Yobu 35 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 35:1-16

1Ndipo Elihu anawonjeza kunena kuti,

2“Kodi mukuganiza kuti mukukhoza?

Mukunena kuti, ‘Ndine wolungama pamaso pa Mulungu.’

3Komanso inu mukufunsa kuti, ‘Kodi phindu langa nʼchiyani,

ndipo ndimapeza chiyani ndikapanda kuchimwa?’

4“Ine ndikufuna ndikuyankheni inu

pamodzi ndi abwenzi anu omwe.

5Yangʼanani kumwamba ndipo muone

mitambo imene ili kutali ndi inuyo.

6Inuyo mukachimwa, Iye zimamukhudza motani?

Ngati machimo anu ndi ochuluka, zimenezo zimachita chiyani kwa Iye?

7Ngati inu ndinu wolungama, mumamupatsa Iyeyo chiyani?

Kapena Iye amalandira chiyani chochokera mʼdzanja lanu?

8Kuyipa kwanu kumangokhudza anthu ngati inuyo,

ndipo chilungamo chanu chimakhudza anthu anzanu.

9“Anthu akufuwula chifukwa cha kuzunzidwa;

akufuna chithandizo kuti achoke pansi pa ulamuliro wa anthu amphamvu.

10Koma palibe amene akunena kuti, ‘Kodi ali kuti Mulungu, Mlengi wanga,

amene amatisangalatsa nthawi ya usiku,

11amene amatiphunzitsa kupambana nyama za dziko lapansi

ndipo amatipatsa nzeru kupambana mbalame zowuluka?’

12Iye sayankha pamene anthu akufuwulira kwa Iye

chifukwa cha kudzikuza kwa anthu oyipa.

13Ndithu, Mulungu samva kupempha kwawo kopanda pake;

Wamphamvuzonse sasamalira zimenezi.

14Ndipo ndi bodza lalikulu kunena kuti

Iye saona zimene zikuchitika.

Iye adzaweruza molungama ngati

inu mutamudikira

15ndiye tsono popeza kuti ukali wake sukupereka chilango,

zoyipa zambiri zimene anthu amachita,

16abambo Yobu mumangoyankhula zopandapake,

mukungochulukitsa mawu opanda nzeru.”