Yobu 39 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 39:1-30

1“Kodi iwe umadziwa nthawi imene mbalale yayikazi imaswera?

Kodi umaonerera pamene nswala ikubala?

2Kodi umawerenga miyezi imene zimakhala ndi bere?

Kodi nthawi imene zimaswana iwe umayidziwa?

3Zimakhala tsonga ndi kuswa ana awo;

pamenepo ululu wobereka nʼkutha.

4Ana a nyamazi amakhala ndi mphamvu ndipo amakulira mʼthengo;

kenaka amachoka ndipo sabwereranso.

5“Kodi bulu wakuthengo amamupatsa ndani ufulu wongodziyendera?

Ndani amamasula zingwe zake?

6Ine ndinamupatsa chipululu kuti chikhale mudzi wake,

nthaka ya mchere kuti ikhale malo ake okhalamo

7Iye amakhala kutali ndi phokoso la mu mzinda;

ndipo samva kufuwula kwa oyendetsa nyama zakatundu.

8Amayendayenda mʼmapiri kudya msipu

ndipo amafunafuna msipu uliwonse wobiriwira.

9“Kodi njati ingavomere kukutumikira?

Kodi ingagone mu gome lako usiku?

10Kodi ungathe kuyimanga ndi zingwe kuti izilima?

Kodi ingasalaze nthumbira mʼmunda mwako?

11Kodi ungadalire njatiyo chifukwa champhamvu zake?

Kodi ungayilekere kuti igwire ntchito zako zolemetsa?

12Kodi ungadalire kuti idzakubweretsera tirigu wako

ndi kumuyika ku malo opunthira?

13“Nthiwatiwa imakupiza mapiko ake monyadira,

koma mapikowo sangafanane ndi mapiko ndi nthenga za kakowa.

14Nthiwatiwa imakwirira mazira ake pansi

ndipo amafundidwa ndi nthaka,

15nthiwatiwayo sidera nkhawa kuti mazira ake angathe kuswanyidwa,

ndi kuti nyama zakuthengo zitha kuwaponda.

16Nthiwatiwa imachitira nkhanza ana ake ngati anawo si ake;

Imayiwala zoti inavutika powabala.

17Chifukwa Mulungu anayimana nzeru,

simvetsa kanthu kalikonse.

18Komatu nthiwatiwa ikadzambatuka ndi kuyamba kuthamanga,

imamusiya kutali kavalo ndi wokwerapo wake.

19“Kodi ndiwe amene umamupatsa mphamvu kavalo

kapena kumuveka chenjerere mʼkhosi mwake?

20Kodi ndiwe amene umalipatsa dzombe ulemerero wolumphira,

ukali wake nʼkumachititsa mantha?

21Iye amalumphalumpha moopseza, kukondwerera mphamvu zake,

ndipo amapita ku nkhondo ndi mphamvu zake zonse.

22Iye sachita mantha, saopa chilichonse;

sabwerera mʼmbuyo akaona lupanga.

23Zida zankhondo zimachita kwichikwichi mʼchimake pambali pake

pamodzi ndi mkondo wonyezimira ndi nthungo.

24Kavaloyo amanjenjemera ndi ukali ndi kulumphalumpha;

satha kungoyima pamene wamva kulira kwa lipenga.

25Lipenga likalira amati, ‘Twee!’

Amamva fungo la nkhondo ali patali,

kufuwula kwa anthu olamulira nkhondo ndi mfuwu wankhondo.

26“Kodi kabawi amawuluka ndi nzeru zako,

ndi kutambasula mapiko ake kupita kummwera?

27Kodi umalamulira chiwombankhanga ndiwe kuti chiziwuluka

ndi kumanga chisa chake pamwamba penipeni?

28Chimakhala pa phiri ndipo chimakhala pamenepo usiku;

chimakhala pa msonga penipeni pa mwala.

29Chili pamenepo chimayangʼanayangʼana choti chigwire kuti chidye;

maso ake amachionera patali chinthucho.

30Ana ake amayamwa magazi,

ndipo kumene kuli mitembo ndiko chimapezeka.”