Yobu 37 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 37:1-24

1“Mtima wanga ukulumphalumpha pa chimenechinso

ndipo ukuchoka mʼmalo mwake.

2Tamverani! Tamverani kubangula kwa liwu lake,

kugunda kumene kukuchokera mʼkamwa mwake.

3Iye amaponya chingʼaningʼani chake pansi pa thambo lonse

ndipo amachitumiza ku dziko lapansi.

4Pambuyo pake kubangula kwake kumamveka.

Iye amabangula ndi liwu lake laulemerero.

Pamene wabangula,

palibe chimene amalephera kuchita.

5Liwu la Mulungu limabangula mʼnjira zambiri zodabwitsa

Iye amachita zinthu zazikulu zimene sitingathe kuzimvetsa.

6Amalamula chisanu chowundana kuti, ‘Igwa pa dziko lapansi,’

ndipo amalamulanso mvula yamawawa kuti, ‘Khala mvula yamphamvu.’

7Kuti anthu onse amene anawalenga athe kuzindikira ntchito yake.

Iye amalepheretsa anthu kugwira ntchito zawo.

8Zirombo zimakabisala

ndipo zimakhala mʼmaenje mwawo.

9Mphepo yamkuntho imatuluka ku malo ake,

kuzizira kumatuluka mʼmphepo yamkunthoyo.

10Mpweya wa Mulungu umawunditsa madzi

ndipo madzi a mʼnyanja amawuma kuti gwaa.

11Iye amadzaza mitambo ndi madzi a mvula,

amabalalitsa zingʼaningʼani zake kuchokera mʼmitambomo.

12Mulungu amayendetsa mitamboyo

mozungulirazungulira dziko lonse lapansi

kuti ichite zonse zimene Iye akufuna pa dziko lapansi.

13Iye amagwetsa mvula kuti alange anthu,

kapena kubweretsa chinyontho pa dziko lapansi kuti aonetse chikondi chake.

14“Abambo Yobu, tamvani izi;

imani ndipo muganizire ntchito zodabwitsa za Mulungu.

15Kodi mukudziwa momwe Mulungu amayendetsera mitambo

ndi kuchititsa kuti kukhale zingʼaningʼani?

16Kodi mukudziwa momwe Mulungu amayalira mitambo,

ntchito zodabwitsa za Iye amene ndi wanzeru zangwiro?

17Inu amene mʼzovala zanu mumatuluka thukuta

pamene kunja kwatentha chifukwa cha mphepo yakummwera,

18kodi mungathe kuthandizana naye kutambasula thambo

limene ndi lolimba ngati chitsulo?

19“Tiwuzeni ife zoti tikanene kwa Iye;

sitingathe kufotokoza mlandu wathu chifukwa cha mdima umene uli mwa ife.

20Kodi nʼkofunika kumudziwitsa Mulungu kuti ndili naye mawu?

Kodi kutero sikuchita ngati kupempha kuti ndiwonongeke?

21Tsopano munthu sangathe kuyangʼana dzuwa,

ndi kunyezimira mlengalenga,

kuwomba kwa mphepo kutachotsa mitambo yonse.

22Kuwala kwake kumaonekera cha kumpoto;

Mulungu amabwera ndi ulemerero woopsa.

23Wamphamvuzonse sitingathe kumufikira pafupi ndi wa mphamvu zoposa;

pa chiweruzo chake cholungama ndi mʼchilungamo chake chachikulu Iye sapondereza anthu ozunzika.

24Nʼchifukwa chake anthu amamuopa kwambiri,

kodi saganizira za onse amene amaganiza kuti ndi anzeru?”