Yobu 31 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 31:1-40

1“Ndinachita pangano ndi maso anga

kuti sindidzapenya namwali momusirira.

2Kodi Mulungu kumwambako wandisungira zotani?

Kodi cholowa changa chochokera kwa Wamphamvuzonse kumwambako nʼchotani?

3Kodi si chiwonongeko kwa anthu oyipa,

tsoka kwa iwo amene amachita zolakwa?

4Kodi Mulungu saona zochita zanga,

ndi kudziwa mayendedwe anga?

5“Ngati ndachita zinthu mwachiphamaso,

kapena kufulumira kukachita zachinyengo,

6Mulungu andiyeze ndi muyeso wake wolungama

ndipo Iye adzadziwa kuti ine ndine wosalakwa,

7ngati mayendedwe anga asempha njira,

ngati mtima wanga wakhumbira zimene maso anga aona,

kapena ngati ndachita choyipa chilichonse.

8Pamenepo ena adye zimene ndinadzala,

ndipo zomera zanga zizulidwe.

9“Ngati mtima wanga unakopekapo ndi mkazi,

ndipo ngati ndinalakalaka mkazi wa mnansi wanga,

10pamenepo mkazi wanga aphikire mwamuna wina chakudya,

ndipo amuna ena azigona naye.

11Pakuti zimenezo zikanakhala zochititsa manyazi,

tchimo loyenera kulangidwa nalo.

12Ndi moto umene umayaka mpaka chiwonongeko;

ukanapsereza zokolola zanga.

13“Ngati ndinkapondereza mlandu wa akapolo anga aamuna kapena aakazi,

pamene ankabwera kwa ine ndi milandu yawo,

14ndidzatani pamene Mulungu adzanditsutsa?

Nanga ndidzayankha chiyani akadzandifunsa?

15Kodi amene anapanga ine mʼmimba mwa amayi anga si yemwe anapanganso iwo?

Kodi si mmodzi yemweyo amene anatipanga tonsefe mʼmimba mwa amayi athu?

16“Ngati ndinawamana aumphawi zinthu zimene ankazikhumba,

kapena kuwagwiritsa fuwa lamoto akazi amasiye amene amafuna thandizo kwa ine,

17ngati chakudya changa ndinadya ndekha,

wosagawirako mwana wamasiye,

18chonsechotu kuyambira unyamata wanga ndinamulera monga abambo ake,

ndipo moyo wanga wonse ndakhala ndikusamalira akazi amasiye,

19ngati ndinaona wina aliyense akuzunzika ndi usiwa,

kapena munthu wosauka alibe chofunda,

20ndipo ngati iyeyo sananditamandepo

chifukwa chomufunditsa ndi nsalu ya ubweya wankhosa,

21ngati ndinaopsezapo mwana wamasiye,

poganiza kuti ndinali ndi mphamvu mʼbwalo la milandu,

22pamenepo phewa langa lipokonyeke,

mkono wanga ukonyoke polumikizira pake.

23Popeza ine ndinaopa kwambiri chiwonongeko chochokera kwa Mulungu,

ndinachitanso mantha ndi ulemerero wake, sindikanatha kuchita zinthu zimenezi.

24“Ngati ndinayika mtima wanga pa chuma

kapena kunena kwa golide wabwino kwambiri kuti, ‘Iwe ndiye chitetezo changa,’

25ngati ndinakondwera chifukwa choti chuma changa chinali chambiri,

zinthu zimene manja anga anazipeza,

26ngati pamene ndinaona dzuwa likuwala,

kapena mwezi ukuyenda mwa ulemerero wake,

27ndipo kuti mtima wanga unakopeka nazo

nʼkuyika dzanja langa pakamwa mozilemekeza,

28pamenepo zimenezinso zikanakhala machimo oti ndilangidwe nawo,

chifukwa ndikanakhala wosakhulupirika kwa Mulungu wakumwamba.

29“Ngati ndinasangalala ndi kuwonongeka kwa mdani wanga,

kapena kusekera mavuto pamene mavuto anamugwera,

30ine sindinachimwe ndi pakamwa panga

potulutsa matemberero a mdani wanga kuti awonongeke,

31ngati anthu amene ndimakhala nawo mʼnyumba mwanga sananenepo kuti,

‘Kodi ndani amene sakhuta ndi chakudya cha Yobu?’

32Komatu mlendo sindinamusiye pa msewu usiku wonse,

pakuti khomo langa linali lotsekuka nthawi zonse kwa alendo,

33ngati ndinabisa tchimo langa monga amachitira anthu ena,

kubisa kulakwa mu mtima mwanga

34chifukwa choopa gulu la anthu,

ndi kuchita mantha ndi mnyozo wa mafuko

kotero ndinakhala chete ndipo sindinatuluke panja.

35“Aa, pakanakhala wina wondimva!

Tsopano ndikutsiriza mawu anga odzitetezera. Wamphamvuzonse andiyankhe;

mdani wanga achite kulemba pa kalata mawu ake ondineneza.

36Ndithu ine ndikanakoleka kalatayo pa phewa langa,

ndikanayivala kumutu ngati chipewa chaufumu.

37Ndikanamufotokozera zonse zimene ndinachita;

ndikanafika pamaso pake ngati kalonga.

38“Ngati minda yanga ikulira monditsutsa ine

ndipo malo ake onse osalimidwa anyowa ndi misozi,

39ngati ndinadya za mʼminda mwake osapereka ndalama

kapena kukhumudwitsa anthu olima mʼmindamo,

40pamenepo mʼmindamo mumere namsongole mʼmalo mwa tirigu

ndi udzu mʼmalo mwa barele.”

Mawu a Yobu athera pano.