Yobu 32 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 32:1-22

Mawu a Elihu

1Tsono anthu atatuwa analeka kumuyankha Yobu, chifukwa chakuti iyeyo ankadziona kuti ndi wolungama. 2Koma Elihu, mwana wa Barakeli, wa fuko la Buzi, wa banja la Ramu, anapsera mtima kwambiri Yobu chifukwa choti Yobuyo anakana kuvomera kuti anachimwa ndi kuti Mulungu anakhoza pomulanga. 3Anapseranso mtima abwenzi ake atatu aja chifukwa sanapeze njira yomutsutsira Yobu, ngakhale iwo anamupeza kuti anali wolakwa. 4Tsono Elihu anadikira kuti ayankhule ndi Yobu chifukwa choti abwenziwo anali akuluakulu kupambana iyeyo. 5Koma Elihu ataona kuti anthu atatuwo analibe mawu oti ayankhulenso, iye anapsa mtima.

6Choncho Elihu mwana wa Barakeli wa fuko la Buzi anati:

“Ine ndine wamngʼono,

inuyo ndinu akuluakulu,

nʼchifukwa chake ndimaopa,

ndimachita mantha kuti ndikuwuzeni zimene ndimadziwa.

7Ndimaganiza kuti, ‘Ayambe ndi akuluakulu kuyankhula;

anthu amvulazakale ndiwo amaphunzitsa nzeru.’

8Koma mzimu wa Mulungu mwa munthu,

mpweya wa Wamphamvuzonse, ndi umene umapereka nzeru zomvetsa zinthu.

9Si okalamba amene ali ndi nzeru,

si amvulazakale okha amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu zimene zili zoyenera.

10“Nʼchifukwa chake ndikuti, ‘Mvereni;

inenso ndikukuwuzani zimene ndikuzidziwa.’

11Ndadikira nthawi yonseyi,

ndimamvetsera mwachidwi zimene mumayankhula,

pamene mumafunafuna mawu oti muyankhule,

12ineyo ndinakumvetseranidi.

Koma palibe ndi mmodzi yemwe wa inu amene anatsutsa Yobu;

palibe aliyense wa inu amene anamuyankha mawu ake.

13Musanene kuti, ‘Ife tapeza nzeru;

Mulungu ndiye amutsutse, osati munthu.’

14Koma Yobu sanayankhule motsutsana ndi ine,

ndipo ine sindimuyankha monga mmene inu mwamuyankhira.

15“Iwo asokonezeka ndipo alibe choti ayankhulenso;

mawu awathera.

16Kodi ine ndidikire chifukwa iwo sakuyankhula tsopano,

pakuti angoyima phee wopanda yankho?

17Inenso ndiyankhulapo tsopano;

nanenso ndinena zimene ndikudziwa.

18Pakuti ndili nawo mawu ambiri,

ndipo mtima wanga ukundikakamiza;

19mʼkati mwanga ndili ngati botolo lodzaza ndi vinyo,

ngati matumba a vinyo watsopano amene ali pafupi kuphulika.

20Ndiyenera kuyankhula kuti mtima utsike;

ndiyenera kutsekula pakamwa panga ndi kuyankha.

21Sindidzakondera munthu wina aliyense,

kapena kuyankhula zoshashalika,

22pakuti ndikanakhala wa luso loyankhula moshashalika,

Mlengi wanga akanandilanga msanga.”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

约伯记 32:1-22

以利户的回答

1三人见约伯自以为义,便不再回答他。 2那时,族的布西巴拉迦的儿子以利户约伯很恼火,因为约伯自以为义,不承认上帝的公义。 3他对约伯的三个朋友也很恼火,因为他们说约伯有罪,却无法回答约伯的质问32:3 因为他们说约伯有罪,却无法回答约伯的质问”有古卷作“因为他们无法回答约伯的质问,因而置上帝于不公”。4由于不及他们年长,以利户便等他们说完才向约伯发言。 5他见三人无法回答约伯,很恼火, 6就说:

“我年纪轻,你们是长辈,

所以我畏惧,不敢陈明观点。

7我想,前辈当先发言,

长者当传授智慧。

8但只有人里面的灵——

全能者的气息赐人悟性。

9长者不一定有智慧,

年老不一定明白是非。

10因此,请听我说,

我也要陈明观点。

11看啊,我一直等候你们发言,

倾听你们的理论,

等你们斟词酌句。

12我仔细聆听,

发现你们无人能驳倒约伯

无人能答复他。

13你们不要说,‘我们找到了智慧,

使他折服的是上帝而非人。’

14约伯没有与我辩论,

我也不会用你们的理论答复他。

15“他们惊慌失措,无言以对,

再也说不出话来。

16难道他们不说话,站在那里无言以对,

我就要等下去吗?

17我也要作出答复,

陈明我的观点。

18因为我心里积满了话,

我里面的灵催促我说出来。

19我里面像盛满了酒,却没有出口,

又如将要破裂的新酒袋。

20我要一吐为快,

我要开口答复。

21我不看人的情面,

也不奉承人。

22我不善奉承,

否则,造物主会很快把我除掉。