Yobu 34 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 34:1-37

1Pamenepo Elihu anapitiriza kuyankhula kuti,

2“Imvani mawu anga, inu anthu anzeru;

tcherani khutu inu anthu ophunzira.

3Pakuti khutu limayesa mawu

monga momwe mʼkamwa mumalawira chakudya.

4Tsono tiyeni tizindikire chomwe chili choyenera;

tiphunzire pamodzi chomwe chili chabwino.

5“Yobu akunena kuti, ‘Ndine wosalakwa,

koma Mulungu akukana kundiweruza molungama.

6Ngakhale ndine wolungama mtima,

akundiyesa wabodza;

ngakhale ndine wosachimwa,

mivi yake ikundichititsa mabala osachiritsidwa.’

7Kodi munthu wofanana ndi Yobu ndani,

amene amayankhula zamwano ngati akumwa madzi?

8Iye amayenda ndi anthu ochita zoyipa;

amayanjana ndi anthu oyipa mtima.

9Paja iye amanena kuti, ‘Munthu sapindula kanthu

poyesetsa kukondweretsa Mulungu.’

10“Tsono mverani ine, inu anthu anzeru zomvetsa zinthu.

Mulungu sangachite choyipa ndi pangʼono pomwe,

Wamphamvuzonse sangathe kuchita cholakwa.

11Iye amamubwezera munthu molingana ndi ntchito zake;

Mulungu amabweretsa pa munthu molingana ndi zomwe amachita.

12Nʼchosayembekezeka kuti Mulungu achite cholakwa,

kuti Wamphamvuzonse apotoze chilungamo.

13Kodi anapatsa Mulungu udindo wolamulira dziko lapansi ndani?

Ndani anayika Mulungu kuti azilamulira dziko lonse?

14Mulungu akanakhala ndi maganizo

oti achotse mzimu wake ndi mpweya wake,

15zamoyo zonse zikanawonongekeratu

ndipo munthu akanabwerera ku fumbi.

16“Ngati ndinu omvetsa zinthu, imvani izi;

mvetserani zimene ndikunena.

17Kodi Mulungu wodana ndi chilungamo angathe kukhala wolamulira?

Kodi iwe ungathe kuweruza Wolungama ndi Wamphamvuyo?

18Kodi si Iye amene amanena kwa mafumu kuti, ‘Ndinu opanda pake,’

ndipo amawuza anthu otchuka, ‘Ndinu oyipa,’

19Iye sakondera akalonga

ndipo salemekeza anthu olemera kupambana osauka,

pakuti onsewa ndi ntchito ya manja ake?

20Iwo amafa mwadzidzidzi, pakati pa usiku;

anthu amachita mantha ndipo amamwalira;

munthu wamphamvu amachotsedwa popanda dzanja la munthu.

21“Maso a Mulungu amapenya njira za munthu;

amaona mayendedwe ake onse.

22Palibe malo obisika kapena a mdima wandiweyani

kumene anthu ochita zoyipa angabisaleko.

23Mulungu sasowa kuti apitirizebe kufufuza munthu,

kuti abwere pamaso pake kudzaweruzidwa.

24Popanda kufufuza, Iye amawononga anthu amphamvu

ndipo mʼmalo mwawo amayikamo ena.

25Pakuti Iyeyo amadziwa bwino ntchito zawo

amawagubuduza usiku ndipo amatswanyika.

26Iye amawalanga chifukwa cha kuyipa kwawo,

pamalo pamene aliyense akuwaona;

27Chifukwa anasiya kumutsata

ndipo sasamaliranso njira zake zonse.

28Anachititsa amphawi kuti kulira kwawo kufike pamaso pake,

kotero Iyeyo anamva kulira kwa amphawiwo.

29Koma ngati Mulungu akhala chete, ndani angamunene kuti walakwa?

Akabisa nkhope yake, ndani angathe kumupenyabe?

Komatu ndiye amene amayangʼana za munthu komanso mtundu wa anthu,

30kuti asalamuliridwe ndi anthu osapembedza,

kuti asatchere anthu misampha.

31“Mwina munthu atanena kwa Mulungu kuti,

‘Ndine wolakwa koma sindidzachimwanso,

32ndiphunzitseni zimene sindikuziona

ngati ndachita choyipa, sindidzachitanso.’

33Kodi Mulungu akuweruzeni potsata mmene inuyo mukuganizira,

pamene inu mukukana kulapa?

Chisankho nʼchanu, osati changa;

tsono ndiwuzeni zomwe mukudziwa.

34“Anthu omvetsa zinthu adzakambirana,

anthu anzeru amene akundimva adzandiwuza kuti,

35‘Yobu akuyankhula mopanda nzeru;

mawu ake ndi opanda fundo.’

36Aa, kunali bwino Yobu akanayesedwa mpaka kumapeto

chifukwa choyankha ngati munthu woyipa!

37Pa tchimo lake amawonjezerapo kuwukira;

amawomba mʼmanja mwake monyoza pakati pathu,

ndipo amachulukitsa mawu otsutsana ndi Mulungu.”