Yobu 30 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 30:1-31

1“Koma tsopano akundinyoza,

ana angʼonoangʼono kwa ine,

anthu amene makolo awo sindikanawalola

kuti azithandizana ndi agalu anga kuweta nkhosa zanga.

2Kodi mphamvu zawo ndi za phindu lanji kwa ine,

pakuti mphamvu zawo zinatha kale?

3Anali atatheratu kuwonda ndi njala,

ankayendayenda mʼdziko lopanda madzi,

mʼchipululu usiku.

4Ankathyola therere ndi masamba owawa,

ndipo chakudya chawo chinali mizu ya mitengo ya masache.

5Anapirikitsidwa pakati pa anthu anzawo,

akuwakuwiza ngati kuti anali akuba.

6Anawumirizidwa kukhala ku zigwembe za mitsinje yowuma,

pakati pa matanthwe ndi mʼmaenje a mʼnthaka.

7Ankalira ngati nyama kuthengo

ndipo ankawunjikana pamodzi pa ziyangoyango.

8Anali anthu achabechabe ndi wopanda dzina,

anathamangitsidwa mʼdziko.

9“Ndipo tsopano ana awo akundiyimba nyimbo zachipongwe;

ineyo ndasanduka chisudzo chawo.

10Iwo amanyansidwa nane ndipo amandithawa;

akandiona salephera kundilavulira mʼmaso mwangamu.

11Tsopano pakuti Mulungu wakhwefula uta wanga ndipo wandisautsa,

iwowo analekeratu kundiopa.

12Ku dzanja langa lamanja anthu akulimbana nane;

andikumbira dzenje loti ndigweremo ndikamayenda,

andipangira mitumbira ya nkhondo kuti alimbane nane.

13Iwo anditsekera njira;

akufuna kundichititsa ngozi,

popanda wina aliyense wowaletsa.

14Akundithamangitsa ngati madzi olowera pa mpanda wobowoka,

iwo akubwererabwerera pakati pa chipasupasu.

15Zoopsa zandithetsa mphamvu;

ulemu wanga wachita ngati wauluzika ndi mphepo,

chuma changa chija chazimirira ngati mtambo.

16“Ndipo tsopano mtima wanga wachokamo;

ndili mʼmasiku amasautso.

17Mafupa anga akuphwanya usiku pakuti

zowawa zanga sizikuleka.

18Mʼmphamvu zake Mulungu wakhala ngati chovala changa;

Iye wandigwira ngati chovala chondithina pa khosi.

19Wandiponya mʼmatope,

ndipo ndasanduka ngati fumbi ndi phulusa.

20“Inu Mulungu, ine ndikulirira kwa Inu, koma simukundiyankha;

ndikayimirira, Inu simundiyangʼana nʼkomwe.

21Inuyo mumandichitira zankhanza;

mumandizunza ndi dzanja lanu lamphamvu.

22Mwandinyamulira ku mphepo ndipo mwandiwulutsa ndi mphepoyo;

mwandiponya mʼmphepo ya mkuntho.

23Ndikudziwa kuti Inu mudzandifikitsa ku imfa,

kumalo kumene amoyo onse adzapitako.

24“Ndithudi palibe munthu amene amalanga munthu wosweka mtima,

amene akupempha thandizo mʼmasautso ake.

25Kodi ine sindinalire nawo iwo amene anali pamavuto?

Kodi mtima wanga sunamvere chisoni anthu osauka?

26Koma pamene ndinkayembekezera zabwino, zoyipa ndiye zinandigwera;

pamene ndinkafunafuna kuwala, mdima ndiye unandigwera.

27Kuwawa kwa mʼkati mwanga sikukuleka;

ndili mʼmasiku amasautso.

28Ndikuyenda wothimbirira, komatu osati ndi dzuwa;

ndimayimirira pa msonkhano ndi kupempha chithandizo molira.

29Ndasanduka mʼbale wa nkhandwe,

mnzawo wa akadzidzi.

30Khungu langa layamba kuda ndipo likufunduka;

thupi langa likutentha chifukwa cha kuphwanya kwa thupi.

31Pangwe wanga wasanduka woyimbira maliro,

ndipo chitoliro changa chikuyimbira anthu olira.