Yobu 26 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 26:1-14

Mawu a Yobu

1Pamenepo Yobu anayankha kuti,

2“Wamuthandizadi munthu wopanda mphamvu!

Walimbitsadi dzanja la munthu wofowoka!

3Wapereka malangizo kwa munthu amene alibe nzeru!

Ndipotu waonetsadi nzeru zochuluka!

4Kodi wakuthandiza ndani kuti uyankhule mawu awa?

Ndipo ndi mzimu wa yani umene unayankhula pakamwa pako?

5“Mizimu ya anthu akufa ikunjenjemera pansi pa madzi,

ndi zonse zokhala mʼmadzimo.

6Dziko la anthu akufa ndi lapululu pamaso pa Mulungu;

chiwonongeko ndi chosaphimbidwa.

7Mulungu anayala thambo la kumpoto pa phompho;

Iye anakoloweka dziko lapansi mʼmalo mwake pamene panali popanda nʼkanthu komwe.

8Amasunga madzi ambiri mʼmitambo yake,

koma mitamboyo siphulika chifukwa cha kulemera kwa madziwo.

9Iye amaphimba mwezi wowala,

amawuphimba ndi mitambo yake.

10Mulungu anawalembera madzi malire wonga uta,

kukhala malire pakati pa kuwunika ndi mdima.

11Mizati yochirikiza mitambo yakumwamba imanjenjemera,

ndi kudabwa pa kudzudzula kwake.

12Ndi mphamvu zake anatontholetsa nyanja;

ndi nzeru zake anakantha chirombo cha mʼmadzi chija chotchedwa Rahabe.

13Ndi mpweya wake anayeretsa zamumlengalenga,

dzanja lake linapha chinjoka chothawa chija.

14Zimenezi ndi pangʼono chabe mwa ntchito yake;

tingomva pangʼono za Iye ngati kunongʼona!

Kodi ndani angathe kudziwa kukula kwa mphamvu zake?”