipo umutsitse,

uwapondereze oyipa onse pamalo pomwe alilipo.

13Onsewo uwakwirire pamodzi mfumbi;

ukulunge nkhope zawo mʼmanda.

14Ukatero Ine ndidzakuvomereza

kuti dzanja lako lamanja lakupulumutsadi.

15“Taganiza za mvuwu,

imene ndinayipanga monga momwe ndinapangira iwe,

ndipo imadya udzu ngati ngʼombe.

16Mphamvu zake ndi zazikulu kwambiri,

thupi lake ndi lanyonga kwambiri!

17Mchira wake umayima tolotolo ngati mtengo wamkungudza;

mitsempha ya ntchafu zake ndi yogwirana bwino.

18Mafupa ake ali ngati mapayipi amkuwa,

nthiti zake zili ngati mipiringidzo yachitsulo.

19Mvuwuyo ndi yayikulu mwa zolengedwa za Mulungu,

komatu mlengi wake amatha kuyiopseza ndi lupanga lake.

20Imapeza chakudya chake ku mtunda

ndipo nyama zakuthengo zonse zimasewera pambali pake.

21Imagona pa tsinde pa zitsamba za mipeta,

imabisala mʼbango ndiponso pa thawale.

22Imaphimbika ndi mthunzi wazitsamba za mipeta;

imazunguliridwa ndi misondozi ya mu mtsinje.

23Madzi a mu mtsinje akakokoma, sichita mantha,

iyo sitekeseka, ngakhale madzi a mu Yorodani afike mʼkhosi mwake.

24Kodi alipo amene angathe kukola mvuwu ndi mbedza

kapena kuyikola mu msampha?