Yobu 23 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yobu 23:1-17

Yobu

1Pamenepo Yobu anayankha kuti,

2“Leronso kudandaula kwanga nʼkwakukulu kwambiri;

Iye akundilanga kwambiri ngakhale ndi kubuwula.

3Ndikanangodziwa kumene ndikanamupeza Mulungu;

ndikanangopita kumene amakhalako!

4Ndikanafotokoza mlandu wanga pamaso pake

ndipo ndikanayankhula mawu odziteteza.

5Ndikanadziwa mawu amene Iye akanandiyankha,

ndi kulingalira bwino zimene akananena!

6Kodi Iye akanalimbana nane mwa mphamvu zake zazikulu?

Ayi, Iye sakanayankhula zinthu zotsutsana nane.

7Kumeneko munthu wolungama akanafotokoza mlandu wake pamaso pake,

ndipo woweruzayo akanandipeza wosalakwa nthawi zonse.

8“Taonani, ndikapita kummawa, Iye kulibe kumeneko,

ndikapita kumadzulo sinditha kumupeza kumeneko.

9Akamagwira ntchito kumpoto, sindimuona kumeneko

akapita kummwera, sindimuona.

10Koma Iye amadziwa mmene ndimayendera;

Iyeyo akandiyesa adzandipeza kuti ndili ngati golide.

11Mapazi anga akhala akuponda mʼmapazi ake;

ndasunga njira yake ndipo sindinayitaye.

12Sindinapatuke kusiya malamulo ochokera pakamwa pake;

ndasunga mawu a pakamwa pake kupambana chakudya changa cha tsiku ndi tsiku.

13“Koma Iyeyo ndi wosasinthika, ndipo ndani angatsutsane naye?

Iye amachita chilichonse chimene wafuna.

14Iye amachita chimene watsimikiza kuti chindichitikire,

ndipo malingaliro oterowa ali nawobe.

15Nʼchifukwa chake ndikuchita mantha kwambiri pamaso pake;

ndikamaganiza zonsezi ndimamuopa.

16Mulungu walefula mtima wanga;

Wamphamvuzonse wandiopseza kwambiri.

17Komatu sindinachititsidwe mantha ndi mdima,

ndi mdima wandiweyani umene waphimba nkhope yanga.